Kukamba zokhuza chikhulupiliro cha chisilamu mwa chidule
Bukuli likulongosola mapata a Chikhulupiliro omwe akukhuza Kukhulupilira mwa Allah, Angelo Ake, Mabuku Ake, Atumiki Ake, Tsiku Lomaliza, ndi Chikonzero Chake. Ndipo bukuli likuonetsa mfundo zoyambirira zomwe Msilamu ayenera kuzikhulupilira ndi kudzigwiritsa ntchito, potsindika kufunika kolimbikitsa ubale ndi Allah kudzera mukumvetsetsa mozama Chikhulupiliro cha chisilamu.
This PDF is generated automatically from the book's text; its layout may differ from the printed edition.
Kukamba zokhuza chikhulupiliro cha chisilamu mwa chidule
Buku lalembedwa ndi Sheikh wolemekezeka komanso wozindikira kwambiri
Muhammad bin Swalih Al-Uthaymeen
Allah awakhululukire iwowo, makolo awo komanso Asilamu onse
M’dzina la Allah, wachifundo chambiri, wachisoni.
MAU OYAMBA
Ndithudi, kutamandidwa konse ndi kwa Allah, tikumutamanda, tikumupempha chithandizo, tikumupempha chikhululuko, komanso tikulapa kwa Iye, Ndipo tikudzitchinjiriza mwa Allah ku zoipa za m’mitima mwathu, ndi ku ntchito zathu zonyansa, Amene Allah wamuongola, palibe angamusocheretse, ndipo amene wamulekelera kusochera palibe angamuongole, Ndipo ndikuikira umboni kuti palibe mulungu woyenera kupembedzedwa mwa choonadi koma Allah M'modzi yekha, alibe wothandizana naye, Ndipo ndikuikiranso umboni kuti Muhammad ndi kapolo komanso mtumiki Wake - chifundo cha Allah ndi m'tendere wake zikhale pa iye, akubanja kwake, ophunzira ake, ndi onse amene akutsatira chiphunzitso chake moyenera.
Pambuyo pake: ndithudi kuzindikira za umodzi wa Allah ndiphunziro lolemekezeka kwambiri, laulemu waukulu, ndiponso lofunika kwambiri kuphunziridwa; chifukwa ndiko kuzindikira za Allah wapamwamba, ndi maina ake, mbiri zake ndi zoyenera kuchitiridwa ndi akapolo ake, ndiponso chifukwa ndi makiyi otsegulira njira yonkera kwa Allah wapamwamba, komanso nditsinde la malamulo ake.
Ndi chifukwa chake: Atumiki onse adagwirizana kuti aitanire anthu ku umodzi wa Allah. Allah wapamwamba adati: {Ndipo sitidatumize iwe usadabwere mtumiki wina aliyense koma kupatula kuti timamupatsa uthenga wonena kuti; palibe mulungu woyenera kupembedzedwa mwa choonadi koma Ine ndekha, choncho ndipembedzeni (Ine ndekha ndipo musamandiphatikize ndi mafano)} 25. [Al-Anbiya:25].
Ndipo Iye wapamwamba wachitira yekha umboni zoti Iye yekha ndi amene ali woyenera kupembedzedwa mwa choonadi, nawonso Angelo achitira umboni zoti Allah yekha ndi amene ali oyenera kupembedzedwa mwa choonadi, chimodzimodzinso anthu ophunzira bwino za chipembedzo akuchitiranso nao umboni, Allah wapamwamba wati: {Allah wachitira umboni zoti palibe mulungu (woyenera kumpembedza mwa choonadi) koma Iye, Angelo nao komanso anthu ophunzira bwino (za chipembedzo ayikira nao umboniu). (Iye nthawi zonse) ndiokhanzikitsa chilungamo. Palibe mulungu (woyenera kumupembedza mwa choonadi) koma Iye wamphamvu zonse,wa nzeru zakuya 18}. [Al-Imran:18].
Ndipo popeza uku ndiko kufunika kwa chikhulupiliro cha umodzi wa Allah n'chokakamizika kwa Msilamu aliyense kuti achisamalire pochiphunzira, kuchiphunzitsa, kuchilingalira mozama, komanso kuchikhulupilira; kuti amange chipembedzo chake pa maziko olimba, a mtendere wa mumtima ndi kugonjera; kuti adzasangalale ndi zipatso zake, ndiponso zotsatira zake.
Ndipo Allah ndemwini kutheketsa zinthu
Mulembi
CHIPEMBEDZO CHA CHISILAMU
Chipembedzo cha Chisilamu: ndi chipembedzo chimene Allah adatumiza nacho Muhammad- mtendere ndi madalitso a Allah zipite kwa iye- ndipo Allah adatsiriza kutumiza zipembedzo ndi Chisilamu, ndipo adachikwaniritsa kwa akapolo ake, nakwaniritsa nacho mtendere pa iwo, ndipo adakondwera nacho kukhala chipembedzo chawo, choncho, palibe chipembedzo china chimene chidzalandiridwe kuchokera kwa aliyense kupatula chimenecho, Allah adayankhula kuti: {Muhammad - mtendere ndi madalitso a Allah zikhale pa iye - sali tate wa aliyense mwa amuna anu, koma iye ndi Mtumiki wa Allah, ndiponso wotsiriza mwa Aneneri, ndipo Allah amadziwa chilichonse 40}. [Al-Ahzab: 40].
Allah adayankhulanso kuti: {Lero ndakukwaniritsirani chipembedzo chanu (chomwe ndi chisilamu), ndipo ndakwaniritsa mtendere wanga pa inu, ndipo ndakusankhirani Chisilamu kukhala chipembedzo chanu}. [Al-Maidah:3].
Allah adayankhulanso kuti: {Ndithu chipembedzo chomwe chikalandiridwe pa maso pa Allah ndi Chisilamu...} [Al-Imran:19].
Allah adayankhulanso kuti: {Kwa yemwe angasankhe chipembedzo china osati Chisilamu, sichikalandiridwa kuchokera kwa iye, ndipo iye ku umoyo ulinkuza azakhala mwa otayika 85}. [Al-Imran: 85].
Allah adalamula anthu onse kuti ampembedze Allah wapamwamba kudzera mu chipembedzochi, ndipo adayankhula pomuuza Mtumiki wa Allah - mtendere ndi madalitso a Allah zikhale pa iye - kuti: {Nena (iwe Mtumiki): E inu anthu! Ndithudi ine ndi Mtumiki wa Allah kwa inu nonse. (Allah) Amene ali Mfumu ya ku mitambo komanso pa dziko la pansi, palibe mulungu oyenera kupembedzedwa mwa choonadi koma Iye yekha, amapereka moyo ndi imfa, choncho, mukhulupilireni Allah komanso Mtumiki wake (Muhammad-mtendere ndi madalitso a Allah zikhale pa iye) - Mtumiki amene samatha kulemba ndi kuwerenga, yemwe amakhulupilira Allah ndi mau Ake, choncho mutsatireni kuti muwongoke} [Al-A'raf:158].
Ndipo mu Sahih Muslim, nkhani ikuchokera kwa Abu Huraira -chisangalalo cha Allah chikhale pa iye- adati Mtumiki wa Allah -mtendere ndi madalitso a Allah zikhale pa iye- adanena kuti: «Ndikulumbilira (Allah) amene moyo wa Muhammad uli m'manja mwake kuti palibe aliyense wa mu m'badwo uno kaya ndi Myuda kapena Mkhirisitu amene angamve za ine kenako ndi kumwalira osakhulupilira zimene ndatumidwa nazo koma kupatula kuti adzakhala mu gulu la anthu aku Moto»[1]. [1] Idatulutsidwa ndi Muslim: buku la Chikhulupiliro, mutu okamba za kukakamizidwa kokhulupilira uthenga wa mneneri wathu Muhammad -mtendere ndi madalitso a Allah zikhale pa iye- kwa anthu onse, ndi kufafaniza zipembedzo ndi chipembedzo chake, nambala yake (153).
Kumukhulupilira Mtumiki zikutanthauza: kukhulupilira zomwe adabwera nazo kuti ndi zoona povomereza ndikutsatira, osati kungokhulupilira kokha; ndi chifukwa chake Abu Talib sadali gulu la anthu okhulupilira mwa Mtumiki - mtendere ndi madalitso a Allah zikhale pa iye -ngakhale amakhulupilira zoti zomwe adabwera nazo zinali zoona komanso kuikira umbone kwake kuti Chisilamu ndi chipembedzo chomwe chili chabwino.
Chipembedzo cha Chisilamu: mukupezeka ma ubwino onse omwe amapezeka mu zipembedzo zonse zomwe zidabwera Chisilamu chisanabwere (Chiyuda ndi Chikhirisitu), ndipo Chisilamu chili pamwamba pa zipembedzo zonsezo chifukwa choti malamulo ake amagwirizana ndi nyengo, malo komanso mibado yonse, Allah akuyankhula kumuuza Mtumiki wake kuti: {Ndipo takuvumbulutsira buku mwa choonadi, lomwe likuikira umboni mabuku omwe adalipo patsogolo pake, ndi kuwateteza...} [Al-Maidah:48].
Ndipo tanthauzo loti malamulo a Chisilamu amagwirizana ndi malo, nyengo ndi m'bado ulionse wa anthu ndi loti: kugwiritsitsa malamulo ake sikumatsutsana ndi zofuna za anthu nyengo iliyonse kapena malo alionse, koma kuti anthu akhale umoyo wabwino amafunika kutsatira malamulo a Chisilamu, ndipo sizikutanthauza kuti malamulo a chipembedzo cha Chisilamu amagonjera nyengo, malo komanso m'bado wa anthu ayi, monga m'mene anthu ena amafunira.
Ndipo Chipembedzo cha Chisilamu: Ndi chipembedzo choona chimene Allah adamutsimikizira munthu amene angachigwirisitse kuti adzamuthandiza, ndi kumupambanitsa pa ena onse. Allah akuyankhula kuti: {Iye ndi Yemwe adatuma Mtumiki Wake ndi ulangizi ndiponso chipembedzo choona kuti achiwonetsere pa zipembedzo zonse, ngakhale atanyansidwa nazo Amushirikuna} [As-Saff:9].
Allah akuyankhula kuti: {Allah walonjeza anthu amene akhulupilira mwa inu ndikumagwira ntchito zabwino, kuti adzawapulumutsa kwa adani awo, ndipo adzawapanga kukhala atsogoleri pa dziko monga momwe adawapangira anthu okhulupilira amene adalipo iwo asadabwere, komanso adawalonjeza kuti achichita chipembedzo chawo chomwe Allah adasangalasidwa nacho kuti chikhale chipembedzo chawo (chomwe ndi chisilamu) kukhala chapamwamba komanso cha mphamvu, komanso (adawalonjeza) zowasinthira mantha awo ndikuwapatsa mtendere, ndipo adzakhala akundipembedza Ine ndekha, asakundiphatikiza ndi china chilichonse, tsono kwa amene angakanire pambuyo pa mtendere umenewo, amenewo ndi anthu omwe agalukira malamulo a Allah-55}. [Al-Nur: 55].
Ndipo Chipembezo cha Chisilamu: kuyambira chikhulupiliro ndi malamulo, ndichipembedzo chokwanira mu chikhulupiliro chake komanso malamulo ake:
1-Chimalamula kumpatula Allah, ndipo chimaletsa kumphatikiza Iye.
2-Chimalamula kunena zoona ndikuletsa kuyankhula za bodza.
3-Chimalamulira zochita chilungamo ndi kuletsa kupondereza, ndipo chilungamo ndiko kufananiza pakati pa zinthu zofanana, ndikusiyanitsa pakati pa zinthu zosiyana. Ndipo chilungamo sichili kufanana kwathunthu monga momwe anthu ena amanenera pamene amati: Chipembedzo cha Chisilamu ndi chipembedzo cholimbikitsa kukhala chowaona anthu mofanana, chifukwa choti kufanana pakati pa zinthu zosiyana ndi kupondereza zomwe sizimabwera kuchokera ku chisilamu, ndipo ochita zimenezo samayamikidwa.
4-Chimalamulira kukhulupirika ndi kuletsa chinyengo.
5-Chimalamulira kukwaniritsa mapangano ndipo chimaletsa chinyengo.
6- Chimalamulira zowachitira zabwino makolo awiri ndikuletsa kuwachitira zoipa.
7- Chimalamulira zolumikiza ubale ndi anthu omwe ndi achibale ndipo amaletsa kudula ubale.
8-Chimalamulira kukhala bwino ndi anthu oyandikana nawo, ndipo chimaletsa kuwachitira zoipa.
Ponena mwachidule: (Chisilamu) chimalamulira za khalidwe lililonse labwino, ndipo chimaletsa khalidwe lililonse lonyansa. Chimalamuliranso zochita ntchito zonse zabwino ndipo chimaletsa ntchito zonse zoipa.
Allah akuyankhula kuti: {Ndithudi, Allah akulamula (kuchita) chilungamo, ndikuchita zabwino, ndi kupatsa achinansi, ndipo akuletsa zauve ndi zoipa ndi kupyola malire; akukulangizani kuti muzindikire ndi kukumbukira-90}. [Al-Nahl:90].
NSANAMIRA ZA CHISILAMU
Nsanamira za Chisilamu: izi ndingodya zake zimene chisilamu chimamangidwira, ndipo zilipo zisanu: Zatchulidwa mu nkhani yomwe ikuchokera kwa Abdullah mwana wa Umar - Allah asangalasidwe nawo onse awiri-yomwe ikuchokera kwa Mneneri wa Allah - mtendere ndi madalitso a Allah zikhale pa iye- amene adanena kuti: «Chisilamu chinamangidwa ndi zinthu zisanu: zokhulupilira za umodzi wa Allah popembedzedwa–mu mayankhulidwe ena mu zinthu zisanu–: Kuikira umboni kuti palibe oyenera kupembedzedwa mwachoonadi koma Allah ndikuti Muhammad ndi kapolo wake komanso Mtumiki wake, kupemphera Swala moyenera, kupereka Zakat, kusala mwezi wa Ramadhan, ndi kukachita mapemphero a Hajj» Ndiye munthu wina adati: Hajj ndi kusala mwezi wa Ramadhan? Abdullah adati: "Ayi, kusala kudya mwezi wa Ramadhan, ndi Hajj" Umu ndimo ndidamvera kwa Mtumiki wa Allah - mtendere ndi madalitso a Allah zikhale pa iye-[2]. [2] Nkhani ikupezeka mu buku la Bukhar: buku la Chikhulupiliro, nambala yake ndi (8), komanso mu buku la Muslim: buku la Chikhulupiliro, mutu wonena za mawu a Mneneri (SAW) akuti Chisilamu chinamangidwa pa zinthu zisanu, nambala yake ndi (16).
1-Ponena za kuikira umboni kuti palibe wina oyenera kupembedzedwa mwachoonadi koma Allah ndikuti Muhammad ndi kapolo wake komanso Mtumiki wake zimatanthauza kuti: ndi chikhulupiliro chokhazikika chofotokozedwa ndi lilime kudzera mu umboniwu, tsono chifukwa cha chitsimikizo chake pa zimenezo amakhala ngati akuziona ndi maso ake. Ndipo umboni uwu udaikidwa kukhala nsanamira imodzi, ngakhale kuti zinthu zoikidwira umbonizo zilipo zingapo
Chifukwa Mtumiki - mtendere ndi madalitso a Allah zikhale pa iye - ndi ofalitsa uthenga ochokera kwa Allah, choncho, kuikira umboni za ukapolo ndi utumiki wake, ndi zomwe zimapangitsa kuti mau oikira umboni kuti palibe mulungu oyenera kupembedzedwa mwa choonadi koma Allah akhale okwanira
Kapenanso: Chifukwa mau awiri oikira umboniwa ndiwo maziko omwe amapangitsa ntchito kukhala yolondola komanso yolandiridwa; chifukwa choti palibe ntchito imakhala yolondola kapena yolandiridwa pamaso pa Allah pokha pokha ikagwiridwa pofuna kusangalatsa Allah ndikupanga potsatira Mtumiki wake - mtendere ndi madalitso a Allah zikhale pa iye.
Kuzera pogwira ntchito pofuna kusangalatsa Allah, mau oikira umboni zoti: palibe mulungu oyenera kupembedzedwa mwachoonadi koma Allah amakwaniritsidwa, komanso kuzera pomutsatira Mtumiki wa Allah, mau oikira umboni zoti Muhammad ndi kapolo ndi Mtumiki wa Allah, amakwaniritsidwa.
Zina mwa zipatso za mau oikira umboni waukuluwu ndi: kuwumasula mtima ku ukapolo opembedza zolengedwa, komanso ku ukapolo owatsatira omwe sali Atumiki.
2-Kuimika mapemphero: kumeneko ndiye kumpembeza Allah popemphera swala mu njira yoyenera komanso mokwaniritsa kena kalikonse popemphera mu nthawi zake komanso ndi kachitidwe kake koyenera.
Ndipo zina mwa zipatso zake: mtendere wa mu mtima, kudekha, kuletsa nsambi zonyasa kwambiri ndi machimo ena onse.
3-Tsono kupereka Zakat: kumeneko ndi kumupembedza Allah kudzera popereka gawo lokakamizidwa kuchokera mu chuma choyenera kuperekera Zakat.
Lina mwa phindu lopereka Zakat ndi: kuyeretsa moyo wa munthu ku khalidwe loipa (umbombo) ndi kukwaniritsa zosowa za Chisilamu ndi Asilamu.
4-Tsono kusala mwezi wa Ramadhan: kumeneko ndikumupembedza Allah posiya zonse zomasulitsa kusala usana wa Ramadhan.
Lina mwa phindu la kusala ndi: kuphunzitsa moyo kusiya zinthu zomwe zili zokondedwa pofuna kumusangalatsa Allah wamphamvu komanso wolemekezeka.
5-Tsono kupanga Hajj: kumeneko ndi kumupembedza Allah popita ku nyumba yopatulika; ukachita mapemphero a Hajj.
Lina mwa phindu la Hajj ndi: kumuphunzitsa munthu kuti azigwiritsa ntchito mphamvu ndi chuma chake potsatira malamulo a Allah wapamwamba; ndi chifukwa chake mapemphero a Hajj ali mtundu umodzi mu mitundu yomenya nkhondo panjira ya Allah.
Ma ubwino tatchulawa ochokera mu malamulo achipembedzowa, komanso omwe sitidawatchule, amalipangitsa gulu la chisilamu kukhala loyera, lotsatira malamulo a Allah eni eni, ndikumagwira ntchito ndi anthu mwa chilungamo komanso mokhulupirika; Chifukwa malamulo ena a Chisilamu amalongosoka ngati ngodya zatchulidwazi zalongosoka, ndipo makhalidwe a anthu amalongosoka ngati zinthu zokhuza chipembedzo zalongosoka, makhalidwe a anthu amaonongeka mmene kungawadutsire kulongosoka kwa zinthu za chipembedzo.
