Books
Books
Njira zothandiza za moyo wachimwemwe
Buku lofotokoza za njira zothandizira kukhala umoyo wa chimwemwe lolembedwa ndi Sheikh Abdul-Rahman bin Nasir as-Sa'die, limafotokoza mozama njira zobweresera chisangalalo chenicheni kuchokera pa mawonedwe a chikhulupiliro chozama; ndipo limatsogolera owerenga ku bata la mtima kudzera mu chikhulupiliro ndi ntchito zabwino, kukumbukira Mulungu, kukhutira, kusinkhasinkha za madalitso, kuchita ubwino, kuyezamira mwa Mulungu, kuleza mtima, ndi kuzindikira moyenera kufunika kwa zinthu. Mu kalembedwe kokongola, limayika pamaso panu kalozera wa moyo wamtendere, wolinganizika, komanso wosangalala…
الإسلام دين رب العالمين
M'dzina la Allah wa chifundo chambiri wa chisoni chosatha CHISILAMU NDI CHIPEMBEDZO CHA MBUYE WA ZOLENGEDWA ZONSE Kodi mbuye wako ndi ndani? Ili ndi funso lalikulu pa dziko la pansi lino; ndipo ndi funso lofunika kuti munthu alidziwe yankho lake. Mbuye wathu ndi Mulungu amene adalenga mitambo ndi nthaka,ndikumasisa madzi a mvula kuchokera ku mwamba,ndipo kuchokera mu madzi amenewo amameretsa ndikumatulutsa zipatso,kumeretsa mitengo yomwe imatulutsa zakudya zathu ndi nyama,yama zake zimene ifenso timadya. Iye ndi Mulungu amene adalenga ife komanso makolo athu,komanso adalenga kena kalikonse.…
CHIDULE CHOFOTOKOZA ZA KACHITIDWE KA MAPEMPHERO A UMRAH
Kuyamikidwa konse ndi kwa Mulungu, Mbuye wa zolengedwa zonse, ndipo madalitso ndi mtendere zikhale pa Mtumiki wathu Muhammad, ndi aku banja kwake pamodzi ndi omutsatira ake onse. Pambuyo pa mau amenewa: Uwu ndi uthenga wachidule ofotokoza za kachitidwe ka mapemphero a Umrah,tinaikira mtima pofotokoza zomwe zimafunika kwa munthu ochita Umrah. Tikupempha Mulungu kuti auchite uthenga umenewu kukhala osangalasa iye yekha, ndikuti auchite kukhala othandiza kwa Asilamu onse.
من خلقني؟ ولماذا؟
Ndani adandilenga? Nanga chifukwa chiyani? Cholengedwa Chili chonse chimasonyeza kupezeka kwa Mlengi. Ndani adalenga kumwamba ndi dziko la pansi ndi zolengedwa zikuluzikulu zomwe zili mkati mwa ziwirizi zomwe sizimadziwika? Kodi ndi ndani adaika ndondomeko yokuya ndi yolongosoka bwino yakayendedwe ka zinthu kumwamba ndi dziko lapansi? Kodi ndani amene adalenga munthu ndikumupatsa makutu, maso, ndi nzeru? ndikumpatsa kuthekera kophunzira ndikudziwa zoona? Kodi mungafotokoze bwanji ndondomeko yodzama ndi yokuya ya momwe Mulungu adaikira ziwalo zapa thupi lako komanso ziwalo za zinthu za moyo?…
الشهادتين
Ngati ukufuna kulowa mu chipembedzo cha Chisilamu,ukuyenera kuyankhula mau oikira umboni awa momveka bwino,komanso umvetsetse matanthauzo ake ndikuwakhulupilira matanthauzowo: Ndikuikira umboni zoti palibe Mulungu oyenera kupembedzedwa mwa choonadi koma Mulungu m'modzi yekha(mau amenewa amatanthauza kuti palibe wina aliyense amene akuyenera kupembedzedwa koma Mulungu m'modzi yekha). Ndikuikiranso umboni kuti Muhammad ndi Mtumiki wa Mulungu, ndikutinso Yesu (Issah) mwana wa Mariya ndi kapolo wa Mulungu komanso Mtumiki wake. Ndikuikira umboni kuti palibe Mulungu oyenera kupembedzedwa mwa…
CHIDULE CHOFOTOKOZA ZA KACHITIDWE KA MAPEMPHERO A HAJJ
Kuyamikidwa konse ndi kwa Mulungu, Mbuye wa zolengedwa zonse, ndipo madalitso ndi mtendere zikhale pa Mtumiki wathu Muhammad, ndi aku banja kwake pamodzi ndi omutsatira ake onse. Pambuyo pa mau amenewa: Uwu ndi uthenga wachidule ofotokoza za kachitidwe ka mapemphero a Hajj,tinaikira mtima pofotokoza zomwe zimafunika kwa munthu ochita Hajj. Tikupempha Mulungu kuti auchite uthenga umenewu kukhala osangalasa iye yekha, ndikuti auchite kukhala othandiza kwa Asilamu onse. Chiyambi:
Zina mwa zizindikiro za umodzi wa Mulungu(Tauhid).
M’dzina la Mulungu, Wachifundo Chambiri, Wachisoni. Kuyamikidwa konse ndi kwa Mulungu, Mbuye wa zolengedwa zonse, ndipo mathero abwino akakhala kwa anthu owopa Mulungu, ndipo ine ndikuikira umboni kuti palibe Mulungu opembedzedwa mwachoonadi koma Mulungu m'modzi yekha, opanda othandizana naye,ndipo ndikuikiranso umboni kuti Muhammad ndi kapolo ndi Mtumiki wake,mtendere ndi madalitso a Mulungu zikhale pa iye, aku banja kwake ndi ophunzira ake onse, pambuyo pa mau amenewa: Kukhulupilira za umodzi wa Mulungu ndi chiyambi ndi mathero a chipembedzo, ntchito zobisika ndi zoonekera zonse zagona…
وجوب العمل بالسنة وكفر من أنكرها
CHIKAKAMIZO CHOGWIRITSA NTCHITO SUNNA ZA MTUMIKI(SAW)NDIKUKANIRA KWA MUNTHU YEMWE ANGAZIKANE SUNNAZO. WOLEMBA BUKU: ABDUL AZIZ BIN ABDUL ALLAH BIN BAZ(ALLAH AWACHITIRE CHISONI). M'dzina la Mulungu ,Wachifundo Chambiri ,Wachisoni Chosatha. MAU OYAMBA Kuyamikidwa konse ndikwa Mulungu, mbuye wa zolengedwa zonse, ndipo mathero abwino pa chinthu chilichonse amakhala kwa anthu oopa Mulungu, mtendere ndi madalitso a Mulungu zikhale pa kapolo komanso mtumiki wake,mneneri wathu Muhammad; amene anatumizidwa kuti akhale ozichitira chisoni zolengedwa zonse,komanso mtendere ukhale kwa anthu aku banja…