Mtumiki wa Chisilamu Muhammad - Allah amuchitire chisoni ndi kumpatsa mtendere.
Buku lotchedwa "Mtumiki wa Chisilamu Muhammad- Allah amuchitire chisoni ndi kumpatsa mtendere", likulongosola za moyo wa Mtumiki Muhammad- Allah amuchitire chisoni ndi kumpatsa mtendere- kuyambira fuko lake, kakulidwe kake kufikira kukwatira kwake, ndi chiyambi cha chibvumbulutso ndikutsika kwa uthenga wake otsiriza, ndiponso likufotokoza za zizindikiro za utumiki ndi zosonyeza kuyankhula kwake zoona kuti iye ndi Mtumiki wa Allah, komanso likulongosola za malamulo amene anabwera nawo ndikulongosola za ntchito yake yomwe ndi kutetedza ma ufulu a munthu ndi ulemelero wake, komanso bukuli…
This PDF is generated automatically from the book's text; its layout may differ from the printed edition.
Mtumiki wa Chisilamu Muhammad - Allah amuchitire chisoni ndi kumpatsa mtendere-.
Komiti yoona za maphunziro moyang'aniridwa ndi bungwe loyendetsa za chipembedzo pa mzikiti olemekezeka waku Makkah ndi mzikiti wa Mtumiki.
Mu dzina la Allah Wachifundo chambiri Wachisoni chosatha Mbiri ya chidule ya mtumiki wa Chisilamu Muhammad ﷺ, ndipo nkatikati mwa mbiri yake ndikulongosola za dzina lake, fuko lake, malo amene anabadwila komanso ndi ma banja ake, chivumbulutso chake chomwe anabwela nacho, kuyitanila kwake ku zinthu zomwe anabwela nazo, zizindikilo za utumiki wake, malomulo ake komanso ndikutambasula za anthu amene ankasutsana naye iye .
1-Dzina lake, fuko lake komanso ndi malo amene anabadwira ndi kukulira
Mtumiki wa Chisilamu ndi Muhammad mwana wa Abdullah, mwana wa Abdul Mutwalib, mwana wa Haashim, mwana wa fuko la Ismael iye ndi mwana wa Ibraheem mtendere ukhale kwa iye.
Mtumiki wa Allah Ibraheem anachoka ku Shami kupita ku Makkah, anali ndi nkazi wake Haajira ndi mwana wake Ismael, panthawiyo Ismael ali mwana wa mchikuta ndiye anawasiya ku Makkah pachilamulo cha Allah, pamene Ismael anasanduka mnyamata Ibraheem anabwela ku Makkah ndipo anamanga Kaba nyumba yolemekezeka iye pamozi ndi mwana wake uja Ismael, ndipo anthu anachuluka oyizungulira nyumbayi ndipo Makkah inasandula kopita anthu kukapanga mapephero kwa Allah mwini zolengedwa zonse amene afuna kukapanga hajj. Ndipo anthu anapitilira kupanga mapephero amenewa mu omozi wa Allah pa chipembezo chimenechi cha Ibraheem mpaka zaka zaka
Kenako anthu anasintha makhalidwe ndipo anasiya kutsatila njira ya Ibraheem, ndiye anasanduka ma arabs kukhala ngati wina aliyense wa madela ena a padziko lapasi, ndipo unawonekela mkhailidwe opembeza mafano, kukwilira ana, kuwapondeleza azimayi, kunama poikila umboni, kumwa mowa, chiwelewere, kudya chuma chamasiye, kutenga katapila....
Pa malo amenewa komanso ndi khalidwe lake limeneli ndipamene anabadwa mtumiki wa Chisilamu Muhammad mwana wa Abdullah kuchokela ku fuko la Ismael mwana wa Ibraheem mtendele upite kwa iye, mu chaka cha 571. Bambo ake anamwalira iye asanabadwe, ndipo mayi ake anamwalira chaka cha 6, ndiye kenako anamulela amalume ake, ndipo anali wa masiye komanso waumphawi, ndipo amadya kuchokela mu ntchito za manja ake.
2-Banja lake lodalitsika ndi mzimayi wodala.