Kwa munthu amene akufuna amvetsetse bwino zimenezi, awerenge mau ake Allah oti: {Akanakhala kuti eni ake mizinda (imeneyi yomwe ife tidatumizamo Atumiki athu) adakhulupilira (zomwe adawabweretsera Atumiki awowo) ndikukhala omuopa (Allah posiya kukanira ndi machimo ndikumatsatira malamulo a Allah), tikanawatsegulira makomo a zinthu zabwino kuchokera kumwamba ndi pansi, koma iwo sadakhulupilire (komanso sadamuope Allah) ,m'malo mwake adakanira (zomwe adadza nazo Atumiki awo), ndipo zotsatira zake ife tidawapatsa chilango mwazizizi chifukwa cha machimo awo omwe adali kuchita-96 Kodi eni ake mizinda imeneyi (yokanirayi) akuganiza kuti ali pa mtendere komanso otetezedwa ku zilango zathu zomwe zithakuwapeza usiku iwe akugona?-97 Kapena eni mizinda (yokanirayi) akuganiza kuti zilango zathu zitha kuwapeza nthawi yaku m'mawa pomwe iwo akuchedza?-98 Kodi (eni mizinda yokanirayi) akuganiza kuti ali otetedzedwa ku chilango cha Allah (powapatsa mtendere ochuluka posayang'anira zoipa zawo), palibe amene akumadziyika pamtendere ku chilango cha Allah kupatula okhawo omwe ali oluza-99}. [Al-A'raf:96-99].
Munthu akuyenera kulingalira mu mbiri ya anthu omwe adalipo iye asanabwere; chifukwa choti mu mbiri ya anthu ena muli maphunziro kwa anthu a nzeru, komanso muli chiphanula maso kwa munthu amene mtima wake sunakutidwe ndi chotchinga, ndipo thandizo lililonse limachokera kwa Allah.
Ngodya za chikhulupiliro cha Chisilamu
Chipembedzo cha Chisilamu:- monga tafotokozera kale- ndi chikhulupiliro komanso malamulo, ndipo tayankhula zokhuza ena mwa malamulo ake, tachula nsanamira zake zomwe zimawerengedwa kuti ndi ngodya za malamulo ake.
Tsono Chikhulupiliro cha Chisilamu, ngodya zake ndi: kukhulupilira mwa Allah, Angelo ake, Mabuku ake, Atumiki ake, Tsiku Lomaliza, ndi Chikonzero: zabwino ndi zoipa zake.
Buku la Qur'an ndi chiphunzitso cha Mtumiki wake - mtendere ndi madalitso a Allah zikhale pa iye -zatsimikiza za ngodya zimenezi.
Allah wapamwamba akuyankhula mu buku lake kuti:: {Zabwino pa maso pa Allah sikuti ndikungolunjika mbali yaku m'mawa ndi kumadzulo (pomwe ukupemphera- ngati ukuchita zimenezo posatsatira malamulo a Allah), koma kuti zabwino zonse zili pa munthu amene wakhulupilira mwa Allah, ndikukhulupiliranso za tsiku louka kwa akufa ndi kukhulupilira Angelo, kukhulupiliranso mabuku, ndikukhulupilira Atumiki...} [Al-Baqarah:177] Kenako ponena za zikonzero zake kuti: {Ndithu ife tidachilenga china chilichonse ndi mlingo wake .49 Ndipo lamulo lathu (pa china chilichonse tikafuna kuti chichitike timangoyankhula) mau amodzi okha (oti"ukhale chakuti)" ndipo chimachitika mofulumira ngati kuphetila kwa diso 50}. [Surat Al-Qamar: 49-50].
Ndipo mu Sunnah za Mtumiki -mtendere ndi madalitso a Allah zikhale pa iye - Mtumiki adanena pomuyankha mngelo Gabriel-mtendere ukhale pa iye - pamene adamufunsa za chikhulupiliro : Chikhulupiliro: kumeneko ndikuti ukhulupilire mwa Allah, Angelo ake, Mabuku ake, Atumiki ake, ndi Tsiku lomliza, komanso ukhulupilire za chikonzero chake: zabwino ndi zoipa zake. [3] Nkhani ikupezeka mu buku la Muslim, Buku la Chikhulupiliro, nambala yake (8), komanso ndi Abu Daud, Buku la Sunnah, mutu okamba za Qadar, nambala yake (4695).
Kukhulupilira mwa Allah wapamwamba.
Tsono mu kukhulupilira mwa Allah muli zinthu zinayi:
Chinthu choyamba: Kukhulupilira zoti Allah wapamwamba alipo:
Ma umboni otsimikiza zoti Allah alipo ndi awa: chilengedwe, nzeru, malamulo achipembedzo ndi zinthu zomwe zimaoneka ndi maso.
Umboni osonyeze kuti Allah alipo ochokera mu chilengedwe cha munthu: cholengedwa china chili chonse chinalengedwe mu chilengedwe chokhulupilira zoti pali Mlengi amene adachilenga popanda kukhala ndi omupatsa maganizo amenewo, kapena kumuphunzitsa, ndipo palibe amene amachoka mu chilengedwe cha maganizo amenewa kupatula amene mu mtima mwake mwapezeka chomusintha maganizo amenewo; Potengera mau a Mtumiki - mtendere ndi madalitso a Allah zikhale pa iye -oti: “Palibe mwana wina aliyense amene amabadwa kupatula kuti amabadwa ndi chilengedwe chokonzeka kukhala Msilamu, koma makolo ake ndi amene amamusandutsa kukhala myuda kapena mkhirisitu kapena opembedza moto”[4]. [4] Nkhani ikupezeka mu buku la Bukhar: gawo lokamba nkhani za Maliro, pamutu wa nkhani yakuti: ‘mwana wamwamuna akalowa Chisilamu ndiye wamwalira, kodi apempheleredwe Swala ya maliro, kodi mwana wachichepele angaitaniridwe ku Chisilamu?’, nambala yake ndi (1292), komanso mu buku la Muslim: gawo lokamba za chikonzero cha Allah, pa mutu otanthauzira mau oti mwana wina aliyense amabadwa ali okonzeka kugonjera malamulo a Allah, ndi lamulo lokamba za ana a anthu osakhulupirira ndi ana a Asilamu omwe amamwalira ali achichepere, nambala yake ndi (2658).
2-Tsono umboni ochokera mu nzeru osonyeza kuti Allah alipo ndi zolengedwazi: zakale ndi zomwe zidzabwere msogolo, ziyenera kukhala ndi Mlengi amene adazipezeketsa; pakuti sizingatheke kuti zidzipezeketse zokha, ndiponso sizingatheke kuti zipezeke mwazizizi.
Sizingathe kudzipanga zokha; chifukwa chinthu sichingadzilenge chokha; kamba koti chisanapezeke chinthucho panalibe, ndiye zitheka bwanji kuti chikhale Mlengi?!
ndiponso ndi zosatheka kuti chipezeke mwazizizi; chifukwa chinthu chili chonse chochitika chimayenera pakhale amene wachichititsa kuti chichitike. Ndipo chifukwa chakuti kupezeka kwake kuli m’ndondomeko yodabwitsa, yogwirizana bwino, ndi yolumikizana kwamphamvu pakati pa zifukwa ndi zotsatira zake, komanso pakati pa zolengedwa china ndi chinzake, zimenezi zimalepheretsa kotheratu kuti zikhale zoti zidangochitika mwazizizi; popeza chinthu chomwe chapezeka mwazizizi sichikhala mwa ndondomeko pa chiyambi cha kupezeka kwake, ndiye zingatheke bwanji kuti chikhale mwa ndondomeko pamene chikupitilira kukhalapo ndi kusintha kwake?!
Ndipo ngati n’kosatheka kuti zolengedwa zonsezi zidzipezekeze zokha, ndiponso kuti zipezeke mwazizizi; nzosapeweka kuti zikhale ndi Mlengi, ndipo iyeyo ndi Allah Mbuye wa zolengedwa zonse.
Allah watchula umboni umenewo ogwiritsa ntchito nzeru komanso umboni otsindikizika mu surah Al-Tur; momwe wayankhula kuti: {Kodi (anthu omuphatikiza Allah ndi zinthu zina) adalengedwa popanda Mlengi owalenga?! Kapena iwo adadzilenga okha?! 35} [Al-Tur:35]. Tanthauzo lake ndi loti: iwo sadalengedwe popanda Mlengi, ndiponso sadazilenge okha; ndiye kuti zatsimikizika kuti Mlengi wawo ndi Allah wodala komanso wapamwamba. Ndichifukwa chake pamene Jubair mwana wa Mut'am - Allah asangalasidwe naye - pomwe adamumva Mtumiki wa Allah -mtendere ndi madalitso a Allah zikhale pa iye - akuwerenga Surah Al-Tur-ndipo adafika pa ndime izi: {Kodi (anthu opembedza mafanowo) adalengedwa popanda owalenga, kapena iwowo adadzilenga okha? 35 Kapena iwo ndi amene adalenga mitambo ndi nthaka? Koma kuti sakutsimikiza (pachikhulupiliro chao)-36. Kapena iwo ndi amene amayang'anira zopereka za Mbuye wako (ndiye amawapatsa omwe awafuna ndikumawamana omwe awafuna)? Kapena iwo ndi amphamvu 37} [Al-Tur:35-37].
Ndipo Jubair, yemwe pa nthawi imeneyo anali opembedza mafano adayankhula kuti: "Mtima wanga unatsala pang'ono kuwuluka, ndipo chimenecho chinali chiyambi cha kukhazikika kwa Chikhulupiliro mu mtima mwanga"[5]. [5] Nkhani ikupezeka mu buku la Bukhar, Surah ya At-Tur, nambala yake (4854).
Ndipo tipeleke fanizo lofotokoza zimenezi: Ngati munthu atakuuzani za nyumba yaikulu ya ufumu yomangidwa bwino, yozunguliridwa ndi minda, ndipo mitsinje ikuyenda pakati pake, yodzala ndi zoyala pansi ndi mabedi, ndipo yokongoletsedwa ndi zokometsera zosiyanasiyana zofunikira ndi zokwaniritsira zake, Ndipo akanakuuza kuti: ndithu nyumba ya ufumu iyi ndi ukwaniri wake onse idadzipezeketsa yokha, kapena idangopezeka mwangozi popanda oipezeketsa”; ndithu iwe ungapange changu pokana ndi kutsutsa zimenezo, ndipo nkhani yake ungaiwerengere ngati mau opanda nzeru. Kodi pambuyo pa zonsezi, ndi zotheka kuti dzikoli mmene lakuliramu: ndi nthaka yake, thambo lake, nyenyezi zake, mmene zinthu zake zimayendera, ndiponso dongosolo lake lodabwitsa, lidadzilenga lokha, kapena lidangopezeka mwangozi popanda olilenga?
3- Tsono umboni ochokera mu malamulo a Allah osonyeza kuti Allah wapamwamba alipo ndi: mabuku onse akumwamba amanena za nkhaniyi, ndiponso malamulo achilungamo amene adadza nawo okhala ndi phindu kwa zolengedwa, ndi umboni osonyeza kuti adachokera kwa Mbuye wa nzeru zakuya, odziwa za zosowa za zolengedwa zake, Ndipo nkhani zokhudza chilengedwe zomwe zadza, zomwe zinthu zooneka zikuchitira umboni kuona kwake, ndi umboni osonyeza kuti zachokera kwa Mbuye wokutha kulenga zimene adazifotokoza.
4-Tsono ma umboni odzera mu kuziona zolengedwa zomwe zimasonyeza kuti Allah alipo; ali mbali ziwiri:
Chimodzi mwa ziwirizo ndi: kuti ife timamva komanso timaona kuyankhidwa kwa opempha, ndi kupulumutsidwa kwa amene ali m'masautso, zomwe ndi umboni osatsutsika oti Allah alipo, ndipo Allah yemwe ali woyera akuyankhula kuti: {Takumbukira (iwe Mtumiki-za nkhani ya) Nowa, nthawi imene adapempha kale, Ife nde tidamuyankha (pomupatsa zomwe amafuna)..} [Al-Anbiya:76]. Allah wapamwamba akuyankhulanso kuti: {Takumbukirani (tsiku la nkhondo ya Badr) pomwe mudapempha thandizo kuchokera kwa Mbuye wanu (kuti akupatseni chipambano pa adani anu) ndipo Iye adakuyankhani (kuti akutumizirani gulu la nkhondo)..}. [Al-Anfal:9].
Ndipo mu Sahih Al-Bukhari, nkhani idachokera kwa Anas bin Malik -Allah asangalasidwe nayeb- amene adati: «Ndithudi munthu wina wochokera ku chipululu adalowa pa tsiku la chisanu - pamene Mtumiki -madalitso ndi mtendere wa Allah zikhale pa iye - amalalikira, ndipo adati: E iwe Mtumiki wa Allah! Chuma chawonongeka, ndipo mabanja ali ndi njala, choncho tipemphereni kwa Allah; pomwepo adakweza manja ake ndipo adapempha, ndipo mitambo idabuka ngati mapiri, ndipo sadatsike pa mimbar yake mpaka ndidaona mvula ikutsika pa ndevu zake» [6]. [6]Nkhani ikupezeka mu buku la Bukhar: buku la Jumua, mutu wa kupempha mvula pa Khutuba tsiku la Jumua, nambala yake (891).
Ndipo la chisanu lotsatira , adaimilira munthu uja wakumidzi, kapena wina, ndipo adati: E Mtume wa Allah! Nyumba zawonongeka, ndipo chuma chamira, choncho tipangireni duwa kwa Allah”; Ndipo adakweza manja ake, ndipo adanena M'neneri madalitso ndi mtendere zipite kwa iye kuti: "E Allah! Izigwa m'mbali mwathu osati pamitu pathu" Sankalozera ku mbali iliyonse koma inkatseguka [7]. [7] Nkhani ikupezeka mu buku la Bukhar: buku la Jumu’ah, mutu wopempha mvula mu khutuba ya tsiku la Jumu’ah, nambala yake ndi (891), komanso mu buku la Muslim: buku la Swala yopempha mvula, mutu wa mapemphero a popempha mvula, nambala yake ndi (897).
Ndipo kuyankhidwa kwa opempha ndi nkhani yoonekeratu mpaka lero lino, kwa amene wadalira Allah moona mtima ndikukwaniritsa zofunikira zoti ayankhidwe.
Mfundo yachiwiri: ndi yakuti zizindikiro za atumiki zomwe zimatchedwa zozizwitsa, zimene anthu amaziona kapena kumva nkhani zake, ndi umboni otsimikizira kupezeka kwa amene adawatumiza, amene ndi Allah wapamwamba; chifukwa izo ndi zinthu zoposa mphamvu za anthu, zimene Allah amazichititsa kuti alimbikitse Atumiki ake, ndi kuwathandiza.
Chitsanzo cha izi: chozizwitsa cha Mussa, mtendele ukhale kwa iye, pamene Allah Wapamwamba adamulamula kuti amenye nyanja ndi ndodo yake, ndiye adaimeya, ndipo idagawanika kukhala njira khumi ndi ziwiri zouma, madzi ali pakati pawo ngati mapiri. Allah wapamwamba akuti: {Ndipo tidambvumbulutsira mau Mussa Oti: menya nyanja ndi ndodo yako, (ndipo adamenya), ndipo nyanja idasiyana (kukhala njira khumi ndi ziwiri mogwirizana ndi chiwerengero cha mitundu ya ana a Israili) mbali iliyonse idali ngati phiri lalikulu-63} [Al-Shura:63].
Ndipo chitsanzo chachiwiri ndi chozizwitsa cha Yesu, mtendere ukhale pa iye, amene adali kuukitsa akufa ndikuwatulutsa m’manda mwawo ndi chilolezo cha Allah, ndipo Allah adanena za iye kuti: {...ndipo ndimaukisa anthu akufa ndi chilolezo cha Allah...} [Al-Imran:49] Komanso Iye (Allah) wati: {...Komanso takumbukira pomwe umawaukitsa akufa ndi chilolezo changa..} [Al-Maidah:110].
Ndipo chitsanzo chachitatu: cha Muhammad mtendele ndi madalitso zipite kwa iye, pamene a Quraysh adampempha chizindikiro, ndipo adaloza ku mwezi, ndipo udagawanika magawo awiri, ndipo anthu adauona, ndipo pa zimenezi pali mau ake (Allah) wapamwamba: {Tsiku lotsiriza lawandikira ndipo mwezi wagawikana. (1) (Anthu opembedza mafano) ataona umboni (wa utumiki wa Muhammad -mtendere ndi madalitso a Allah zikhale pa iye -sangakhulupilire ndipo pambuyo poona chidzindikirocho) adzatsutsa ndikuyankhula mau oti: uwu ndi ufiti wopitilira 2}. [Al-Qamar:1-2].
Motero zizindikiro zooneka izi zomwe Allah wapamwamba amazichititsa; monga chilimbikitso ndi chithandizo kwa Atumiki ake, zimasonyeza umboni otsimikizika wa kupezeka kwake Iye wapamwamba.
Chinthu chachiwiri chimene chikupezeka mukukhulupilira mwa Allah: ndi kukhulupilira mwa Umbuye wake; kutanthauza kuti Iye yekha ndiye Mbuye, alibe wophatikizana naye, ndiponso alibe womuthandiza.
Ndipo Ambuye: ndi mwini chilengedwe, ufumu, ndi ulamuliro, choncho palibe mlengi wina koma Allah, ndipo palibe mwini wina koma Iye, ndiponso ulamuliro onse ndi wake yekha. Allah wapamwamba wati: {..dziwani kuti Iye (Allah) ndiye Mwini kulenga ndi kulamula..} [Al-A'raf:54] Komanso Iye wati: {...Amene (adapanga zimenezo) ndi Allah Mbuye wanu amene ali ndi ufumu. Ndipo milungu yomwe mumaipembedza kusiya Iye, ndiyoti ilibe kena kalikonse ngakhale kochepesesa ngati kaulusi ka mkati mwa tende..} [Fatir:13].
Ndipo sikunadziwike kuti wina aliyense mwa zolengedwa adakana Umbuye wa Allah yemwe ndiwoyera pokhapokha atakhala munthu wamakani chabe, osakhulupilira zimene akuyankhula, monga momwe zinachitikira ndi Farawo, pamene adanena kwa anthu ake kuti: {Ndipo Faraoh adayankhula (mozitukumula) kuti ine ndiye Mbuye wanu wapamwamba-24} [Al-Nazi’at:24] komanso adati: {...E inu anthu olemekezeka: ine sindikudziwa ngati muli ndi mulungu wina oyenera kupembedzedwa posakhala ine...} [Al-Qasas:38], koma zimenezo sizinachokere m'chikhulupiliro chenicheni. Allah wapamwamba adanena kuti: {ndipo adazikana (zomwe anabweretsa Mussa) mwachinyengo ndi kudzikweza chikhalirecho mitima yao imazikhulupilira...} [Surat Al-Naml:14]. Mussa adayankhula kwa Pharaoh, nkhani yomwe Allah waifotokoza mu Quran zokhuza iyeyo Mussayo: {(Mussa) adati: Ndithu wadziwa kuti palibe amene watumiza (mitsutso) iyi kupatula Mbuye wa thambo ndi nthaka kuti zikhale chiphanula maso. Koma ine ndikukuona iwe Farao kuti waonongeka}. [Al-Isra:102] Ndipo pa chifukwa chimenechi ophatikiza Allah ndi mafano adali kuvomereza Umbuye wa Allah wapamwamba, pomwe amamphatikiza Iye pa nkhani ya kupembedzedwa, Allah wapamwamba akuyankhula kuti: {Nena: "Kodi nthaka njayani ndi zomwe zili mmenemo, ngati inu mukudziwa (kanthu)!" Adzanena kuti: "Nza Allah!" Nena: "Nanga bwanji simukumkumbukira (kuti Iye Ngokhoza chilichonse)?" Nena: "Kodi ndani Mbuye wa thambo zisanu ndi ziwiri, ndi Mbuye wa Arsh (Mpando wachifumu) yaikulu?" Anena (kuti): "Nza Allah." Nena: "Nanga bwanji simukumuopa?" Nena: "Kodi ndani yemwe mmanja mwake muli mphamvu yolamulira chinthu chilichonse? Ndipo Iye amateteza zonse. Ndipo palibe chimene chingatetezedwe ku chilango Chake. Ngati inu mukudziwa?" Anena (kuti): "Ndi Allah." Nena: "Nanga mukulozedwa bwanji (ndi satana)?" 84-89} 84-89
Komanso Allah wapamwamba akuyankhula kuti: {Ndipo ukawafunsa: "Ndani adalenga thambo ndi nthaka?" Ndithu ayankha kuti: "Adazilenga (Allah) Mwini mphamvu, Wodziwa."-9}. [Al-zukhruf:9]
Allah woyera wanena kuti: {Ndipo ngati utawafunsa: "Ndani adawalenga?" Anena motsimikiza kuti: "Ndi Allah." Nanga akutembenuzidwa bwanji (Kusiya choona)?-87} [Surat Al-Zukhruf:87].
