الشهادتين
Ngati ukufuna kulowa mu chipembedzo cha Chisilamu,ukuyenera kuyankhula mau oikira umboni awa momveka bwino,komanso umvetsetse matanthauzo ake ndikuwakhulupilira matanthauzowo: Ndikuikira umboni zoti palibe Mulungu oyenera kupembedzedwa mwa choonadi koma Mulungu m'modzi yekha(mau amenewa amatanthauza kuti palibe wina aliyense amene akuyenera kupembedzedwa koma Mulungu m'modzi yekha). Ndikuikiranso umboni kuti Muhammad ndi Mtumiki wa Mulungu, ndikutinso Yesu (Issah) mwana wa Mariya ndi kapolo wa Mulungu komanso Mtumiki wake. Ndikuikira umboni kuti palibe Mulungu oyenera kupembedzedwa mwa…
Ngati ukufuna kulowa mu chipembedzo cha Chisilamu,ukuyenera kuyankhula mau oikira umboni awa momveka bwino,komanso umvetsetse matanthauzo ake ndikuwakhulupilira matanthauzowo: Ndikuikira umboni zoti palibe Mulungu oyenera kupembedzedwa mwa choonadi koma Mulungu m'modzi yekha(mau amenewa amatanthauza kuti palibe wina aliyense amene akuyenera kupembedzedwa koma Mulungu m'modzi yekha). Ndikuikiranso umboni kuti Muhammad ndi Mtumiki wa Mulungu, ndikutinso Yesu (Issah) mwana wa Mariya ndi kapolo wa Mulungu komanso Mtumiki wake.
Ndikuikira umboni kuti palibe Mulungu oyenera kupembedzedwa mwa choonadi koma Mulungu m'modzi yekha,ndikuikiranso umboni kuti Muhammad ndi Mtumiki wa Mulungu.