Pamene dzaka zake zidakwana 25, anakwatila mzimayi olemekezeka mwa azimayi apa Makkah amene ali Khadija mwana wa Khuwailidi Allah asangalale naye, ndipo anapatsidwa mwayi wa ana atsikana anayi ndi ana achimuna awiri, ndipo ana onse achimuna anamwalira ali achichepere, ndipo khalidwe lake kwa mkazi wake ndi banja lake linali labwino, loleza mtima ndilachikondi, pachimenecho anamukonda mkazi wake kwambiri ndipo iye nayenso anabwezela kumukonda Khadija ndipo sanamuyiwale ngakhale pambuyo poti wamwalira ankazinga mbuzi ndikuyigawa kwa azinzake a Khadija powalemekeza ndikusunga chikondi Khadija pomuchitila zabwino
3-Chiyambi cha chibvumbulutso
Mtumiki ﷺ anali ndimakhalidwe abwino kuyambila chimulengeleni Allah, ndipo anthu ake ankamutcha kuti oyankhula zoona komanso wokhulupirika kasungitsidwa zinthu, komanso ankagwilira limodzi ntchito zikulu-zikulu ndi anthu, komanso amanyansidwa ndi khalidwe la anthu lopembeza ma fano, ndipo samapanga nawo zimenezo.
Pa nthawi yomwe anakwanitsa dzaka 40 ali ku Makkah Allah anamusankha kukhala Mtumiki, ndipo anamubwelera mngelo Jibriel mtendere upite kwa iye anamubwelera ndi surat yoyamba mu Qur'an amene ali mawu a Allah woti :
Adalenga munthu kuchokera ku magazi owundana(2)
Wamuphunzitsa munthu zinthu zomwe sadali kudzidziwa(5)).
Kenako Mtumiki ﷺ anabwelera kwa mkazi wake amene ali Khadija Allah asangalale naye ali ndi mantha Mtumiki mu mtima mwake, ndiye anamulongosolera nkhani ija yokhuzana ndi kutsika kwa chivumbulutso, ndiye Khadija anamukhazikitsa mtima pansi, kenako Khadija anamutengera Mtumiki ﷺ kwa mwana wa amalume ake amene anali Waraqa mwana wa Nufair ndipo anali mkhiristu woti amatha kuwelenga baibulo, ndiye Khadija adanena kwa Nufair kuti: E iwe mwana wa amalume! Tanvani zomwe akuyankhula mwana wa m'bale wako uyu. Ndiye Waraqa anafunsa kuti: Kodi iwe mwana wa m'bale wanga ukuwona chani? Kenako Mtumiki ﷺ anafotokoza nkhani yonse pa zomwe adawona. Ndiye Waraqa ananena kuti:
Ameneyu ndi mngelo amene anatumizidwanso kwa Mussah. Koma ndikudandaula chifukwa cha ukalamba, ndikudandaula zikanakhala kuti ndizakhalapo pamene anthu ako azidzakuthamangitsa. Ndiye Mtumiki ﷺ anati: Kodi anthu azandithamangitsa? Waraqa anati: Inde, palibe amene anabwela ndi zangati zomwe wabwela nazo iwe anthu ake ndikusamuda ayi, ndipo likadandipeza tsiku lakolo ndikadakuthandiza mwamphamvu .[2]
Ali ku Makkah Qur'an inkatsika mondondozana ndipo imatsika podusila kwa Jibriel mtendere wochokera kwa Allah mwini zolengedwa zonse upite kwa iye, monganso mmene ankabweletsera malamulo otambasula bwino awuthenga wa chivumbulutso.
Ndiye anali akuwaitanila anthu ake (ma Quraish) ku chipembezo cha Chisilamu, koma iwo anamuda ndi kukangana naye, ndipo kenako anamuwuza kuti asiye kuyitanila mwa Allah ampatsa ufumu ndi chuma, koma Mtumiki ﷺ anakana zonsezo, ndipo iye anamunenera zinthu ngati mmene anthu akale ankawanenera atumiki awo kuti mfiti, wabodza, wopeka zinthu. Ndipo anaupanga umoyo wake kukhala othina, komanso anampatsa zopweteka pathupi lake lolemekezeka ndi kwavutitsa omutsatila akenso.