Ndipo lamulo la Allah woyera limaphatikizapo lamulo la chilengedwe komanso lamulo la chipembedzo, monga momwe Iye ali woyendetsa chilengedwe ndi okhazikitsa lamulo m'menemo ndi zomwe akufuna, malinga ndi momwe nzeru zake zikufunira, chomwechonso Iye ndi olamulira m'menemo pokhazikitsa malamulo a mapemphero, ndi malamulo a kayendesedwe ka zinthu pakati pa anthu, malinga ndi momwe nzeru zake zikufunira. Ndipo aliyense amene wadzichitira opanga malamulo wina mu mapemphero posakhala Allah, kapena olamulira pa zochitika za pakati pa anthu; ndiye kuti wapanga shirk pomphatikiza Iye, ndipo sanakwaniritse chikhulupiliro.
Mfundo yachitatu mwa zomwe kukhulupilira mwa Allah kumatenga: Kukhulupilira zakuyenera kopembedzedwa kwake: Kukhulupilira kuti Iye yekha ndiye opembedzedwa mwachoonadi, opanda ophatikizana naye. Ndipo (Al-Ilah) tanthauzo lake ndi (Al-Ma'luh), kutanthauza kuti: (opembedzedwa) mwachikondi ndi kumulemekeza.
Allah wapamwamba akuyankhula kuti: {Ndipo mulungu wanu ndi Mulungu M'modzi basi. Palibe wopembedzedwa mwachoonadi koma Iye. Ngwachifundo chambiri, Ngwachisoni chosatha.-163} [Al-Baqarah:163] Allah wapamwamba akuyankhulanso kuti: {Allah (Mwini) akuikira umboni kuti: "Palibe wopembedzedwa mwa choonadi koma Iye basi." Ndipo akuikiranso umboni (zomwezi) Angelo ndi eni nzeru (kuti Iye) Ngokhazikitsa chilungamo. Palibe wina wopembedzedwa mwa choonadi koma Iye. Ngwamphamvu zoposa, Ngwanzeru zakuya.-18}. [Al-Imran:18], Ndipo aliyense amene wadzichitira mulungu wina yemwe amamupembedza posakhala Allah, ndithudi umulungu wake ndi olakwika, Allah akuyankhula kuti: Zimenezo nchifukwa chakuti Allah ndi Wowona (alipo;) ndipo zimene akuzipembedza kusiya Iye, nzachabe. Ndipo Allah Ngwapamwambamwamba Ngwamkulu. [Al-Hajj:62]. Ndipo kutchulidwa kwawo kuti milungu, sizimawapatsa kuyenera kwa Umulungu, Allah akuyankhula ponena za (Al-Lati, Al-Uzza, ndi Manat): {Sali (mafanowo) chilichonse koma ndimaina basi omwe mudawatcha inu ndi makolo anu, (molingana ndi zilakolako zanu zachabe); Allah sadatsitse umboni pazimenezo (wotsimikiza pamau anuwo)...} [Al-Najm:23].
Allah akuyankhula zokhuza Hud -mtendere ukhale pa iye - kuti iye adayankhula kwa anthu ake kuti: {...Kodi mukukangana nane pa za maina (a mafano) omwe mudawatcha inu ndi makolo anu, pomwe Allah sadatsitse umboni ulionse (pa milungu yanu yabodzayo?....} [Al-A'raf:71].
Allah akuyankhula zokhuza Yusuf-mtendere ukhale pa iye - pomwe adayankhula kwa azinzake omwe adali nawo ku ndende kuti: {"E inu anzanga awiri a m'ndende! Kodi milungu yambiri yosiyana ndiyo yabwino (kupembedzedwa), kapena Allah M'modzi Mwini mphamvu (pa chilichonse)?" "Simupembedza china kusiya Iye (Allah) koma ndi maina basi amene inu nokha mudawatcha ndi makolo anu, Allah sadatsitse umboni ulionse pa zimenezo....} [Surah Yusuf:39-40].
Ndi chifukwa chake Atumiki -mtendere ndi madalitso zipite kwa iwo- anali akumawauza anthu awo kuti: {...Pembedzani Allah. Inu mulibe mulungu wina koma Iye... [Al-A'raf: 59] Koma anthu omphatikiza Iye ndi zolengedwa zina adakana zimenezo, ndipo adapanga milungu ina kusiya Allah imene amaipembedza pamodzi ndi Allah woyera komanso wapamwamba, ndi kupempha thandizo ndi chipulumutso kwa iyo.
Ndipo Allah wapamwamba adatsutsa chizolowezi cha opembedza mafano chopanga milungu imeneyi ndi umboni uwiri wa nzeru:
Choyamba: kuti milungu imene aipangayi ilibe chilichonse cha makhalidwe a Umulungu; iyo ndi yolengedwa, siilenga, ndipo siingapereke phindu kwa opembedza ake, kapenanso kuwachotsera vuto, ndipo ilibe mphamvu yowapatsa moyo kapena imfa, ndipo ilibe chilichonse chakumwamba, kapenanso siigawana nawo mbali m'menemo.
Allah wapamwamba akuyankhula kuti: {Ndipo m’malo mwa Iye (Allah weniweni, osakhulupirira) adzipangira milungu yomwe siilenga chilichonse koma iyo ndiyomwe idalengedwa; ndiponso ilibe mphamvu yodzichotsera masautso ngakhale kudzidzetsera zothandiza, ndiponso ilibe mphamvu zoperekera irnfa ndi moyo, ngakhale kuukitsa akufa}. [Al-Furqan:3].
Allah wapamwamba akuyankhula kuti: {Nena: "Itanani amene mukuwatcha kuti ndi milungu kusiya Allah (kuti akuthandizeni. Koma sangakuthandizeni chilichonse); pakuti iwo alibe ngakhale kachinthu ka kumwamba ndi pansi kolemera ngati nyelere yaing’ono kwambiri; m’menemo iwo alibe gawo lililonse (lothandizana ndi Allah), ndipo ngakhale Iyenso alibe mthandizi ochokera mwa iwo. Ndipo palibe chithandizo chovomerezeka pamaso pake kupatula kwa amene Iye wavomereza...} [Saba:22-23] Allah wapamwamba akuyankhula kuti: {Kodi akumphatikiza (Allah) ndi zinthu zomwe sizilenga chilichonse pomwe izo zikulengedwa, ndipo sizingathe kuwathandiza kapena kudzithandiza zokha-192}. [Al-A'raf: 191-192].
Ndipo ngati uwu ndiwo mkhalidwe wa milungu imeneyo, ndiye kuti kuzipanga kukhala milungu ndi uchitsiru weniweni, ndiponso ndi chinthu cholakwika kwambiri.
Chachiwiri: ndichoti opembedza mafano aja ankavomereza kuti Allah wapamwamba yekha ndiye Mbuye, Mlengi, amene m'manja mwake muli ufumu wa chinthu chilichonse, ndipo Iye ndiye woteteza, koma palibe angatetezedwe kwa Iye, ndipo izi zikufunikira kuti ampatule Iye yekha pomupembeza monga momwe amampatulira mu Umbuye wake. Monga adanenera Allah wapamwamba: {E inu anthu! Pembedzani Mbuye wanu Yemwe adakulengani inu ndi omwe adalipo kale inu musadadze, kuti mukhale oopa (Allah). Yemwe adakupangirani nthaka kukhala choyala ndi kumwamba kukhala denga, ndipo adatsitsa madzi kuchokera kumwamba, ndipo adatulutsa nao zipatso monga chakudya chanu, choncho musapange anzake kwa Allah pamene mukudziwa-22} [Al-Baqarah: 21-22].
Allah akuyankhulanso kuti: {Ngakhale utawafunsa Iwo (opembedza mafano) kuti: "Ndi ndani amene adawalenga iwowo?" Ndithudi adzayankhula kuti: "Allah (ndi amene adatilenga)". Nanga akutembenuzidwa bwanji (kosiya kumpembedza Allah)-87} [Surah Al-Zukhruf:87].
Allah akuyankhulanso kuti: {Nena (iwe Mtumiki kwa anthu okanirawo) kuti: "Kodi ndani akukupatsani zopatsa kuchokera kumwamba (povumbwitsa mvula), ndi pansi (pomeretsa mmera), nanga ndani amakupatsani kumva ndi kupenya, nanga ndani amene akutulutsa chamoyo kuchokera m’chakufa ndi kutulutsa chakufa kuchokera m’chamoyo? Nanga ndani akukonza zinthu zonse?" Anena: "Ndi Allah". Choncho, nena: "Kodi bwanji simukumuopa?" Choncho, ameneyo ndiye Allah, Mbuye wanu owona. Choncho, pambuyo pa choonadi ndi chiyani china chosakhala kusochera? Kodi mukuchotsedwa bwanji (kusiya chowonadi) -32} [Surah Yunusu: 31-32].
Mfundo yachinayi ya Kukhulupilira mwa Allah: Kukhulupilira za maina ake ndi mbiri zake:
Ndiko kuti: kutsimikizira zimene Allah wadzitsimikizira yekha m'buku lake, kapena mu Sunnah ya Mtumiki wake (s.a.w), mwa maina ndi mbiri, m'njira yoyenerana ndi Iye, popanda kusintha matanthauzo, kapena kuzikanira, kapena kuyelekezera mmene zilili, kapena kufanizira ndi zina, Allah wapamwamba adati: {Allah ali ndi maina okongola choncho, mpempheni kudzera mwa Iwo, ndipo muwasiye anthu omwe amasiya kutsatira zoona zokhuza maina ake (ndikumawapatsa ena maina amenewa omwe sali Allah, kapena kuwakana mainawa, kapena kutembenuzo matanthauzo ake kapena kuwafanizira mainawo ndi zina zotero, anthu omwe amachita zimenezi) akalipidwa (zilango zowawa kwambiri) kamba ka zomwe amachitazi-180} [Al-A'raf:180] Allah wapamwamba akuyankhulanso kuti: {...Iye (Allah) ali ndi mbiri zapamwamba (pa mbiri iliyonse yomwe amakhala akusimbidwa nayo) ku mitambo ndi panthaka. Iye ndi wa mphamvu (amene sagonjetsedwa ndi kena kalikonse) ndi wa nzeru zakuya mu zoyankhula komanso zochita zake} [Al-Rum:27]. Allah wapamwamba akuyankhulanso kuti: {...Palibe chilichonse chomwe chimafanana ndi Iye, Iye ndi wakumva (zoyankhula za akapolo ake), amaona (zochita zawo).} [Al-Shura:11].
Magulu awiri a anthu adasokera pa nkhani imeneyi:
Limodzi mwa maguluo ndi: (Al-Mu'attilah) amene amakana maina komanso mbiri za Allah, kapena zina mwa izo, ponena kuti kutsimikizira izi kwa Allah kumabweretsa kufanizira, ndiko kuti: kumufanizira Allah wapamwamba ndi zolengedwa zake. Ndipo kunena kumeneku nkopanda pake; pazifukwa zingapo, mwa izo ndi izi:
Choyamba: kuti kumadzetsa zinthu zopanda pake; monga kutsutsana m'mawu a Allah, chifukwa chakuti Allah adadzitsimikizira maina ndi mbiri zake, komanso adakana kuti palibe chilichonse chofanana naye, Zikadakhala zoti kutsimikizira kwake kukubweretsa kufanizira; ndiye kuti mau a Allah akanakhala kuti akutsemphana komanso akutsutsana okhaokha.
Chachiwiri: Kufanana kwa zinthu ziwiri pa dzina kapena mbiri sikukutanthauza kuti zinthuzo zili zofanana ndendende, pakuti umapeza anthu awiri akufanana ponena kuti aliyense wa iwo ndi munthu, wakumva, openya, ndi oyankhula, Ndipo sizikutanthauza kuti afanane mu makhalidwe a chibadwa cha umunthu, makutu, maso, ndi kuyankhula.
Ndipo umaona zinyama zili ndi manja, miyendo, ndi maso, koma kukhala ndi ziwalozi sikukakamiza kuti manja awo, miyendo yawo, ndi maso awo zifanane.
Ngati kusiyana kumaonekera pakati pa zolengedwa m'maina kapena mbiri zomwe zili zofanana, ndiye kuti kusiyana pakati pa Mlengi ndi cholengedwa n'koonekeratu ndiponso n'kwakukulu kwambiri.
Gulu lachiwiri: (Ofanizira) ndi amene amavomereza maina a Allah ndi mbiri zake, koma n'kumafanizira Allah wapamwamba ndi zolengedwa zake, ponena kuti ili ndiye tanthauzo limene malembo akusonyeza; chifukwa Allah wapamwamba amalankhula ndi akapolo ake ndi zomwe amazimvetsa. Koma kunena uku n'kwabodza; pazifukwa zingapo, zina mwa izo ndi izi:
Choyamba: kuti kufanana kwa Allah ndi zolengedwa zake ndi nkhani imene nzeru ndi malamulo a Allah zimailepheretsa, ndipo sizingatheke kuti zopezeka mmalemba a buku la Quran ndi Sunnah zikhale zopanda pake.
Chachiwiri: ndithu Allah amayankhula ndi akapolo ake ndi zomwe amazimvetsetsa pa mbali ya tanthauzo lake loyambirira, koma choona chake ndi mkhalidwe weniweni wa tanthauzo limenelo, Allah wapamwamba adadzipatulira yekha kuzidziwa pa zokhudzana ndi Iye mwini ndi mbiri zake.
Ndipo Allah akadzitsimikizira yekha kuti Iye ndi wokumva; ndiye kuti tanthauzo la kumva limadziwika (komwe ndi kuzindikira mau), koma mmene kumva kwa Allah kulili sikudziwika; chifukwa kumva kumasiyana ngakhale pakati pa zolengedwa zokha; choncho kusiyana pakati pa Wolenga ndi cholengedwa nkoonekera kwambiri komanso kwakukulu.
Ndipo pamene Allah Wapamwamba adatiuza kuti Iye anakhazikika pampando wake wa chifumu; tanthauzo leni leni la kukhazikikaku limadziwika, koma mmene Iye anakhazikikira kwenikweni ife sitikudziwa pankhani ya kukhazikika kwa Allah pampando wake wachifumu; chifukwa mmene kukhazikiika kulili kumbali ya zolengedwa kumasiyana. Chifukwa kukhazikika pampando okhazikika sikufanana ndi kukhazikika pa chishalo cha ngamila yovuta ndi yothaŵa, ndiye ngati zimenezi zikusiyana pa nkhani ya zolengedwa; kusiyana kumeneku pakati pa Mlengi ndi cholengedwa nkowonekeratu kwambiri ndiponso nkwakukulu.
Ndipo kukhulupilira mwa Allah wapamwamba monga mmene tafotokozera kumaabalira okhulupilira zipatso zolemekezeka, zina mwa izo:
Choyamba: Kukwaniritsa Tauhid ya Allah wapamwamba, kotero kuti pasakhale chiyembekezo kapena mantha kwa wina aliyense kusiya Iye, ndipo asapembedze wina kupatula Iye yekha.
Chachiwiri: Kumukonda Allah mokwanira komanso kumulemekeza mogwirizana ndi maina ake okongola, ndi mbiri zake zapamwamba.
Chachitatu: Kukwaniritsa kupembedzedwa kwake pochita zimene adalamula, ndikupewa zimene adaletsa.
*
Kukhulupilira mwa Angelo
Angelo: Ndi dziko losaoneka ndi maso, zolengedwa, opembedza Allah wapamwamba, ndipo alibe chilichonse mwa makhalidwe a Umbuye kapena Umulungu. Allah wapamwamba adawalenga kuchokera mu kuwala, ndipo adawapatsa kumvera kotheratu ku lamulo lake, ndi mphamvu zokwaniritsira lamulolo. Allah wapamwamba wati: Ndipo amene ali kwa Iye (Angelo), sadzitukumula posiya kumulambira, ndiponso satopa (ndi mapemphero), amamutamanda usana ndi usiku salekeza [Al-Anbiya:19-20].
Ndipo iwo ndi ochuluka kwambiri, palibe amene angakwanitse kuwawerenga kupatula Allah yekha wapamwamba, ndipo zatsimikizika m'ma Sahihi awiri kuchokera mu hadith ya Anasi (Allah asangalasidwe naye) pa nkhani ya MIRAJ, kuti Mneneri - mtendere ndi madalitso a Allah zikhale pa iye - adakwezedwera Baytul Ma'mur kumwamba, yomwe amapempheramo tsiku lililonse angelo okwana sevente sauzande, ndipo akachoka, sabwereramonso m’menemo.
Ndipo kukhulupilira mwa angelo kumatenga mfundo zinayi:
1- Kukhulupilira kuti alipo.
Chachiwiri: Kukhulupilira mwa amene tawadziwa ndi mayina awo (monga Gabulieli), ndipo amene sitikudziwa mayina awo timawakhulupirira mchigulugulu.
Chachitatu: Kukhulupilira mbiri zawo zomwe tazidziwa, monga mbiri za Gabulieli, Mtumiki - mtendere ndi madalitso a Allah zikhale pa iye -adanena kuti adamuona m'maonekedwe ake amene Allah adamulengera, ali ndi mapiko mazana asanu ndi limodzi, amene adatseka mlengalenga.
Ndipo nthawi zina mngelo amasanduka ndi lamulo la Allah wapamwamba, n’kukhala ndi maonekedwe a munthu wamwamuna, Monga momwe zidamuchitikira (Jibril) pamene Allah Wapamwamba adamtumiza kwa Mariya ndipo adadzionetsera kwa iye m’maonekedwe a munthu wangwiro. Ndi pamene adadza kwa Mtumiki -madalitso ndi mtendere zikhale pa iye - ali chikhalire pakati pa maswahaaba ake, adadza kwa iye m'maonekedwe a munthu okhala ndi zovala zoyera kwambiri, tsitsi lakuda kwambiri, sichimaoneka mwa iye chizindikiro chapaulendo, ndipo palibe aliyense mwa maswahaaba ake amene anamuzindikira. Ndipo anadzakhala pafupi ndi Mtumiki -madalitso ndi mtendere zikhale pa iye - ndipo anagundanitsa maondo ake ndi maondo ake (a Mtumiki), ndipo anaika zikhatho zake pa ntchafu zake, ndipo adafunsa Mtumiki - madalitso ndi mtendere zikhale pa iye - za Chisilamu, Chikhulupiliro, Ubwino, ndi za Chimaliziro, ndi zizindikiro zake. Mtumiki - madalitso ndi mtendere zikhale pa iye - adamuyankha, ndipo adachoka. Kenako Mtumiki -madalitso ndi mtendere zikhale pa iye- adati: «Uyu ndi Jibril; anabwera kudzakuphunzitsani chipembedzo chanu»[8]. [8] Nkhani ikupezeka mu buku la Muslim: buku la Chikhulupiliro, mutu wofotokoza za Chikhulupiliro, Chisilamu, ndi ubwino, ndiponso kufunika kokhulupilira potsimikiza za chikonzero cha Allah, nambala yake (8).
Chimodzimodzinso Angelo amene Allah adawatumiza kwa Abraham, ndi Lot, adali m'maonekedwe a amuna.
Chachinayi mwa zimene kukhulupilira mwa angelo kumatenga: Kukhulupilira zochita zawo zomwe tazidziwa, zomwe amazichita ndi lamulo la Allah wapamwamba; monga kumuyeretsa Iye, ndi kumupembedza Iye usiku ndi usana popanda kutopa kapena kufooka.
Ndipo ena mwa iwo amakhala ndi ntchito zapadera.
Monga: Gablieli, okhulupirika pa chibvumbulutso cha Allah, amene Allah amamutuma nacho kwa Aneneri ndi Atumiki.
Monga: Mikaeli: ndi amene anapatsidwa udindo ogwetsa mvula ndi kumeretsa zomera.
Israfili: anapatsidwa udindo oliza Lipenga pa tsiku lotsiriza, pamene zolengedwa zidzaukitsidwa.
Mwachitsanzo: mngelo wa imfa: adapatsidwa ntchito yochotsa mizimu ya akapolo nthawi yomwalira ikakwana.
Komanso monga Malik: adapatsidwa ntchito ya Moto, ndipo iye ndi msungi wa Moto.
Chisanzo china: Angelo amene anapatsidwa udindo woyang’anira ana a m’mimba, munthu akakwanitsa miyezi inayi ali m’mimba mwa mayi ake, Allah amatumiza mngelo kwa iye ndikumulamula kulemba riziki lake, ndi nthawi ya imfa yake, ndi ntchito zake, ndiponso kuti adzakhala watsoka kapena wodala.
Chisanzo china: Angelo amene anapatsidwa udindo wosunga ntchito za ana a Adamu ndi kuzilemba, munthu aliyense ali ndi angelo awiri, mmodzi kudzanja lamanja ndipo wachiwiri kudzanja lamanzere.
Chisanzo china: angelo omwe adapatsidwa ntchito yofunsa munthu wakufa akamuika m'manda mwake; amamdzera angelo awiri, ndipo amamufunsa za Mulungu wake, ndi chipembedzo chake, ndi Mtumiki wake.
Ndipo kukhulupilira mwa Angelo kumabala zipatso zolemekezeka, zina mwa izo ndi:
Choyamba: Kuzindikira za ukulu wa Allah wapamwamba, ndi mphamvu zake, ndi ulamuliro wake; pakuti ukulu wa cholengedwa umasonyeza ukulu wa Mlengi.
Chachiwiri: kuyamika Allah pa chisamaliro chake pa ana a Adamu; popeza adaika mwa angelo amenewa amene amawasunga, ndi kulemba zochita zawo, ndi zinthu zina zowathandiza.
Chachitatu: Kuwakonda angelo pa ntchito yawo yopembedza Allah wapamwamba.
Ndipo adakana anthu ena mwa osokera kuti angelo ali ndi matupi, ndipo adati: Iwo ndi mphamvu chabe za ubwino zobisika mu zolengedwa.Uku ndi kutsutsa Buku la Allah ndi ndi Sunnah ya Mtumiki wake - mtendere ndi madalitso zikhale pa iye - ndi mgwirizano wa Asilamu.
Allah wapamwamba adanena kuti: {Kutamandidwa konse ndi kwa Allah Mlengi wa mitambo ndi nthaka, amene adawapanga Angelo kukhala Atumiki omwe ali ndi mapiko awiri,ena atatu,ena anayi...} [Fatir:1].
Allah wapamwamba akuyankhulanso kuti: {...Ukanakhala kuti umaona pa nthawi yomwe Angelo a imfa amakhala akuchosa mizimu ya osakhulupilira, (amaichosa mizimu yawo) uku akuwamenya nkhope zawo (akakhala kuti awayang'anitsa nkhope zawo), ndiponso (amawamenya) misana yawo (akakhala kuti akuthawa)...} [Al-Anfal: 50].
Allah wapamwamba akuyankhulanso kuti: {...Ukanakhala kuti umaona (iwe Mtumiki) pamene achinyengo ali mu ululu wa imfa, Angelo atatambasula manja awo (powazunza ndikuwamenya, uku akuwayankhula mwa nkhanza kuti): Tulutsani nokha mizimu yanu (ife tidzangoitenga ikatulukamo)...} [Al-An’am:93].
Allah wapamwamba akuyankhulanso kuti: {...Kufikira pamene mantha achoka m'mitima mwawo (Angelo) amayankhula (kwa Gabriel) kuti: "Kodi Mbuye wanu wayankhula chani?" Ndiye amayankha kuti: "Wayankhula zoona zokha zokha, Iyeyo ndi wapamwamba, ndi wamkulu}. [Saba:23].
Allah akuyankhula pa nkhani yokhuza anthu omwe akalowe ku minda yaku mtendere:: {...Ndipo Angelo adzikalowa kwa iwo makomo onse (akuwafunira zabwino ndi kumawapatsa moni ndawi zonse zomwe adzikalowa kwa iwo poyankhula kuti:) Mtendere uli pa inu kamba kakupilira kwanu (potsatira malamulo a Allah, komanso kamba kopilira ndi zikonzero zake zopweteka,komanso kamba kopilira posiya kunyozera malamulo ake), kaye kukongola mathero anu} [Al-Rad:23-24]
Zinalembedwa mu buku la Bukhar kuchokera kwa Abu Huraira - Allah asangalasidwe naye - kuti Mtumiki -mtendere ndi madalitso a Allah zikhale pa iye - adati: "Allah akakonda kapolo, amaitana Gabriel nati: ndithu Allah akumkonda munthu wakuti wakuti, choncho, iwenso uzimukonda ameneyo,ndipo Gabriel amamukonda, kenako Gabriel amaitana pakati pa Angelo ndikuyankhula kuti: ndithudi Allah akumukonda munthu wakuti wakuti, ndiye nanunso muzimukonda, ndipo Angelo amamukonda munthu ameneyo, kenako Allah amaika mmitima mwa anthu chikondi chomukonda munthuyo."[9]. [9] Nkhani ikupezeka mu Bukhar, buku la chiyambi cha chilengedwe, khomo la kutchula za Angelo, nambala yake ndi (3037), komanso mu Muslim, buku la ubwino, kulumikiza ubale, ndi kukhala ndi makhalidwe a bwino, khomo la: Allah akamukonda kapolo amampangitsa kukondedwa ndi anthu, ndipo nambala yake ndi (2637).
Mulinso nkhani yochokera kwa Abu Huraira - chisangalalo cha Allah chikhale pa iye - adati: Mtumiki -mtendere ndi madalitso a Allah zikhale pa iye - adati: «Likafika tsiku la chisanu pakhomo lililonse la mzikiti pamakhala angelo akulemba woyamba kulowa, kenako otsatira, ndipo Imam akakhala pansi, amapinda zolemba zawo ndikubwera kudzamvetsera Khutuba»[10]. [10] Nkhani ikupezeka mu Bukhar: Buku la Jumu’ah, Mutu wokhudza kumvetsera Khutbah, nambala yake ndi (887), komanso mu Muslim: Buku la Jumu’ah, Mutu okhudza ubwino opita msanga tsiku la Jumu’ah, nambala yake ndi (850).
Ndipo malembawa ndi oonekera poyera posonyeza kuti Angelo ndi zolengedwa zokhala ndi matupi, osati mphamvu zopanda thupi, monga mmene ananenera opotoka, ndipo pa umboni wa malembawa n’pamene Asilamu onse adagwirizana.
*
Kukhulupilira Mabuku
Mabuku: ndi mau ochulukitsa a (buku), omwe amatanthauza (cholembedwa).
Ndipo tanthauzo lake apa ndi: mabuku amene Allah wapamwamba adawavumbulutsa kwa Atumiki ake, monga chisoni kwa zolengedwa, ndiponso chiongoko kwa iwo; kuti kudzera mwa iwo afikire ku chimwemwe chawo pa dziko lapansi ndi pa tsiku lachimaliziro.
Ndipo kukhulupilira mabuku mumapezeka zinthu zinayi:
1-Kukhulupilira kuti adavumbulutsidwa kuchokera kwa Allah mwachoonadi.
Chachiwiri: Kukhulupilira mwa mabuku amene tawadziwa ndi mayina awo: monga Qur’an yomwe idavumbulutsidwa kwa Muhammad -mtendere ndi madalitso a Allah zikhale pa iye, ndi Torah yomwe idavumbulutsidwa kwa Mose-mtendere ndi madalitso a Allah zikhale pa iye. Komanso Uthenga wabwino omwe unavumbulutsidwa kwa Issah -mtendere ukhale kwa iye Ndi Zaburi yomwe adapatsidwa Daud - mtendere ukhale kwa iye, tsono mabuku omwe sitikudziwa mayina awo, timawakhulupirira mchigulugulu.
Chachitatu: Kuvomereza nkhani zake zotsimikizika, monga nkhani za mu Qur’an, ndi nkhani za m’mabuku akale zomwe sizidasinthidwe kapena kusokonezedwa.
4-Kugwiritsa ntchito malamulo ake omwe sanachotsedwe, ndikukhutira nawo komanso kuwagonjera, khaya tazindikira zolinga zake kapena sitinazindikire, ndipo mabuku onse akale adachosedwa malamulo ake ndi buku lolemekezeka la Quran, Allah wapamwamba adanena kuti: {Ndipo takuvumbulutsira buku MWA choonadi, lomwe likuikira umboni maabuku omweu adalipo patsogolo pake, ndi kuwateteza..} [Al-Maidah:48] Kutanthauza: Oika malamulo.
Motero: sikuloledwa kugwiritsa ntchito lamulo lililonse la m'mabuku akale, pokhapokha lomwe lili lolondola, ndipo Qur'an yalivomereza.
Kukhulupilira za mabuku a Allah kumabereka zipatso zolemekezeka, zina mwa izo ndi:
Choyamba: Kuzindikira za chisamaliro cha Allah wapamwamba pa akapolo ake; popeza adavumbulutsa kwa mtundu uliwonse buku lowaongolera nalo.
Chachiwiri: Kuzindikira nzeru za Allah wapamwamba m'malamulo ake, ndikuti adakhazikitsira mtundu uliwonse choyenerana ndi makhalidwe awo, Monga momwe Allah wapamwamba akuyankhulira: {...Ndipo m'bado ulionse mwa inu tidaukira malamulo oti adzigwiritsa ntchito komanso kachitidwe ka zinthu komveka bwino (koti adzitsatira pogwiritsa ntchito malamulo achipembedzowo)...} [Al-Maidah:48].
Chachitatu: Kuthokoza madalitso a Allah pa zimenezo.
*
Kukhulupilira mwa Atumiki
Atumiki: Ndi mau ochuluka a (Mtumiki) ndi tanthauzo la: (otumizidwa), kutanthauza kuti: otumidwa kuti alengeze chinachake.
Tanthauzo apa ndi: munthu amene adavumbulutsidwira lamulo ndipo adalamulidwa kulifalitsa.
Ndipo oyamba mwa Atumiki ndi Nowa - mtendere ukhale pa iye, ndipo otsiriza mwa iwo ndi Muhammad - mtendere ndi madalitso a Allah zikhale pa iye.
Allah wapamwamba akuyankhula kuti: {Ndithudi, takuvumbulutsira (chivumbulutso) monga momwe tidamubvumbulutsira Nowa ndi aneneri Amene anadza pambuyo pake...} [Al-Nisa:163]
Ndipo mu buku la Bukhar kuchokera kwa Anasi Bin Maliki, Allah asangalale naye, mu nkhani ya Chipembedzero, ndithu Mtumiki - madalitso ndi mtendere zipite kwa iye adati: “Kwanenedwa kuti anthu adzapita kwa Adamu, kuti awapempherere, ndipo adzapepesa kwa iwo ndipo adzanena kuti: "Pitani kwa Nowa, Mtumiki oyamba amene Allah adamutuma.” Ndipo adatchula nkhani yonse[11]. [11] Nkhani adaitulutsa Bukhar: mutu wa Tawhid, gawo lonena za mau a Allah wapamwamba oti: (zimene ndazilenga ndi manja anga aŵiri), nambala yake ndi (7410), komanso mu buku la Muslim: mutu wa chikhulupiliro, gawo lonena za munthu amene akakhale janna ya pansi, nambala yake ndi (193).
Allah wapamwamba akuyankhula zokhuza Muhammad - mtendere ndi madalitso a Allah zipite kwa iye-kuti: {Muhammad sikuti ndi bambo wa wina aliyense mwa amuna anu, koma ndimtumiki wa Allah komanso womaliza mwa aneneli......} [Surah Al-Ahzab].
Ndipo palibe mtundu ulionse umene unakhalapo opanda Mtumiki amene Allah amamutuma ndi malamulo ake apadera kwa anthu ake, kapenanso mneneri amene amamuvumbulutsira malamulo a amene adamutsogolera; kuti awakonzenso, Allah wopambana adati: {Ndithudi tidatumiza ku mmado ulionse Mtumiki amene adali kuwawuza zoti: "Pembedzani Allah ndikuwatalikira mafano...} [Al-Nahl:36].
Allah wapamwamba akuyankhulanso kuti: {...Ndipo palibe m'bado (mu mibado yomwe idapita m'mbuyomu) kupatula kuti adapitamo mchenjez} [Fatir:24].
Allah wapamwamba akuyankhulanso kuti: {Ndithudi, tidaivumbulutsa Taurat yokhala ndi chiwongoko ndi kuunika; aneneri (a Allah) omwe adagonjera Allah adali kulamulira nayo Ayuda...} [Al-Maidah:44].
Ndipo atumiki ndi anthu olengedwa, alibe kena kalokonse kokhuzana ndi Umbuye kapena kupembezedwa, adayankhula Allah wapamwamba za mtumiki wake Muhammad, amene ndi mtsogoleri wa Atumiki, ndiponso wolemekezeka kwambiri pa iwo onse kwa Allah kuti: {Nena (iwe Mtumiki): Ine ndekha ndilibe mphamvu yodzibweretsera chabwino kapena kudzichotsera choipa, koma chimene Allah wafuna, ndikadakhala kuti ndikudziwa zobisika ndikadadzichulukitsira zabwino ndipo choipa sichikadandikhudza, ine sindili chilichonse koma mchenjezi ndi ouza anthu okhulupilira nkhani zabwino-188} [Al-A'raf:188] .
Allah wapamwamba akuyankhulanso kuti: {Nena (iwe Mtumiki) kuti: "Ine ndilibe udindo okupatsani mavuto kapena chilungamo (ndi zabwino)". Nena: "Ine palibe amene anganditeteze kwa Allah ndipo sindidzapeza pothawirapo popanda Iye-22} [Al-Jinn:21-22].
Atumiki nawonso zimawachitikira zomwe anthu ena onse zimawachitikira: monga matenda, imfa, kukhumbira chakudya ndi chakumwa, ndi zina zotero. Allah wapamwamba adayankhula zokhuza Abraham- mtendere ukhale pa iye-pomwe Abrahamuyo amamufotokoza Mbuye wake amene iye amamupembedza ponena kuti: {Ndi yemwe amandidyetsa ndi kundimwetsa (79) Ndipo ndikadwala iyeyo ndi amene amandichiritsa(800 Iye ndi amene adzandipase imfa kenako nkudzandiukitsanso kwa akufa-81}. [Al-Shura:79-81].
Mtumiki wa Allah - mtendere ndi madalitso a Allah zikhale pa iye -adati: "Ndithu ine ndi munthu ngati inu, ndimaiwala monga momwe inunso mumaiwalira, choncho ngati ndaiwala, ndikumbutseni[12]." [12] Nkhani ikupezeka mu buku la Bukhar: Mitu ya nkhani za Qiblah, mutu okhudza kulunjika ku Qiblah kulikonse kumene munthu ali, nambala yake ndi (392), komanso mu buku la Muslim: Buku la mizikiti ndi malo opempherera mutu okhudza kuiwala mu Swala ndi kupanga Sajda yake, nambala yake ndi (572).
Ndipo Allah adawasimba ndi ukapolo kwa Iye, ali pa maulemelero awo apamwamba, ndiponso powachemerera. Adanena Allah wapamwamba zokhuza Nowa - madalitso ndi mtendere wa Allah zikhale pa iye-: {...Ndithu iye adali kapolo wothokoza kwambiri} [Al-Isra:3] Ndipo Allah adayankhula zokhuza Muhammad - mtendere ndi madalitso a Allah zikhale pa iye - kuti: {Watukuka Mwini kupereka madalitso yemwe wavumbulutsa Qur’an kwa kapolo wake kuti akhale mchenjezi kwa zolengedwa zonse-1} [Al-Furqan:1].
Ndipo adanena zokhudza Ibrahim, ndi Ishaq, ndi Yaqoob - mtendere ukhale kwa iwo-: {Kumbukira (iwe Mtumiki) za akapolo athu Ibrahim, Ishaq ndi Yaqoob eni mphamvu (pa ntchito yachipembedzo) ndi kuyang’ana kozindikira. Ndithudi, ife tidawapatsa chikhalidwe chabwino (chomwe) ndikukumbukira nyumba yomaliza (nthawi zonse), ndipo iwo ali kwa ife mwa osankhidwa abwino} [Swad:45-47].
Allah adanena zokhuza Yesu mwana wa Mariya - mtendere ukhale pa iye- kuti: {Iye sadali kanthu koma ndi kapolo amene tidampatsa mtendere; ndipo tidamchita kukhala chitsanzo (chodabwitsa) cha ana a Israyeli} [Al-zukhruf:59].
Ndipo kukhulupilira mwa Atumiki kumatenga mfundo zinayi:
Choyamba: Kukhulupilira kuti uthenga wawo ndi owona ochokera kwa Allah, munthu amene angakanire uthenga wa m'modzi wa iwo, ndiye kuti wakanira onse, Monga momwe Allah wapamwamba akunenera: Anthu a Nowa adatsutsa Atumiki. [Al-Shuara:105] Choncho Allah adawachita kukhala okanira Atumiki onse, ngakhale kuti kunalibe Mtumiki wina aliyense kupatula iyeyo pamene amamukana. Motsatira zimenezi, Akhirisitu amene adamukana Muhammad - mtendere ndi madalitso a Allah zikhale pa iye - ndipo sanamutsatire; ndithudi amukananso Yesu mwana wa Mariya, ndipo sali omutsatira iyenso. Makamaka popeza iye adawauza nkhani yabwino yonena za kubwera kwa Muhammad - mtendere ndi madalitso a Allah zikhale pa iye -, ndipo palibe tanthauzo lina la nkhani yabwino imeneyi kwa iwo, kupatula loti iye ndi Mtumiki otumidwa kwa iwo, kuti Allah awapulumutse kudzera mwa iye ku kusochera, ndi kuwatsogolera ku njira yolungama.