Panthawi yomwe Mtumiki ﷺ anali ku Makkah ankaitanila anthu kwa Allah maka maka nthawi ya Hajj komanso ndi nthawi ya misika ya arab. Amakumana ndi anthu mmenemo ndikumawalongosolera za Chisilam. Ndipo sanafune zinthu za padziko, kapena udindo ayi, ndipo sanaope lupanga, analibe udindo ngakhale ufumu. Ndipo kumayambiliro kwa kuitanila kwakwe anawauza anthu kuti abweletse Qur'an yofanana ndi yomwe iye wabweletsa. Ndipo anapitiliza kulimbana ndi anthu amene ankamutsutsa. Ndiye anakhulupilira amene anakhulupilira mwa maswahaba ake Allah asangalale nawo onse.
Panthawi imene anali ku Makkah Mtumiki Allah anamulemekeza ndi chizindikilo chachikulu kwambiri umene uli ulendo omwe anayenda kupita ku Baitil Maqdasi kenako ananyamuka wa kumwamba. Ndipo zomwe zili zodziwika ndizoti Allah anamunyamula kupita ku mwamba ngati m'mene anamunyulira Iliyas ndi Issah mtendere ukhale kwaiwo ngati mmene zinafotokozedwera kwa asilamu ndi achrisitu.
Pamene Mtumiki ﷺ anali kumwambako analandila lamulo la swala. Ndipo imeneyo ndiswala yomwe lero lino asilamu amapephera kasanu pa tsiku. Komanso ali ku Makkah kunachitika chinthu chachikulu kumene kuli kugawikana kwa mwezi mpkana anthu opembeza mafano anawona nawo zimenezi.
Anthu okanila ochokela mwa ma Quraish anayesetsa njira zosiyana siyana kuti alimbane ndi Mtumiki ﷺ kuwaletsa anthu kuti asatsatile komanso kuwathamangitsa kuti asayandikile kunvela zokamba za Mtumiki ﷺ, ndi kumampanga kuti abweletse maumboni kuti iye ndi mtumikidi wa Allah ndi kumawapempha ayuda kuti awanthandize ndi maumboni omutsutsila Mtumiki ﷺ komanso kuwaletsa anthu kuti asafike kwa iye.
Panthawi imene anthu okanila mwa Allah ochokela mwa maquraish anapitiliza kumuvutitsa Mtumiki ﷺ ndi anthu okhulupilira, anawalamula kuti asamukile ku Habasha, ndipo anawawuza kuti kumeneko kuli mfumu yachilungamo yomwe palibe yemwe amapondelezedwa pamatso pake. Ndipo anasamuka magulu okwanila awiri kupita ku Habasha pamene maswahaba anafika ku Habasha anaidziwitsa mfumu ija za Chisilamu chomwe chinabwela ndi Mtumiki ﷺ ndipo analowa Chisilamu, ndipo anati: Ndithu ndikulumbila Allah! Zomwe zabwela ndi Muhammad ndi za Mussah zachokela malo amodzi. Kenako mavuto anayamba kubwela mondondozana kuchokera kwambiri anthu ake omuvutitsa iye ndi ophunzira ake.
Mwa anthu amene analowa Chisilamu nthawi ya Hajj ndikagulu kamene kanabwela kuchokela ku Madina ndiye anapanga malonjezo ndi Mtumiki ﷺ kuti azamuteteza ngati atasamukila ku Madina kumene panthawiyo kunkatchedwa kuti Yathribu. Ndiye Mtumiki ﷺ anawalamula amene anatsala ku Makkah kuti asamukile ku Madina ndipo anasamukila, ndiye Chisilamu chinafalikila ku Madina mpakana sikunatsale nyumba yomwe Chisilamu sichinalowemo
Pambuyo poti wakhala mu Makkah dzaka khumi ndi zitatu akuyitanila kwa Allah kenako Allah anamulamula zosamuka kupita ku Madina ndipo anasamuka, ndipo anakapitiliza kuyitanila, nawo malamulo anali akupitiliza kutsika lamulo pambuyo palamulo. Ndiye kenako anayamba kutumiza mauthenga kwa azitsogoleli ndi mafumu kwaitanila ku Chisilamu. Ndipo mwa ena amene anawatumizila ndi mfumu ya ku Romu, mfumu yaku Persia (pano ndi Iran) komanso mfumu yaku iguputo (Eygpt).