Chachiwiri: Kukhulupilira mwa amene tawadziwa ndi mayina awo, monga: Muhammad, Abraham, Mose, Yesu, ndi Nowa, mtendere ukhale pa iwo. Ndipo asanuwa ndi Atumiki okhala ndi chitsimikizo chachikulu, ndipo Allah wapamwamba adawatchula malo awiri mu Qur'an, m'mau ake oti: {Ndipo (akumbutse) pamene tidalandira kuchokera kwa Aneneri (onse) pangano lawo,ndi kwa iwe, ndi kwa Nowa, Ibrahim, Mussa, ndi Isa (Yesu) mwana wa Mariya. Ndipo tidatenga kwa iwo pangano lamphamvu (kuti adzafikitsa uthenga wa Allah kwa anthu ndi kuitanira anthu ku chipembedzo cha Allah) -7} [Al-Ahzab:7] Ndi mau ake oti: {Wakhazikitsa kwa inu chipembedzo chonga chomwe adam’langiza Nowa. Ndipo chimene takuvumbulutsira iwe ndi chimenenso tidavumbulutsira Ibrahim, Mûsa, ndi Isa (Yesu) kuti: mulimbike chipembedzo (potsatira malamulo) ndikuti musalekane pa chipembedzo. Koma ndizovuta kwa opembedza mafano kuvomera zimene ukuwaitanira. Allah amadzisankhira amene wam’funa ndipo amamuongolera amene akutembenukira kwa Iye}. [Al-Shura:13]
Koma za amene sitikudziwa mayina awo; timawakhulupilira mchigulugulu, Allah wapamwamba adati: {Ndithu tidawatuma atumiki patsogolo pako; ena mwa iwo tidakusimbira nkhani zawo ndi maina awo, ena mwa iwo sitidakusimbire...}. [Ghafir:78].
3-Kuvomeleza nkhani zawo zotsimikizika.
Chachinayi: Kugwiritsa ntchito malamulo a yemwe anatumidwa kwa ife mwa iwo, ndipo ndiye otsiriza wawo Muhammad - mtendere ndi madalitso zipite kwa iye, yemwe anatumizidwa kwa anthu onse. Allah wapamwamba adati: {Ndikulumbira Mbuye wako, iwo sangakhale okhulupirira moona pokhapokha akuyese muweruzi wawo pa zomwe akukangana pakati pawo. Kenako asaone vuto m’mitima yawo pa zomwe waweruza, ndipo adzipereke kwathunthu pogonjera (chiweruzo chako) -65} [Al-Nisa:65].
Kukhulupilira mwa Atumiki kuli ndi zipatso zolemekezeka monga:
Choyamba: Kuzindikira chisoni cha Allah ndi chisamaliro chake pa akapolo ake; kotero kuti adawatumizira Atumiki; kuti adzawaongolere ku njira ya Allah wapamwamba, ndi kuwalangiza momwe angamupembedzere Allah; chifukwa nzeru za munthu pa zokha sizingathe kuzindikira zimenezo.
Chachiwiri: kumuthokoza Allah kamba ka mtendere waukulu ngati umenewu.
Chachitatu: kuwakonda Atumiki -madalitso ndi mtendere zikhale pa iwo- ndi kuwalemekeza, ndi kuwachemelera ndi mobility zomwe zikuyenerana nawo; chifukwa chakuti iwo ndi Atumiki a Allah, ndipo adakhazikika pomupembedza Iye, pofalitsa uthenga wake, ndi polangiza akapolo ake.
Ndipo amakani adatsutsa aneneri awo, ponena kuti aneneri a Allah wapamwamba sayenera kukhala anthu! Ndipo Allah wapamwamba adatchula bodza limeneli, ndipo adaliononga ndi mawu ake (Allah) Woyera akuti: {Ndipo palibe chimene anthu opembedza mafano (aku Makka) chawaletsa kukhulupilira (choona) pamene chiongoko chawadzera, koma kunena kwawo (kwa umbuli kwakuti): "Kodi Allah amatuma munthu kukhala Mtumiki wake?" Nena: "Pakanakhala kuti pansi pano panali angelo akuyenda mwamtendere, tikanatsitsa kwa iwo mngelo kuchokera kumwamba kukhala Mtumiki ." - 95} [ Al-Isra:94-95]
Ndipo Allah anatsutsa bodza limeneli ponena kuti Mtumiki akuyenera kukhala munthu; chifukwa iye adatumizidwa kwa anthu a padziko lapansi, amenenso ndi anthu, ndipo pakadakhala kuti anthu a padziko lapansi ali angelo, ndithu Allah akadawatsitsira kuchokera kumwamba mngelo kukhala Mtumiki; kuti akhale ngati iwowo, Ndipo momwemonso Allah wapamwamba ndimmene adakambira za anthu okanira Atumiki kuti iwo adati: {...Inu sikanthu kena koma ndinu anthu ngati ife. Mungofuna kutitsekereza ku zimene ankazipembedza makolo athu; choncho tibweretsereni umboni woonekera, Atumiki awo adati kwa iwo: "Ife sikanthu kena koma ndife anthu ngati inu, koma Allah amadalitsa amene Iye amfuna mwa atumiki ake. Ndipo sitingakubweretsereni umboni woonekera pokhapokha ndi chilolezo cha Allah."} [Ibrahim:10-11].
*
Kukhulupilira za tsiku lomariza
Tsiku lomaliza: Ndi tsiku Kiyama limene anthu adzaukitsidwe kuti akawerengedwe ntchito zawo ndi kulipidwa.
Ndipo latchedwa ndi dzina limeneli chifukwa kulibe tsiku lina pambuyo pake, tero anthu a ku minda ya mtendere adzakhanzikika m'malo mwawo, komanso a ku Moto adzakhanzikika m'malo mwawo.
Ndipo kukhulupilira za tsiku lomaliza kumatenga mfundo zitatu:
Choyamba: Kukhulupilira za kuukitsidwa: ndiko kuukitsa akufa pamene lipenga lidzayimbidwa kachiwiri; ndipo anthu adzaimirira pamaso pa Mbuye wa zolengedwa zonse, ali opanda nsapato, ali amaliseche, osachita mdulidwe. Allah Wapamwamba adati: {....(Tsiku la chiweruzo) tidzaukitsa (anthu ali) monga m'mene tidawalengera kumayambiliro, (monga momwe azimayi awo adawaberekera), limenelo ndipangano lathu, ndithu Ife zomwe timalonjeza timapanga nthawi zonse} [Al-Anbiya:104].
Ndipo kuukitsidwa mmanda ndi zoona zotsimikizika, zimene zatsimikizidwa ndi Qur'an, ndi Sunnah, ndiponso mgwirizano wa Asilamu.
Allah wapamwamba adanena kuti: {Kenako ndithu inu pambuyo pa zimenezo mudzamwalira(15)Kenako ndithu inu tsiku la Kiyama mudzaukitsidwa-16} [Al-Muminuna:15-16].
Mtumiki wa Allah - mtendere ndi madalitso a Allah zikhale pa iye -adati: «Anthu adzasonkhanitsidwa pa tsiku lakiyama ali opanda nsapato, ali maliseche, ndiponso osachitidwa mdulidwe»[13]. Adailandira Bukhari ndi Muslim. [13] Nkhaniyi adaitulutsa Muslim, buku la Jannah, pofotokoza za chisangalalo chake ndi anthu ake, mutu wonena za kutha kwa dziko lapansi, ndipo kufotokoza za kusonkhanitsidwa tsiku la Kiyama, nambala yake (2859).
Ndipo Asilamu onse anavomerezana pa kutsimikizika kwake, ndipo izi zikugwirizana ndi nzeru; popeza nzeru zimafuna kuti Allah wapamwamba apangire zolengedwa izi umoyo wina, umene adzawalipiremo pa zomwe adawalamulira kudzera mwa atumiki ake omwe adawatuma, Allah akuyankhula kuti: {Kodi mumaganiza kuti tidakulengani chabe, ndikuti simudzabwelera kwa Ife-115} [Al-Mu'minun:115] Allah adayankhula kwa Mtumiki wake - mtendere ndi madalitso a Allah zikhale pa iye - kuti: {(Ndithudi Allah) amene adakubvumbulutsira iwe buku la Quran (ndi kukulamulira zofalitsa uthenga wake komanso kugwiritsa ntchito malamulo ali m'menemo), adzakubweza iwe kupitanso kumalo obwelera (ku Kiyama)} [Al-Qasas: 85].
Chachiwiri: Kukhulupilira za chiwerengero ndi malipiro: Kapolo adzawerengeredwa ntchito yake, ndipo adzalipidwa pa iyo, ndipo zimenezi zatsimikizidwa ndi Buku, ndi Sunnah, ndiponso mgwirizano wa Asilamu.
Allah wapamwamba akuyankhula kuti: {Ndithu kobwelera kwawo ndi kwa Ife basi(25) Kenako, Ife tidzawerengesera ntchito zawo-26} [Al-Ghashiya:25-26] Allah wapamwamba akuyankhulanso kuti: {Amene wachita chabwino alipidwa zabwino khumi zofanana ndi icho, ndipo amene wachita choipa sadzalipidwa koma chonga icho popanda kuonjezera, ndipo iwo sadzaponderezedwa-160}. [Al-An'am:160]. Allah wapamwamba akuyankhulanso kuti: {Ndipo tsiku la Kiyama tidzaika masikelo achilungamo (kuti ntchito za anthu zidzayezedwe), ndipo palibe munthu amene adzaponderezedwe (popungula zabwino zake kapena kuwonjezera nsambi zake), ngati (ntchito zomwe zidzayezedwe) zidzakhale zochepa kumafanana ndi ka njere ka mbewu, Ife ntchito imeneyo tidzaibweresa (kuiyeza), Ife takwanira kukhala owerengesera (ntchito za akapolo athu) -47} [Al-Anbiya:47].
Nkhani ikuchokera kwa Abdullah mwana wa Umar, Allah asangalasidwe nawo onse awiri, kuti Mneneri - mtendere ndi madalitso a Allah zikhale pa iye ndi pa banja lake - adanena kuti: «Ndithudi Allah adzayandikitsa okhulupilira, ndipo adzaika chitetezo chake pa iye - kutanthauza, chophimba chake - ndikumphimba. Ndipo adzati: "Kodi ukulidziwa tchimo lakuti-lakuti? Kodi ukulidziwa tchimo lakuti-lakuti?" Ndipo iye adzayankha kuti: "Inde, e Mbuye wanga!" Mpaka atamvomerezetsa machimo ake onse, ndipo adzaziona mu mtima mwake kuti waonongeka, Allah adzati: "Ndidawabisa machimo akowo pa dziko lapansi, ndipo lero ndikukhululukira". Kenako adzapatsidwa buku lake la ntchito zabwino. Koma okanira ndi achiphamaso, kudzalengezedwa pamaso pa zolengedwa zonse kuti: Awa ndi amene adamukanira Mbuye wawo, matembelero a Allah ali pa ochita zoipa.»[14] Adailandira Bukhari ndi Muslim. [14] Nkhani ikupezeka mu sahih Bukhar: buku la za kupondereza, mutu wonena za mawu a Allah wolemekezeka (Dziwani kuti matembelero a Allah ali pa achinyengo), nambala yake ndi (2309), komanso mu sahih Muslim: buku la kulapa, mutu wonena za kulandiridwa kwa kulapa kwa wopha munthu, ngakhale atapha kwambiri, nambala yake ndi (2768).
Kudatsimikizidwa kuchokera kwa Mneneri - madalitso ndi mtendere zipite kwa iye - kuti adati: «Munthu amene alingalira kuchita chabwino ndipo n'kuchichita; Allah amamulembera zabwino khumi mpaka kufika pa mazana asanu ndi awiri, mpaka zochulukitsidwa zambiri-mbiri, ndipo munthu amene alingalira kuchita ntchito yoipa ndipo ndikuichita; Allah amamulembera ntchito limodzi lokha»[15]. [15] Idasimbidwa ndi Muslim: Buku la Chikhulupiriro, Mutu: Kapolo akaganiza kuchita chabwino chimalembedwa, ndipo akaganiza kuchita choipa sichilembedwa, Nambala (131).
Ndipo Asilamu onse agwirizana pa zotsimikizira za kuwerengeredwa ndi kulipidwa malipiro a ntchito, ndipo ichi ndicho chofunika munzeru; pakuti Allah wapamwamba adavumbulutsa mabuku, ndikutumiza Atumiki, ndipo adalamula kwa akapolo ake kuvomereza zomwe adabwera nazo, ndi kuchita zomwe zili zoyenera kuchitidwa kuchokera mu zimenezo, ndipo adalamula kumenya nkhondo ndi otsutsana nazo, ndipo adaloleza magazi awo, ndi ana awo, ndi akazi awo, ndi chuma chawo. Pakadapanda kukhala chiwerengero ndi Malipiro, zinthu zoterezi zikadakhala zachabechabe, zimene Mbuye Wanzeru ali woyeretsedwa nazo. Ndipo Allah Wapamwamba walozera ku nkhaniyi ponena kuti: {(Tsiku lotsiriza) tidzawafunsa anthu omwe Atumiki adatumizidwa kwa iwowo (kuti kodi Atumikiwo adawayankha motani), ndipo tidzawafunsa Atumiki (ngati anafalitsa uthenga omwe adalamuridwa kuti afalitse kwa anthu, ndikuti anthu awo adawayankha motani) (6), tidzawauza (anthu onse za ntchito zawo zomwe adagwira pa dziko la pansi) potengera ndi kudzindikira (kwathu, ndithudi Ife timadziwa bwino za ntchito zawo zonse, palibe ntchito yomwe imabisika kwa Ife), sitinali kuti tatalikira) pomwe iwo amagwira ntchitozo nthawi ina iliyonse} [Al-A'raf:6-7].
Chachitatu: Kukhulupilira zoti kuli Minda ya mtendere ndi Moto, ndikuti ndio malo obwerera amuyaya a zolengedwa.
Tsono Jannah ndio malo achisangalalo amene Allah wapamwamba wawakonzera anthu okhulupirira oopa Allah, omwe adakhulupirira mu zomwe Allah adawalamula kuti azikhulupirire, ndipo adali kumvera Allah ndi Mtumiki wake modzipereka kwa Allah, ndikumatsatira Mtumiki wake, m'menemo muli mitundu yosiyanasiyana ya chisangalalo. «Zomwe maso sanayambe aona, komanso makutu sanayambe atamva, komanso sizinayambe zafika m'maganizo a munthu»[16]، Allah wapamwamba akuyankhula kuti: {Ndithudi anthu omwe adakhulupilira Allah ndikumagwira ntchito zabwino, zimenezo ndi zolengedwa zomwe zili zabwino(7).(Tsiku la chiweruzo akalandira) malipiro awo kuchokera kwa Mbuye wawo komwe ndikukalowa minda yaku mtendere (yokongola kwambiri) ya Edeni komwe misinje ukuyenda pansi pake, akakhala kumeneko mpaka kale kale, Allah adzasangalasidwa nawo (ndipo adzalandira ntchito zawo zabwino), nawonso adzasangalasidwe ndi Allah (pa zomwe wakonzera mu mitundu ya ulemelero), malipiro abwinowa akaperekedwa kwa munthu amene amaopa Allah (ndikumapewa machimo) -8}. [Al-Bayyinah:7-8] Allah wapamwamba akuyankhulanso kuti: {Munthu wina aliyense sakudziwa zomwe Allah wasungira anthu okhulupilira zomwe adzakondwere akadzaziona, (mtima wawo ndikudzadza ndi chimwemwe), omwe adzakhale malipiro a ntchito zawo zabwino-17} [Al-Sajdah:17]. [16] Nkhani ikupezeka mu sahih Bukhar, gawo la Tafsiri, mutu wonena za mawu Ake: (Munthu wina aliyense sakudziwa zomwe Allah wasungira anthu wokhulupirira zomwe adzakondwere akadzaziona), nambala yake ndi (4501), komanso mu sahih Muslim, gawo lonena za Jannah ndi kufotokoza za zabwino zake ndi anthu ake, ndipo nambala yake ndi (2824).
Tsono Moto: ndiye nyumba ya chilango imene Allah wapamwamba wakonzera anthu osakhulupirira osalungama, amene adakanira Iye ndi kusamvera Atumiki ake. Mkati mwake muli mitundu ya chilango ndi mazunzo osayerekezeka. Allah wapamwamba adanena kuti: {Ndipo uopeni Moto umene wakonzedwa kwa anthu osakhulupilira-113} [Al-Imran:131] Allah akuyankhulanso kuti: {Ndipo nena (iwe Mtumiki kwa osakhulupilirawo, kuti): "Ichi ndi choonadi chimene chachokera kwa Mbuye wanu. Choncho amene afuna, akhulupilire; ndipo amene afuna kusachikhulupilira asakhulupilire". Ndithu achinyengo tawakonzera Moto, womwe mipanda yake ikawazinga. Ndipo akakapempha chithandizo (chifukwa cha ludzu loopsya lomwe likawapeza), akathandizidwa popatsidwa madzi otentha kwambiri monga madzi a chitsulo chosungunuka, omwe adzasupula nkhope zawo, taona kuipa chakumwa ndi kuipa malo otsamira-29} [Al-Kahf:29]. Allah akuyankhulanso kuti: {Ndithu Allah wawatembelera osakhulupilira ndi kuwakonzera Moto woyaka kwambiri(64), akakhalabe momwemo kosatha. Sadzapeza wothandizira kapena wopulumutsa(65},Tsiku limene nkhope zawo zidzatembenuka mu Moto, adzanena kuti tsoka ilo tikanamvera Allah ndi kumvera Mtumiki-66} [Al-Ahzab:64-66].
Ndipo kukhulupilira za tsiku lomaliza kuli ndi zipatso zolemekezeka, ndipo zina mwa izo ndi :
Choyamba: Kulakalaka kuchita ntchito yomvera, ndikuchilimika pa ntchitoyo; poyembekezera malipilo a tsiku limenelo.
Chachiwiri: Mantha a kuchita tchimo ndi kukondwera nalo; poopa chilango cha tsiku limenelo.
Chachitatu: Kutonthoza wokhulupilira pa zomwe zikumudutsa padziko lapansi kudzera m'zimene akuyembekezera za mtendere wa pa tsiku lomaliza, ndi malipilo ake.
Ndipo anthu osakhulupilira adatsutsa za kuwuka pambuyo pa imfa; ponena kuti zimenezo sizingatheke.
Kunena uku nkwabodza, ndipo bodza lake likuwonetsedwa ndi malamulo a chipembedzo, zowoneka ndi maso, komanso nzeru zabwino.
Pankhani ya Chilamulo, Allah wapamwamba adayankhula kuti: {Amene sadakhulupilire akumadzinamiza kuti sadzaukitsidwa kwa akufa, nena (iwe Mtumiki) si zili choncho, pali Mbuye wanga ndithu mudzaukitsidwa kwa akufa, ndipo mudzauzidwa zimene mumachita (pa dziko lapansi), zimenezo kwa Allah ndi zosavuta (kuzichita)-7} [Al-Taghabun:7] Ndipo Mabuku onse ochokera kumwamba adagwirizana pa zimenezi.
Koma ponena za umboni owoneka ndi maso: Allah adawaonetsa akapolo ake kuukitsidwa kwa akufa pa dziko lino lapansi, ndipo mu Surah ya Al-Baqarah muli zitsanzo zisanu pa nkhaniyi, zomwe ndi izi:
Chitsanzo choyamba: anthu a Mussa, pamene adayankhula kwa Mussah kuti: {...Sitingakukhulupilire iwe mpaka timuone Allah powonekera...} [Al-Baqarah:55] ndipo Allah adawapatsa imfa, kenako nkuwaukitsa, Ndipo pa zimenezi Allah wapamwamba akuyankhula kwa ana a Israel kuti: {Ndipo kumbukiraninso nkhani iyi pamene mudati: E iwe Mussa! Sitingakukhulupilire iwe mpaka timuone Allah masomphenya, ndipo nkokomo wa moto udakugwirani uku inu mukuona. Kenako tinakuwukitsaninso pambuyo pa imfa yanu kuti mukhale othokoza-56} [Al-Baqarah:55-56].
Chitsanzo chachiwiri: Mu nkhani ya munthu wophedwa uja amene ana a Israel adakankhirana, Allah adawalamula kuti azinge ng'ombe kenako n’kumumenya wakufayo ndi chigawo chake; kuti adzuke n’kuwauza amene adamupha, ndipo pa nkhaniyi Allah wapamwamba akuti: {Ndipo (kumbukiraninso nkhani iyi) pamene mudapha munthu, kenako mudakangana ndi kukankhirana za munthuyo (ena ankati uje ndiye wapha, pomwe ena ankati koma uje ndiye wapha). Ndipo Allah atulutsira poyera zimene mudali kubisa. Choncho tinati, mumenyeni ndi gawo lina la iyo,momwemo Allah amaukitsa akufa ndipo akuwonetsani zizindikiro zake kuti mukhale ndi nzeru-73} [Al-Baqarah:72-73].
Fanizo lachitatu: mu nkhani ya anthu omwe adatuluka m'nyumba zawo akuthawa imfa ndipo adali zikwizikwi; ndipo Allah wapamwamba adawapatsa imfa, kenako adawaukitsa, ndipo pa zimenezi Allah wapamwamba adayankhula kuti: {Kodi sudamve nkhani za amene adatuluka m’nyumba zawo ali zikwizikwi kuopa imfa? Ndipo Allah adawauza: "Mwalirani", (ndipo adamwalira chabe popanda chifukwa chilichonse), kenako adawaukitsa (kuti adziwe kuti imfa njosathawika). Ndithudi, Allah Ndimwini kuchita zabwino pa anthu, koma anthu ambiri sathokoza-243} [Al-Baqarah: 243].
Chitsanzo chachinayi: Ndi nkhani ya munthu amene anadutsa pamudzi wakufa, ndipo adaona ngati zosatheka kuti Allah wapamwamba angauukitse; ndipo Allah wapamwamba adamupatsa imfa kwa zaka zana limodzi, kenako n'kumuukitsa, ndipo pa nkhani imeneyi Allah wapamwamba akuti: {Kapena ngati fanizo la uja amene adadutsa pafupi ndi mudzi umene madenga ndi zipupa zake zidaphwasuka (udaferatu) adati: "Kodi Allah adzaukitsa chotani mudzi uwu pambuyo pakufa kwake?" Ndipo Allah adampatsa imfa kwa nthawi yokwana zaka zana limodzi , kenako adamuukitsa namufunsa: "Kodi wakhala nyengo yaitali bwanji?" Adati: "Ndakhala nthawi yatsiku limodzi, kapena theka latsiku". Allah adati: "Koma wakhala zaka zana limodzi, ndipo ona zakudya zako ndi zakumwa zako, sizinaonongeke (sizinavunde). Ndipo yang’ana bulu wako ali mafupa okha okha oyoyoka; ndi kuti ukhale chisonyezo kwa anthu, (ndi chifukwa chake takuukitsa ku imfa). Ndipo yang’ana mafupa (a bulu wako) momwe tingawaukitsire, kenako nkumaaveka minofu. Choncho pamene zidazindikirika kwa iye, (woukitsidwayo), adati: “Ndikudziwa kuti Allah Ngokhoza chilichonse} [Al-Baqarah:259].
Chitsanzo chachisanu: M'nkhani ya Ibrahim bwenzi la Allah - mtendere wa Allah ukhale pa iye -, pamene adapempha Allah wapamwamba kuti amuonetse mmene amaukitsira akufa; pamenepo Allah wapamwamba adamulamula kuti azinge mbalame zinayi, ndi kuzigawa mzidutswa pa mapiri omwe adamuzungulira, kenako aziyitane; ndipo zidutswa zija zidalumikizana china ndi chinzake, ndikubwera kwa Ibrahim mothamanga. Ndipo pa zimenezi Allah wapamwamba akunena kuti: {Ndipo kumbukira pamene Ibrahim adati: "E Mbuye wanga!, Ndionetseni mmene mudzaaukitsire akufa". Allah adati: "Kodi sunakhulupilirebe?" Iye adati: "Iyayi, ndikukhulupilira, koma ndikufuna kuona zimenezo kuti mtima wanga ukhanzikike". (Allah) adati: "Choncho katenge mbalame zinayi; uzisonkhanitse kwa iwe mpaka uyizindikire mbalame iliyonse mmene ilili, (ndipo kenako uziduledule zonsezo zidutswazidutswa ndikuzisakaniza ndi kuzigawa mzigawo zinayi.) Ndipo paphiri lililonse ukaikepo gawo limodzi la zimenezo, ndipo kenako uziitane. Zikudzera zikuthamanga. Ndipo dziwa kuti Allah ndi Mwini mphamvu zoposa, Ngwanzem zakuya"} [Al-Baqarah:260].
Zimenezi ndi zitsanzo zooneka ndi maso ndiponso zoona, zosonyeza kuthekera kwa kuukitsa akufa. Ndipo paja panatchulidwa kale za zozizwitsa zimene Allah adampatsa Issa mwana wa Mariam pa nkhani yodzutsa akufa, ndi kuwatulutsa m'manda mwawo -ndi chilolezo cha Allah-.
Umboni ogwiritsa ntchito nzeru: uli mbali ziwiri:
Chimodzi mwa izi ndi chakuti: Allah ndi Mlengi wa kumwamba ndi pansi, ndi zonse zili m'menemo, amene adazilenga zonsezi pachiyambi. Ndipo amene ali ndi mphamvu zoyambitsa kulenga zolengedwa, sangalephere kuzibwezeretsanso zitafa. Allah wapamwamba akuyankhula kuti: {Ndipo iye ndiamene adayambitsa zolengedwa. Ndipo ndi yemwe adzazibwerezenso kachiwiri, ndipo kuzibwerezako, ndi kosavuta kwa Iye...} [Al-Rum:27]. Allah akuyankhulanso kuti: {Monga tidayamba kulenga zolengedwa poyamba, tidzabwerezanso kuzilenga kachiwiri, ili ndilonjezo lomwe lili pa Ife,ndithu Ife ndi Ochita (zomwe tikunena)} [Al-Anbiya:104]. Ndipo adanena, polamula kuti amuyankhe amene amakanira zakuukitsidwa kwa munthu oti wasanduka mafupa ofumbwa: {Nena (iwe Mtumiki) kuti: "Adzawaukitsa yemwe adawalenga panthawi yoyamba, ndipo Iye Ngodziwa kalengedwe ka mtundu ulionse"-79}. [Yasin:79].
Chachiwiri: Ndi chakuti nthaka imakhala yakufa youma, yopanda mtengo uliwonse wobiriwira; ndipo madzi a mvula akagwera pamwamba pake; imakhala ndi moyo kukhala yobiriwira, n'kumeretsa zomera zamitundu yonse zokongola. Ndipo amene ali okutha kuidzutsa nthakayo pambuyo pa imfa yake, ndiyenso okutha kudzutsa akufa. Allah wapamwamba adati: {Ndipo zina mwa zisonyezo zake (zoposa), ndithu iwe umaona nthaka ili youma; koma tikatsitsa madzi pa iyo imagwedezeka ndi kufufuma; ndithu amene waiukitsa (nthaka itauma), ngoukitsa akufa. iye ndi wamphamvu zoposa pa chilichonse-39} [Fussilat:39] Allah akuyankhulanso kuti: {Ndipo tatsitsa madzi odalitsidwa kuchokera ku mitambo, ndipo kupyolera m’madziwo, tameretsa mmera m’minda ndi mbewu zokololedwa(9) ndi mitengo ya tende yotalika yomwe ili ndi zipatso zoyikidwa bwino(10)kuti ikhale chakudya kwa akapolo, ndipo tapatsa moyo kudera lomwe linali lakufa, momwemo kudzakhala kuukitsidwa-11} [Qāf:9-11].
Ndipo kumaphatikizidwa ku kukhulupilira za tsiku lomaliza: Kukhulupilira zinthu zonse zomwe zimachitika pambuyo pa imfa, monga:
(A) Chiyeso cha m'manda: ndiko kufunsidwa kwa wakufa pambuyo poikidwa kwake m'manda zokhudza Mbuye wake, ndi chipembedzo chake, ndi Mneneri wake; ndipo Allah amawalimbitsa amene adakhulupilira ndi mau a chilimbikitso, ndipo amayankha kuti: Mbuye wanga ndi Allah, chipembedzo changa ndi Chisilamu, ndipo Mneneri wanga ndi Muhammad, madalitso ndi mtendere za Allah zikhale pa iye. Ndipo Allah amawalekelera kusochera anthu odzichitira okha zoipa, choncho wokanira amati: Ha, ha, sindikudziwa, ndipo wachiphamaso kapena okaikira amanena kuti: sindikudziwa, ndimawamva anthu akuyankhula mau ena ake ndiye nanenso ndimayankhula nawo.
(b) Zilango za m'manda ndi mtendere wake: Chilango chimakhala kwa anthu opyola muyezo mwa achiphamaso ndi anthu okanira, Allah wapamwamba adati: {...Ukadakhala kuti waona (iwe Mtumiki) anthu ochita zoipa pomwe akuthatha ndi ululu wa imfa, nawo angelo atatambasula manja awo (powamenya uku akuwauza mwa nkhanza): "Tulutsani moyo wanu nokha; (ife tidzangoutenga mukautulutsamo), tsiku la lero mulipidwa chilango chonyozetsa chifukwa cha zomwe mudali kumunamizira Allah podzinenera bodza (kuti ndi Atumiki ndikuti uthenga wa Allah umabvumbulutsidwa kwa inu monga momwe Allah amabvumbulutsira kwa Atumiki ake), komanso chifukwa chozitukumula kwanu posakhulupilira zizindikiro zake} [Al-An’am:93].
Allah wapamwamba akuyankhula zokhuza anthu omutsatira Farao: {(Pambuyo pa imfa yawo), moto umaonetsedwa kwa iwowo kum'mawa ndi kumadzulo, ndipo tsiku la Kiyama (zizayankhulidwa kwa iwo kuti:) alowetseni otsatira a Faraoh ku zilango zowawa kwambiri, (kamba kokanira kwawo ndikuwatsekereza ena kutsatira choona-46).” [Ghafir:46].
Zinalembedwa mu buku la Sahih Muslim mu nkhani yomwe ikunenedwa ndi Zaid bin Thabit - Allah asangalasidwe naye - amene adanena kuti Mtumiki wa Allah - mtendere ndi madalitso a Allah zikhale pa iye -adanena kuti: «Kukanapanda kuopezera kuti mungasiye kuikana m'manda, ndithu ndikadamupempha Allah kuti akupangitse kumva zilango za m'manda zimene ine ndimamva» Kenako anatembenuka ndi nkhope yake ndipo adati: "«Dzitchinjirizeni mwa mwa Allah ku chilango cha Moto.»" Ophunzira a Mtumiki adanena kuti: "Tikudzitchinjiriza mwa Allah ku chilango chaku Moto". Kenako Mtumiki adanena kuti: "Dzitchinjirizeni mwa Allah ku chilango cha m'manda". Ndipo iwo adati: "Tikudzitchinjiriza mwa Allah ku zilango za m'manda." Kenako Mtumiki adati: «Dzitchinjirizeni mwa Allah ku mayesero owonekera komanso obisika» Ndipo iwo adati: "Tikudzitchinjiriza mwa Allah ku mayesero omwe awonekera komanso abisika." Kenako Mtumiki adati: «Dzitchinjirizeni mwa Allah ku mayesero a Dajjal» Ndipo Iwo adati: "Tikudzitchinjiriza mwa Allah ku mayesero a Dajjal."-[17]. [17] Nkhani ikupezeka mu Swahih Muslim: Buku la Jannah, kufotokoza za chisangalalo chake ndi anthu ake, Mutu wonena za kuonetsedwa kwa wakufa malo ake okhala ku Jannah kapena ku Moto, ndi kutsimikizira chilango cha m'manda ndi kupempha chitetezo kuchokera ku chilangocho, nambala yake (2867).
Ndipo ponena za mtendere wa m'manda: ndi wa anthu okhulupilira omwe adali oyankhula zoona pa chikhulupiliro chawo. Allah wapamwamba akuyankhula kuti: {Ndithu anthu amene adanena kuti: "Mbuye wathu ndi Allah (ndipo tilibe Mbuye wina koma Iye yekha", kenako ndi kumapitiriza kukhala olungama (potsatira malamulo ake, ndikumapewa zomwe adaletsa," amawatsikira Angelo nthawi ya imfa yawo (omwe amakhala akuyankhula kuti": Musaiope (imfa komanso chili chonse chomwe chingabwere pa mbuyo pake,) ndipo musadandaule (ndi zomwe mwasiya pa dziko la pansi, sangalalani zokalowa ku munda wa mtendere womwe mudali kulonjezedwa (pa dziko la pansi chifukwa chokhulupilira kwanu komanso ntchito zanu zabwino-30} [Fussilat:30].
Allah akuyankhulanso kuti: Mmaona bwanji mzimu wa mmodzi wa inu ukafika kummero (panthawi ya imfa)(83) ndipo inu mukuyang'ana pa nthawi imeneyo(84) Ndipo Ife timakhala naye pafupi naye kuposa inu koma simumaona(85). Mmaona bwanji ngati simuli omangidwa(86)Mubwezeretse ngati muli onena zoona(87) Koma ngati ali mmodzi wa omwe ali oyandikitsidwa (kwa Allah)(88)ndiye kuti mpumulo ndi zonunkhira zabwino ndi munda wa chisangalalo (ndizake)-89} [Al-Waqiah:83-89].
Ndipo kuchokera kwa Al-Bara bin Azib, Allah asangalale naye - adanena kuti Mtumiki - mtendere ndi madalitso a Allah zikhale pa iye - adanena zokhuza munthu okhulupilira pamene wayankha Angelo awiri a m’manda mwake: "Amaitama woyitana kuchokera kumwamba kuti: 'Ndithu kapolo wanga wanena zoona, choncho muyalireni zoyala za ku Jannah, ndipo mvekeni zovala za ku Jannah, ndipo mutsegulireni khomo lolowera ku Jannah.' Adati: 'Ndipo kumabwera kwa iye mpweya wake wabwino ndi fungo lake lokoma, ndipo manda ake amakulitsidwa kufikira pamene maso ake amathera kuona.'" Adailandira Ahmad ndi Abu Dawood mu nkhani yaitali[18]. [18] Anaitulutsa Abu Dawood mu buku la Sunnah, mutu okhudza mafunso a m'manda ndi chilango cha m'manda, nambala yake (4753), komanso Ahmad: mu Musnad ya anthu a ku Kufa, nkhani ya Al-Bara bin Azib, nambala yake (18534).
Ndipo lasochera gulu la anthu opotoka, motero adakana chilango cha m’manda ndi chisangalalo chake, ponena kuti zimenezo nzosatheka chifukwa zikutsutsana ndi zenizeni. Iwo adati: “Pakuti ngati mtembo utavundukulidwa m’manda mwake, ungapezeke monga momwe udalili, ndipo mandawo sangasinthe mwa kutanuka kapena kupapatiza.”
Aka ndi kaganizidwe kolakwika potengera ma umboni a chipembedzo ,ma umboni owoneka ndi maso komanso kugwiritsa ntchito nzeru zabwino:
Kumbali ya ma umboni achipembedzo: malemba atchulidwa kale osonyeza kutsimikizika kwa zilango ndi mtendere wa m'manda
Ndipo mu sahih Bukhar, mu nkhani yochokera kwa Ibn Abbas - Allah asangalale nawo onse awiri - adati: "Mtumiki - mtendere ndi madalitso a Allah zikhale pa iyeyo - anatuluka m'minda ina ya ku Madina; ndipo adamva mau a anthu awiri omwe amalangidwa m'manda mwawo" ndipo adatchula nkhani yonse, ndipo m'menemo mukunenedwa kuti: {mmodzi wa iwo sanali kudzitchinjiriza ku mkodzo} Mu kuyankhula kwina: "ku mkodzo wake" (Ndipo kuti winayo anali odanitsa anthu - kuzitape), Ndipo mu kuyankhula kwina kwa Muslim: «Samadziyeretsa ku mkodzo»[19]. [19] Nkhani ikupezeka mu sahih Bukhar: buku la udhu, mutu onena za kutsuka mkodzo, nambala yake ndi (215).
Tsono maumboni owoneka ndi maso: Ndithu munthu yemwe wagona amalota ali pamalo aakulu osangalatsa, akusangalalapo, kapena ali pamalo opapatiza owopsa, akumva kupweteka chifukwa cha malowo, ndipo nthawi zina amadzuka kutulo chifukwa cha zimene walotazo. Ndipo iye ali pabedi lake m'chipinda chake momwe alilimo, ndipo tulo ndi m'bale wa imfa; nchifukwa chake Allah adatcha kuti ndi (imfa), Allah adanena kuti: {Allah ndiye amatenga mizimu pa nthawi ya imfa yake ndipo amatenga mizimu yomwe siidafe panthawi yogona tulo. Ndipo amaigwira mizimu imene wailamula kufa, (osaibwezera ku matupi awo), koma inayo amaitumiza (kumatupi awo, yomwe nthawi yake siidakwane) kufikira nthawi yake (yofera ikwane)} [Al-Zumar:42].
Tsono ma umboni ogwiritsa ntchito nzeru zabwino: ndithu munthu amene wagona tulo amalota ku tulo kwakeko zinthu zoona zomwe zimagwirizana ndi mmene chinthu walotacho chilili, ndipo mwina n'kumuona Mtumiki - mtendere ndi madalitso a Allah zikhale pa iye - m'maonekedwe ake enieni, ndipo amene wamuona m'maonekedwe ake enieniwo; ndiye kuti wamuonadi, koma ngakhale zili choncho, wogonayo amakhala ali m'chipinda chake pogona pake, kutali ndi zimene waonazo, Ngati zimenezi zili zotheka pa zinthu za dziko lino, bwanji sizingatheke pa zinthu za tsiku lomaliza?
Koma ponena za kudalira kwawo pa zonena zawo, zakuti akadavundukulidwa omwalirayo m'manda mwake, akadapezeka monga momwe analili, ndipo mandawo osasintha potambasuka kapena kupanikizika; ndiye yankho la zimenezi lili ndi mbali zambiri, zina mwa izo ndi izi:
Choyamba: sikoyenera kutsutsa zomwe zabwera m’chipembedzo ndi zifukwa zosocheretsa komanso zopanda pake, zomwe ngati wotsutsayo akadalingalira mozama pa zomwe zabwera m'chipembedzo, akadadziwa za kupanda pake kwa zifukwa zosocheretsazi, ndipo pamanenedwa kuti:
Ndipo ndi angati odzudzula mau olondola
Ndipo vuto lake limachokera ku kumvetsetsa kolakwika.
Chachiwiri: kuti zochitika mkati mwa moyo omwe uli pambuyo pomwalira zili mu gulu lazinthu zobisika zomwe sizingadziwike poziona, ndipo zikadakhala kuti ndi zotheka kuzidziwa poziona, phindu lokhulupilira zinthu zobisika pakadakhala palibe, ndipo akadafanana anthu okhulupilira ndi okanira zinthu zobisika pozivomereza.
Chachitatu: kuti chilango ndi chisangalalo, ndi kutambasuka kwa manda ndi kupanikizika kwake; ndithudi womwalirayo yekha ndiye amaziona osati wina aliyense, ndipo izi zili ngati momwe munthu wogona amaonera m'maloto ake kuti ali pamalo opanikizika ndi oopsa, kapena pamalo otambasuka ndi okondweretsa, pamene amene ali pafupi naye saona zimenezo ndiponso samva. Nthawi zina mau a Allah amabvumbulutsidwa kwa Mtumiki -mtendere ndi madalitso a Allah zikhale pa iye - atakhala limodzi ndi ophunzira ake; ndiye Mtumiki amawamva mauwo, koma ophunzira ake samawamva, pena amatheka kumubwelera mngelo Gabriel mu kaonekedwe ka munthu ndikumamuyankhula koma ophunzira ake osamuona mngeloyo komanso osamumva zomwe akuayankhula.
Chachinayi: Ndichakuti kuzindikira kwa zolengedwa nkopelewera pa zomwe Allah wolemekezeka adazipatsa mphamvu kuti zizizindikire, ndipo sizingatheke kuti izo zizindikire chirichonse chopezeka, pakuti thambo zisanu ndi ziwiri, ndi nthaka, ndi zomwe zili mkati mwake zimatamanda Allah, kutamanda kwenikweni, ndipo Allah wapamwamba amawapangitsa kumva amene wawafuna mu zolengedwa zake nthawi zina. Ngakhale zili choncho, kutamanda kumeneko kuli kobisika kwa ife, ndipo pankhani imeneyi, Allah wapamwamba adati: {Zonse za ku mitambo isanu ndi iwiri ndi nthaka ndi za m’menemo, zikulemekeza Iye; ndipo palibe chilichonse koma chikumlememekeza ndi kumtamanda; koma inu simuzindikira kulemekeza kwawo...} [Al-Isra:44]. Chomwechonso a satana ndi ziwanda amayendayenda pa dziko lapansi pobwera ndi kupita, ndipo ziwanda zidabwera kwa Mtumiki wa Allah mtendere ukhale pa iye, ndikumvetsera kuwerenga kwake zili chete, ndikubwerera kwa anthu awo uku zikuwachenjeza. Ngakhale zili choncho, iwo ali obisidwa kwa ife. Ndipo pankhani imeneyi Allah wapamwamba akunena kuti: {E inu ana a Adam! Satana asakusokonezeni monga momwe adawatulutsira makolo anu m’munda wa mtendere ndi kuwavula onse awiri chovala chawo kuti awasonyeze umaliseche wawo, ndithu iye ndi mtundu wake akukuonani pomwe inu simukuwaona, ndithu asatana tawachita kukhala abwenzi a osakhulupilira-27} [Al-A'raf:27]. Ndipo ngati zolengedwa sizingamvetse chinthu chilichonse chopezeka; ndiye sichoyenera kuti zikanire zinthu zotsimikizika za zobisika, ngakhale sizidazimvetse.
*
Kukhulupilira za Chikonzero
Chikonzero: Ndi chikonzero cha Allah wapamwamba pa zolengedwa, malinga ndi kudziwa kwake koyambirira, komanso monga m'mene nzeru zake zidafunira.
Ndipo kukhulupilira za Chikonzero kumatenga mfundo zinayi:
Choyamba: Kukhulupirira kuti Allah wapamwamba amadziwa chinthu chilichonse, zonse mwakamodzi ndi motambasula, kuyambira kalekale mpaka muyaya, kaya ndizokhudzana ndi zochita zake, kapena zochita za akapolo ake.
Chachiwiri: Kukhulupirira kuti ndithu Allah wapamwamba adalemba zimenezo mu ALLAUHILMAHFUUDH (Ubawo otetezedwa), ndipo pa nkhani ziwiri izi Allah wapamwamba adati: {Kodi sukudziwa (iwe Mtumiki) zoti Allah amadziwa zinthu zomwe zili ku mwamba komanso dziko la pansi, (palibe chomwe chimabisika kwa iye mu zomwe zili mkati mwa ziwiri zimenezi,) kudzindikira kwake pa zinthu zimenezi zidalembedwa mu buku (lomwe lasonkhanitsa kena kalikonse,) ndithudi kudziwa zinthu zonsezi ndi zopepuka kwa Allah-70} [Al-Hajj:70].
Mu Sahih Muslim, mu nkhani yomwe ikuchokera kwa Abdullah mwana wa Amr bin Al-As, Allah asangalale nawo awiriwo - adati: "Ndidamumva Mtumiki wa Allah - mtendere ndi madalitso a Allah zipite kwa iye -akunena kuti: «Allah adalemba chikonzero cha zolengedwa zonse, zaka zikwi makumi asanu asanayambe kulenga mitambo ndi nthaka»[20]. [20] Nkhani adaitulutsa Muslim: buku la Qadari, mutu wa mtsutso wa pakati pa Adam ndi Mussa - mtendere ukhale pa awiriwo -, nambala yake (2653).
Chachitatu: Kukhulupirira kuti zolengedwa zonse sizipezeka pokhapokha mu chifuniro cha Allah wapamwamba, kaya zikhale zokhudzana ndi zochita zake, kapena zokhudzana ndi zochita za zolengedwa. Allah wapamwamba adati pa nkhani ya zochita zake: {Ndipo Mbuye wako (iwe Mtumiki) amalenga chomwe wafuna kuchilenga, ndiponso amamusankha (amene wamufuna kuti akhale omvera malamulo ake komanso kumpatsa utumiki)..} [Al-Qasas:68]. Allah adatinso: {...Allah amachita zimene wafuna} [Ibrahim:27]. Allah adatinso: {Iye ndi amene amakulengani mu kaonekedwe kosiyanasiyana muli m'zikuta mwa azimayi anu mmene iyeyo akufunira...} [Al-Imran:6] Ndipo Allah adayankhulanso zokhuza zomwe zimachita zolengedwa kuti: {Allah akadafuna, akadawapatsa mphamvu yokugonjetserani ndipo akadakumenyani...} [Al-Nisa:90] Allah adatinso: {...Ndipo Mbuye wako akadafuna, sakadatha kuchita zimenezi, choncho, asiye ndi bodza lomwe akupekalo}. [Al-An’am:112].
Chachinayi: Kukhulupilira kuti zonse zopezeka ndizolengedwa ndi Allah wapamwamba, zinthu zeni zenizo, mbiri zake, ndi zichitochito zake. Allah wapamwamba adati: {Allah ndiye Mlengi wa chilichonse, (amene amayendesa china chili chonse), ndipo iye ndi amene amayang'anira china chilichonse (chokhuza akapolo ake)-62} [Al-Zumar:62] Allah woyera adanenanso kuti: {...Adalenganso china chilichonse ndipo adachikonza molingana ndi chikonzero chake}. [Al-Furqan:2] Allah akuyankhula zokhuza Mtumiki wake Abraham - mtendere ukhale pa iye - kuti adati kwa anthu ake: {Allah ndi amene adakulengani inu, komanso adalenga ntchito zomwe inu mumagwira-96}. [Al-Safat: 96].
Ndipo kukhulupirira za chikonzero - monga tafotokozera - sizimatsutsana ndi kuti kapolo akhale ndi chifuniro pa zochita zomwe amasankha kuti achite, ndiponso kuthekera pa zimenezo; chifukwa chilamulo komanso zochitika pa moyo wa munthu zikutsindika za zimenezo.
Tsono ku mbali ya chilamuli, Allah akuyankhula zokhudza chifuniro kuti: {...Kwa munthu amene akufuna (kukapulumuka ku zilango za Mbuye wake,) akuyenera kupeza njira yonkera kwa Mbuye wake (yokamupulumusira pogwira ntchito zabwino zomwe zingamukondweretse Mbuye wake)}. [Al-Naba: 39]. Allah adatinso: {...Idzereni minda yanu mbali iliyonse yomwe mungafune...} [Al-Baqarah:223]. Iye adayankhula zokhuzana ndi kuthekera: {Muzimuopa Allah (pochita zomwe adalamulira ndikupewa zomwe adaletsa) mmene mungathere muzimvera ndikulolera (Allah ndi Mtumiki wake)..} [At-Taghabun:16] Allah adatinso: {Allah samalamula munthu kugwira ntchito kupatula yomwe angaikwanitse. Kwa munthu amene angagwire ntchito yabwino adzapasidwa malipiro a ntchito yakeyo (popanda kupunguka chilichonse), ndipo kwa munthu amene angagwire ntchito yoipa adzalipidwanso (motengera ndi mchimo lake)...} [Al-Baqarah:286].
Ndipo ponena za zochitika pa moyo wa munthu: ndithu munthu aliyense amadziwa kuti ali ndi Chifuniro ndi Kuthekera, ndi zimenezi amachita, ndiponso ndi zimenezi amasiya, ndipo amasiyanitsa pakati pa zomwe zimachitika mwa chifuniro chake monga kuyenda, ndi zomwe zimachitika popanda chifuniro chake monga kunjenjemera, koma Chifuniro cha kapolo (munthu) ndi Kuthekera kwake zimachitika mwa Chifuniro cha Allah wapamwamba ndi Mphamvu zake; chifukwa cha mawu a Allah wapamwamba: {Zimenezi ndi zokhuza munthu amene akufuna mwa inu kuyenda njira yowongoka(28)Simungafune (kuwongoka kapena china chilichonse kuti chichitike) kupatula ngati Allah Mbuye wa zolengedwa zonse atafuna-29} [Al-Takwir: 28-29] Ndipo chifukwa chilengedwe chonse ndi cha Allah wapamwamba, palibe chimene chimachitika mu ufumu wake popanda kudziwa kwake ndi chifuniro chake.
Ndipo kukhulupilira za chikonzero, monga tafotokozera, sikumapatsa munthu chifukwa pa zokakamizidwa zomwe adazisiya, kapena pa machimo omwe adachita. Chifukwa cha ichi, kudziyeretsa kwake ndi chikonzerocho nkwachabe pa zifukwa zosiyanasiyana:
Choyamba: mau ake a Allah wapamwamba: {Anthu omuphatikiza Allah ndi zinthu zina adzayankhula (pa tsiku la chiweruzo poikira umboni chifuniro cha Allah ndi chikonzero chake zoti iwo amalondola pomuphatikiza Allah ndi zinthu zina); akadafuna Allah kuti tisamuphatikize iye kapena makolo athu, sitikanamuphatikiza iye ndi zinthu zina, komanso (akadafuna Allah kuti ife tisazichite kukhala zoletsedwa zomwe timati ndi zoletsedwa kuziletsera tokha), sitikanazichita kukhala zoletsedwa. M'mene akuperekera umboni wawo wa bodzawu, sizikusiyana ndi momwe anthu omwe adalipo kale amanenera (powakanira Atumiki awo kuti; akadafuna Allah kuti ife tisawakanire Atumikiwo, nde adapitiriza akukanira Atumiki athu) mpaka pomwe chilango chathu chidawapeza chomwe tidawatumizira, nena (iwe Mtumiki kwa anthu opembedza mafanowo kuti): "Kodi muli ndi umboni woti mungatitulutsire (wosonyeza kuti Allah adasangalasidwa kuti muzimuphatikiza ndi zinthu zina?" Ndithudi inu mumangotsatira maganizo anu, (ndipo ndithu kungoganiza chabe sikuthandiza china chili chonse kuti ndikukhala choona,) inu mwangokhala kuti anthu oti mungokanira (ndikumatsutsa za Allah)-148} [Al-An'am:148]. Akadakhala kuti iwowo ali ndi umboni ovomerezeka okhuza chikonzero cha Allah, ndekuti Allah sakadawapatsa zilango zake.
Chachiwiri: mau a Allah wapamwamba oti: {(Ndidatumiza) Atumiki (kupita kwa zolengedwa zanga kuti) akasangalatse (ndi nkhani ya malipiro anga,) komanso kuti akachenjeze (zolengedwa zanga zokhuza zilango zanga); kuti anthu asadzakhale ndi chowilingula kuti mkukandaula kwa Allah pambuyo poti Atumiki adatumizidwa kwa iwo, Allah ndi wa mphamvu (pa ufumu wake), waluntha (poyendesa zinthu zokhuza akapolo ake)-165} [An-Nisa:165]. Zikadakhala kuti chikonzero cha Allah ndi umboni okwanira kwa anthu ochita zosemphana ndi Allah ndiye kuti siukanachoka potumiza Atumiki; chifukwa kutsutsana kwachitika pambuyo potumiza Atumiki zomwe zidachitika kamba ka chikonzero cha Allah.
Chachitatu: Nkhani yomwe adaisimba Bukhar ndi Muslim -ndipo mau ake akuchokera mu buku la Bukhar- kuchokera kwa Ali bin Abi Talib Allah asangalale naye, kuti Mtumiki, mtendere ndi madalitso a Allah zikhale pa iye adati: «Palibe aliyense mwa inu koma adalembedwa kale malo ake ku Moto kapena ku Janna» Ndipo munthu wina mwa iwo adati: “Kodi tisangodalira, E iwe Mtumiki wa Allah?” Iye adati: “Ayi, gwirani ntchito, pakuti aliyense wapeputsiridwa.” Kenako adawerenga mau oti: {Tsono kwa amene akupereka ndikumapewa zomwe Allah waletsa-5} [Al-Layl:5]. Ndipo mu kuyankhula komwe kuli mu buku la Muslim: «Choncho aliyense amapeputsiridwa kuchita zomwe adalengedwera»[21] Choncho Mtumiki - mtendere ndi madalitso a Allah zikhale pa iye- adalamula za kugwira ntchito, ndipo adaletsa kudalira pa chikonzero cha Allah. [21] Nkhani ikupezeka mu sahih Bukhar: m'buku la Qadar, pa mutu wa "Ndipo lamulo la Allah linali lokonzedweratu", nambala yake ndi (6605), komanso mu sahih Muslim: m'buku la Qadar, pa mutu wa "Mmene munthu amalengedwera m'mimba mwa mayi wake, kulembedwa kwa rizq (za moyo) wake, nthawi yake yakumwalira, zochita zake, ndiponso kukhala kwake wachisoni kapena wachimwemwe", ndipo nambala yake ndi (2647).
Chachinayi: Kuti Allah wapamwamba adalamula munthu ndipo adamuletsa, ndipo sadamulamule kupatula zomwe angakwanitse, Allah akuyankhula kuti: {Muzimuopa Allah (pochita zomwe adalamulira ndikupewa zomwe adaletsa) pogwiritsa ntchito njira yomwe mungakwanitse (potsatira malamulowo), muzimvera ndi kumulola Allah ndi Mtumiki wake...} [At-Taghabun:16] Allah adatinso: {{Allah samalamulira munthu kugwira ntchito kupatula yomwe angakwanitse} [Al-Baqarah:286]. Ndipo zikanakhala kuti munthu amakakamizidwa pa zochita zake, ndiye kuti akanapatsidwa udindo wochita zinthu zomwe sangakwanitse kuzipewa, ndipo zimenezi n'zosalondola. N'chifukwa chake ngati atachita machimo mosadziwa, kapena kuiwala, kapena mokakamizidwa, alibe tchimo; chifukwa iye ndi olekedwa - alibe mulandu.
Chachisanu: ndithu Chikonzero cha Allah wapamwamba ndi chinsinsi chobisika, sichimadziwika pokhapokha pambuyo pochitika kwa cholembedwacho, ndipo khumbo la Kapolo pa zomwe akuchita limatsogolera kuchita kwake; choncho khumbo lake lakuchita silimazikidwa pa kudziwa kwake za Chikonzero cha Allah, pamenepo kuchichita Chikonzero kukhala chifukwa kumachotsedwa; popeza munthu alibe chifukwa pa chinthu chomwe sakuchidziwa.
Chachisanu ndi chimodzi: Ndithu ife timaona munthu akulimbikira pa zinthu zomuyenerera za moyo wake wa dziko lapansi kufikira atazipeza, ndipo samakhota n’kusankha zomwe sizimuyenerera; kenako nkudzitetezera pa kukhota kwakeko ndi chokonzero. Nanga n’chifukwa chiyani amakhota kusiya zomwe zingamupindulitse pa nkhani za chipembedzo chake n’kupita ku zomwe zingamuvulaze, kenako n’kudzitetezera ndi chikonzero? Kodi mkhalidwe wa nkhani ziwirizi si umodzimodzi?
Ndipo nachi chitsanzo chofotokoza zimenezi momveka:
Ngati munthu atakhala ndi njira ziwiri pamaso pake: Yoyamba imathera ku dziko la chipwirikiti chokhachokha: kuphana, kulanda katundu, kuphwanya ulemu, mantha, ndi njala. Ndipo yachiwiri imathera ku dziko la dongosolo lokha-lokha, mtendere okhazikika, moyo wabwino osavuta, ndi kulemekeza miyoyo, ulemu, ndi chuma. Ndiye, angasankhe kutsata njira iti?
Ndithu iye adzatsatira njira yachiwiri, yomwe imamufikitsa ku dziko la dongosolo ndi chitetezo, ndipo n'kosatheka konse kwa munthu aliyense wa nzeru kutsatira njira ya dziko la chipwirikiti ndi mantha, n'kumapereka chifukwa cha chikonzero cha Allah. Nanga nchifukwa chiyani pa nkhani ya tsiku lotsiriza amatsatira njira yopita ku Moto kusiya ya ku Jannah, kenako nkumabweretsa chifukwa cha chikonzero?
Chitsanzo china: timaona wodwala akulamulidwa kumwa mankhwala; ndipo amawamwa, ngakhale mtima wake sukuwafuna, ndipo amaletsedwa kudya chakudya chimene chingamuvulaze; n’kuchisiya, ngakhale mtima wake ukuchifuna; zonsezi n’cholinga chofuna kuchira ndi kupeza bwino, ndipo sizingatheke kuti akane kumwa mankhwala, kapena kudya chakudya chimene chingamuvulaze, ndikupereka chifukwa cha chikonzero cha Allah. Chifukwa chiyani munthu amasiya zimene Allah ndi Mtumiki wake adalamula, kapena kuchita zimene Allah ndi Mtumiki wake adaletsa, kenako n'kumadziteteza chikonzero?
Chachisanu ndi chiwiri: Munthu amene amadzitetezera ndi chikonzero cha Allah pa zokakamizika zomwe wazilephera kuchita, kapena pa machimo omwe wawachita, ngati munthu wina atamulakwira pomulanda chuma chake, kapena kuwononga ulemu wake, ndipo kenako wolakwayo n'kudzitetezera ndi chikonzero cha Allah, n'kunena kuti, "Usandidzudzule pakuti kulakwitsa kwanga kunali mwa chikonzero cha Allah," sangavomereze kudzitetezera kwakeko. Ndiye zitheka bwanji kuti amukane munthu kudzitetezera ndi chikonzero cha Allah pamene wamulakwira Iye, pomwe iye mwini amadzitetezera nacho pomwe waphwanya ufulu wa Allah wapamwamba?!
Zikunenedwa kuti Mtsogoleri wa okhulupilira, Umar mwana wa Khattabi - Allah asangalale naye-, adabweretsedwa kwa iye wakuba amene amayenera kudulidwa dzanja; ndipo adalamula kuti adulidwe dzanja lake. Ndipo wakubayo adati: Dikirani kaye, inu Mtsogoleri wa okhulupilira, pakuti ine ndidangoba mwa chikonzero cha Allah. Kenako Umar adati: Ndipo ifenso tikungodula mwa chikonzero cha Allah.
Kukhulupilira mu chikonzero cha Allah kuli ndi zipatso zolemekezeka, zina mwa izo ndi:
Choyamba: kuyezamira mwa Allah pogwira ntchito, posangoyezamira mu ntchito yakeyo basi; chifukwa choti china chili chonse chimachitika mu chikonzero cha Allah.
Chachiwiri: Kuti munthu asadzitame yekha akakwaniritsa chofuna chake; chifukwa kukwaniritsidwa kwake ndi chisomo chochokera kwa Allah wapamwamba, kudzera m'zimene adazikonza za njira za ubwino ndi kupambana, ndipo kudzitama kwakeko kumamuiwalitsa kuyamika chisomo chimenechi.
Chachitatu: Kudekha, ndi mpumulo wa mu mtima pa zimene zikumuchitikira kuchokera ku chikonzero cha Allah wapamwamba; choncho sakhala ndi nkhawa chifukwa chotaya chinthu chokondedwa, kapena kuchitika kwa chinthu chosakondedwa; pakuti zimenezo zili m'chikonzero cha Allah amene ali ndi ufumu wakumwamba ndi dziko lapansi, ndipo nzochitika ndithu. Ndipo pa zimenezi Allah wapamwamba akunena kuti: {Silidapezeke vuto pa dzulo lapansi kapena mwa inu anthu kupatula kuti linasindikizidwa m'buku (Allauhul mahfuudh) tisadalilenge (vutolo.) Ndithu zimenezo kwa Allah ndizofewa(22). Zonsezi zili chonchi ndi cholinga choti musakhumudwe (inu anthu) pa zinthu zomwe zakudutsani, komanso kuti musanyade ndi mtendere omwe akupatsani (kunyada kozitukumula), ndithudi Allah samamukonda munthu wina aliyense ozikweza ndi kuzimva) pa maso pa anthu kamba ka zomwe Allah wampatsa-23} [Al-Hadid:22-23] Mtumiki wa Allah - mtendere ndi madalitso a Allah zikhale pa iye-akuyankhula kuti: «Zodabwitsa za nkhani ya okhulupirira, ndithu zochita zake zonse ndi zabwino, ndipo zimenezi sizipezeka kwa aliyense koma kwa okhulupilira; ngati zabwino zitamuchitikira, amamuyamika Allah ndipo zimakhala zabwino kwa iye, ndipo ngati masautso atamugwera, amapilira, ndipo zimakhala zabwino kwa iye»[22]. [22] Nkhani ikupezeka sahih Muslim: buku la za kupewa za mdziko ndi zofewetsa Mtima, mutu wa nkhani oti zochita za okhulupilira zonse zimakhala zabwino, nambala yake (2999).
Ndipo padasokera magulu awiri pa nkhani ya Chikonzero:
Limodzi mwa iwo ndi: a-Jabriyyah amene adanena kuti: Kapolo amakakamizidwa pa zochita zake, ndipo alibe chisankho kapena mphamvu pazimenezo.
Lachiwiri: ndi a Qadariyyah amene adanena kuti: Ndithu Kapolo ali odziimira payekha pa zochita zake mu chifuniro ndi mphamvu, ndipo palibe ku chifuniro cha Allah wapamwamba ndi mphamvu zake chotsatira chilichonse pa izo.
Kuliyankha gulu loyamba la (Al-Jabriyyah) potsatira malamulo a Chisilamu ndi zochitika za pa moyo:
Kudzera m'malamulo, Allah wapamwamba adatsimikizira zoti Kapolo amakhala ndi Khumbo komanso chifuniro, ndipo adalumikiza ntchito kwa iye, Allah adayankhula kuti: {...Ena mwa inu pali akufuna zopeza za dziko la pansi, nde pali ena mwa inu amene akufuna malipiro a moyo omwe ukubwera..} [Al-Imran:152], Allah akuyankhulanso kuti: {Nena (iwe Mtumiki): zomwe ndakubweretserani inu ndi zinthu zoona, ndipo ndi zochokera kwa Mbuye wanu (osati zochokera kwa ine), kwa amene akufuna mwa inu kuti akhulupilire choonachi, achite choncho, (ndipo adzasangalasidwe ndi malipiro ake), ndipo kwa amene akufuna kuchikanira choona, ateronso, (ndipo sadzasangalasidwa ndi zilango zomwe zikumuyembekezera), ndithu ife tawakonzera anthu okanira Moto (waukulu) omwe ukawazungulire ndi mpanda wake (kotero kuti sadzatha kuthawamo).....} [Al-Kahf: 29], Allah akuyankhulanso kuti: {Munthu amene angagwire ntchito ya bwino, phindu la ntchito yake yabwinoyo limabwelera kwa iye mwini, kwa munthu amene angagwire ntchito yoipa, zoipa za ntchito yakeyo zizabwelera kwa iye mwini, ndipo Mbuye wako - iwe Mtumiki - sali opondereza akapolo ake, (sadzawapungulira malipiro a zabwino zawo,komanso sadzawaonjezera machimo awo)-46} [Fusilat:46].
Kutengera pa zochitika pa moyo: ndithu munthu aliyense amadziwa kusiyana pakati pa zochita zake zachisankho zomwe amazichita mwa chifuniro chake: monga kudya, kumwa, kugulitsa, ndi kugula, ndi pakati pa zomwe zimamuchitikira popanda chifuniro chake: monga kunjenjemera chifukwa cha malungo, ndi kugwa kuchokera pa denga. Choncho pa zoyambazi iye ndi wochita mwa chisankho chake ndi chifuniro chake, popanda kukakamizidwa, ndipo pa zachiwirizi iye si wosankha, komanso sanali wofuna zimene zamuchitikirazo.
Ndipo kulitsutsa gulu lachiwiri (Qadariyyah) pogwiritsa ntchito malamulo a Allah ndi nzeru:
Kudzera mu malamulo a chisilamu: ndithudi Allah wapamwamba ndi Mlengi wa chilichonse, ndipo chilichonse chimachitika ndi kufuna kwake, ndipo Allah wapamwamba adafotokoza m’buku lake kuti zochita za akapolo ake zimachitika ndi kufuna kwake, choncho Allah wapamwamba adati: {...Akadafuna Allah kuti anthu omwe adabwera pambuyo pa Atumiki asamenyane sakadamenyana pambuyo powabwelera maumboni owonekera ndikumveka bwino, koma iwo adasemphana ndiye adagawikana, ena mwa iwo adakhulupilira mwa Allah, ndipo ena adakanira mwa Allah, akadafuna Allah kuti asamenyane sakadamenyana, koma kuti Allah amachita zomwe wafuna} [Al-Baqarah:253] Allah wapamwamba akuyankhulanso kuti: {Tikadafuna tikadampatsa munthu wina aliyense chiwongoko chake, koma ndi zoyenera kwa ine kukwaniritsa mau anga (omwe ali ndi nzeru komanso a chilungamo) oti: "Ndikadzadzitsa Gahena (pa tsiku la chiweruzo ndi magulu awiri): anthu ndi ziwanda onse pamodzi, (chifukwa chosankha kwawo njira yokanira ndi kusokera kusiya njira ya chikhulupiliro ndi yowongoka)-13} [Al-Sajdah:13].
Tsono potengera mzelu: Ndithudi chilengedwe chonse ndi cha Allah wapamwamba, ndipo munthu ali mbali ya chilengedwechi; choncho iye ndi kapolo wa Allah wapamwamba, ndipo sizingatheke kwa kapolo kuyendetsa zinthu mu ufumu wa Mfumu yake popanda chilolezo chake ndi chifuniro chake.
*
Zolinga za Chikhulupiliro cha chisilamu
Liwu loti Cholinga (m'chiyankhulo): limakhala ndi matanthauzo angapo, mwa iwo: (Chinthu chimene chimaikidwa kuti chilunjikidwe, ndi chinthu chilichonse chokhumbidwa)
Zolinga za Chikhulupiliro cha Chisilamu: Ndizo zokhumba zake, ndi zolinga zake zolemekezeka, zomwe zimapezeka pogwiritsitsa chikhulupilirocho, ndipo ndi zambiri zosiyanasiyana, zina mwa zolingazo ndi:
Choyamba: Kumuyeretsera Allah yekha wapamwba cholinga ndi mapemphero, chifukwa Iye ndiye Mlengi, alibe wothandizana naye, choncho n'koyenera kuti cholinga ndi mapemphero zikhale kwa Iye yekha.
Chachiwiri: Kumasula nzeru ndi maganizo ku chisokonezo chopanda dongosolo chomwe chimabwera chifukwa chakusowa kwa chikhulupiliro ichi mu mtima; chifukwa amene mtima mwake mulibe chikhulupilirochi, ndiye kuti iye mwina mtima wake ulibe chikhulupiliro chilichonse ndipo amapembedza zinthu zakuthupi zokhazokha, kapenanso amakhala wosokonezeka m'kusokera kwa zikhulupiliro zabodza.
Chachitatu: Mpumulo wa mumtima ndi wa m'maganizo, choncho palibe nkhawa mumtima ndiponso palibe chisokonezo m'maganizo; chifukwa chikhulupiliro ichi chimalumikiza munthu wokhulupilira ndi Mlengi wake; ndipo amakhutitsidwa naye monga Mbuye Woyendetsa zinthu, ndiponso Wolamulira Wopereka malamulo; choncho mtima wake umakhazikika ndi chikonzero chake, ndipo mtima wake umalandira mokondwa Chisilamu; ndipo safuna china chilichonse m'malo mwake.
Chachinayi: Kukhala ndi cholinga ndi zochita zolungama popembedza Allah wapamwamba, kapena pochita zochitachita ndi zolengedwa; chifukwa chimodzi mwa maziko ake ndi kukhulupilira mwa Atumiki, chomwe chimaphatikizapo kutsatira njira yawo yolungama m'cholinga ndi m'zochita.
Chachisanu: kukhala otsimikiza ndi wa khama pa zinthu, m'njira yoti saphonya mpata uliwonse wochita ntchito yabwino koma amaugwiritsa ntchito; poyembekezera mphotho, ndipo saona malo a uchimo koma amawapatuka; poopa chilango; chifukwa chimodzi mwa maziko ake ndi kukhulupirira za kuuka kwa akufa, ndi za malipiro a ntchito.
Allah wapamwamba akuyankhula kuti: {Munthu wina aliyense (amene angagwire ntchito yomvera malamulo a Allah kapena kunyoza malamulo a Allah), ali ndi malo ake (omwe akafikire kwa Allah ngati malipiro) pa ntchito yomwe adali kugwira, ndipo Mbuye wako (iwe Mtumiki) samaiwala ntchito yomwe (akapolo ake) amagwira-132} [Al-An'am:132] Ndipo adalimbikitsa Mneneri -madalitso ndi mtendere zipite kwa iye - pa cholinga ichi mu mau ake akuti: “Okhulupilira wamphamvu ndiwabwino koposa komanso ndiokondedwa kwambiri pa maso pa Allah kuposa okhulupilira ofowoka ndipo onsewo ali ndi ubwino. Uziikira mtima pa zomwe zingakuthandize, ndipo funa thandizo kwa Allah pa zochita zako, ndiponso usamafooke; ngati chitakupeza chinthu chowawa usamayankhule mau oti: ndikanakhala kuti ndachita tere, bwenzi zitachitika motere motere,’ koma uzinene kuti umu ndi momwe Allah adakonzera ndipo zomwe adafuna kuti achite wachita; chifukwa choti mau onena kuti (zikanatere) amatsegula ntchito za Satana.” Nkhani idalandiridwa ndi Muslim (23). [23] Nkhani ikupezeka mu sahih Muslim: buku la Qadar, mutu wa lamulo lokhala a mphamvu, kusiya kufooka, kupempha chithandizo kwa Allah, ndi kusiya mmanja mwa Allah zonse zomwe adakonza kuti zidzachitika, nambala yake (2664).
Cha Chisanu ndi Chimodzi: kukhazikitsa gulu la mphamvu la Asilamu, limene limapereka nsembe zonse zotheka pokhazikitsa chipembedzo chake ndi kulimbikitsa mizati yake, posasamala mavuto amene angakumane nawo pochita zimenezo. Ndipo pankhaniyi Allah wapamwamba akuyankhula kuti: {Ndithu anthu amene ali okhulupilira eni eni ndi anthu amene akhulupilira mwa Allah ndi Mtumiki wake, kenako sanasakanize chikhulupiliro chawo ndi chikaiko chilichonse, ndipo amamenya nkhondo ndi chums chaos komanso ndi iwo eni (popita ku nkhondo) pa njira ya Allah, iwo ndi amene ali oyankhula zoona (pa chikhulupiliro chawo)-15} [Al-Hujurat:15].
Chachisanu ndi chiwiri: Kufikira ku chisangalalo cha padziko lapansi ndi tsiku lomaliza, pokonza munthu aliyense payekha ndi magulu onse a anthu, ndiponso kupeza malipiro ndi zinthu zolemekezeka. Ndipo pa nkhaniyi, Allah wapamwamba akuti: {Amene akuchita zabwino wamwamuna kapena wamkazi uku ali okhulupilira timukhazika ndi moyo wabwino pano pa dziko, ndi tsiku la chiweruzo tidzawalipira powapatsa malipiro abwino kwambiri kamba ka ntchito yabwino yomwe adali kugwira-97}. [Al-Nahl:97].
Izi ndi zina mwa zolinga za Chikhulupiliro cha chisilamu, tikupempha Allah wapamwamba kuti atikwaniritsire ife, ndi kwa Asilamu onse; ndithu Iye ndi owolowa manja, olemekezeka. Ndipo kuyamikidwa konse ndi kwa Allah, Mbuye wa zolengedwa zonse.
Mtendere ndi madalitso a Allah zikhale pa Mtumiki wathu Muhammad, akubanja kwake, ndi ophunzira ake onse.
Latha kulembedwa ndi mwini wake olemba bukuli.
Muhammad Al-Salih Al-Uthaymeen
Related books
All books
Njira zothandiza za moyo wachimwemwe62 languagesNjira zothandiza za moyo wachimwemwe
Buku lofotokoza za njira zothandizira kukhala umoyo wa chimwemwe lolembedwa ndi Sheikh Abdul-Rahman bin Nasir as-Sa'die, limafotokoza mozama njira zobweresera chisangalalo chenicheni kuchokera pa mawonedwe a chikhulupiliro chozama; ndipo limatsogolera owerenga ku bata la mtima kudzera mu chikhulupiliro ndi ntchito zabwino, kukumbukira Mulungu, kukhutira, kusinkhasinkha za madalitso, kuchita ubwino, kuyezamira mwa Mulungu, kuleza mtima, ndi kuzindikira moyenera kufunika kwa zinthu. Mu kalembedwe kokongola, limayika pamaso panu kalozera wa moyo wamtendere, wolinganizika, komanso wosangalala…
CHIKAKAMIZO CHOGWIRITSA NTCHITO SUNNA ZA MTUMIKI(SAW)NDIKUKANIRA KWA MUNTHU YEMWE ANGAZIKANE SUNNAZO.23 languagesCHIKAKAMIZO CHOGWIRITSA NTCHITO SUNNA ZA MTUMIKI(SAW)NDIKUKANIRA KWA MUNTHU YEMWE ANGAZIKANE SUNNAZO.
WOLEMBA BUKU: ABDUL AZIZ BIN ABDUL ALLAH BIN BAZ(ALLAH AWACHITIRE CHISONI). M'dzina la Mulungu ,Wachifundo Chambiri ,Wachisoni Chosatha. MAU OYAMBA Kuyamikidwa konse ndikwa Mulungu, mbuye wa zolengedwa zonse, ndipo mathero abwino pa chinthu chilichonse amakhala kwa anthu oopa Mulungu, mtendere ndi madalitso a Mulungu zikhale pa kapolo komanso mtumiki wake,mneneri wathu Muhammad; amene anatumizidwa kuti akhale ozichitira chisoni zolengedwa zonse,komanso mtendere ukhale kwa anthu aku banja kwake,ophunzira ake anthu amene anatenga uthenga ochokera mu buku la mbuye wawo pamodzi ndi…
Ndani adandilenga? Nanga chifukwa chiyani?75 languagesNdani adandilenga? Nanga chifukwa chiyani?
Cholengedwa Chili chonse chimasonyeza kupezeka kwa Mlengi. Ndani adalenga kumwamba ndi dziko la pansi ndi zolengedwa zikuluzikulu zomwe zili mkati mwa ziwirizi zomwe sizimadziwika? Kodi ndi ndani adaika ndondomeko yokuya ndi yolongosoka bwino yakayendedwe ka zinthu kumwamba ndi dziko lapansi? Kodi ndani amene adalenga munthu ndikumupatsa makutu, maso, ndi nzeru? ndikumpatsa kuthekera kophunzira ndikudziwa zoona? Kodi mungafotokoze bwanji ndondomeko yodzama ndi yokuya ya momwe Mulungu adaikira ziwalo zapa thupi lako komanso ziwalo za zinthu za moyo? ndani adalenga zimenezo? Kodi dziko…
Zina mwa zizindikiro za umodzi wa Mulungu(Tauhid).12 languagesZina mwa zizindikiro za umodzi wa Mulungu(Tauhid).
M’dzina la Mulungu, Wachifundo Chambiri, Wachisoni. Kuyamikidwa konse ndi kwa Mulungu, Mbuye wa zolengedwa zonse, ndipo mathero abwino akakhala kwa anthu owopa Mulungu, ndipo ine ndikuikira umboni kuti palibe Mulungu opembedzedwa mwachoonadi koma Mulungu m'modzi yekha, opanda othandizana naye,ndipo ndikuikiranso umboni kuti Muhammad ndi kapolo ndi Mtumiki wake,mtendere ndi madalitso a Mulungu zikhale pa iye, aku banja kwake ndi ophunzira ake onse, pambuyo pa mau amenewa: Kukhulupilira za umodzi wa Mulungu ndi chiyambi ndi mathero a chipembedzo, ntchito zobisika ndi zoonekera zonse zagona…