Ali ku Madina kunachitika kadansana ndipo anthu anawopa kwambiri. Ndipo zimenezi zinachitika tsiku lomwe anamwalira mwana wa Mtumiki ﷺ wotchedwa Ibraheem. Ndiye anthu ankanena kuti izi zachitika chifukwa cha infa ya mwana wa Mtumiki ﷺ ndiye Mtumiki ﷺ ananena kuti:
(Ndithu mwezi ndi dzuwa sizimakumana chifukwa cha infa ya wina aliyense ayi kapena chifukwa cha moyo wake koma zimenezi ndi zizindikilo za Allah zimene Allah amawopyezela akapoplo ake)[3].
Zikanakhala kuti Mtumiki ﷺ anali wabodza poyitanila pake ndiye kuti akanatengela mwayi wa kadansana ameneyu ndi kuwawuza anthu kuti zachitika chifukwa cha infa ya mwana wake. Ndipo akananena kuti: "Zachitika izi chifukwa cha infa ya mwana wanga nanga kuli bwanji inu amene mukunditsutsa ine."
[3] Swahih Muslim-Buku la Imaam Muslim -nambala ya hadith mu bukumo (901).
Allah anamukongoletsa Mtumiki ﷺ ndi makhalidwe abwino okwanila, ndipo anamusimba ndi mawu ake oti:
Mtumiki ﷺ ankaziwika ndi mbiri zabwino monga kuyankhula zoona, kumuyeletsera Allah mapemphero, mphavu, chilungamo, kukwanilitsa malonjezo angakhake ndi anthu oti sakugwilizana nawo, kuwolowa manja, ankakondanso kupeleka kwa ovutika ndi masikuni, azimayi amene asiyidwa ndi amuna awo, ndi anthu onse amene ali ofunika thandizo, amayesetsa kuwawongolela ndi kuwapangila chisoni, kuzichepetsa kwa anthu, mpakana zimapezeka kuti munthu wachilendo kubwera akumufuna Mtumiki ﷺ koma osamudziwa chikhalilenicho ali pompo, mpaka amafunsa kuti: "Kodi Muhammad ndi ndani apa?"
Mbiri ya Mtumiki ﷺ chinali chisonyezo chakukwanila kwa makhalidwe ake pakakhalidwe kake ndi anthu onse, popanda kusiyanitsa m'dani wake ndi mzake, oyandikana nawo kapena apatali, wankulu kapena mwana, mamuna kapena mzimayi, zinyama ngakhale mbalame.
Pa nthawi yomwe Allah anakwanilitsa chipembezo chake kwa Mtumiki ﷺ, ndipo Mtumiki ﷺ naye nafalitsa uthenga wake mmene umafunikila, kenako anamwalira ali ndi dzaka makumi asanu ndi limozi kuza zitatu 63, ndipo dzaka makumi anayi ndizomwe anakhala asanalandile utumiki, ndipo dzaka makumi awiri ndi zitatu atalandila utumiki komanso uneneri.
Anaikidwa ku Madina ﷺ ndipo sanasiye chuma kapena katundu oti anthu agawane, kupatula nyulu yake yoyela yomwe ankakwela ndi nthaka yomwe anasiya kwa anthu apaulendo ngati sadaka.[4]
[4]Sahih Bukhar (4461), 6/15.
Anali anthu ambiria amene analowa Chisilam ndikutsatila ndipo anapanga nawo Hajj yomaliza ena mwa iwo okwana100 sauzand ndipo panali patangotsala miyezi 3 kuti amwalire. Mwinanso zimenezi ndi zina mwa zinsinsi zimene zinapangitsa kuti Chipembezo chifalikile ndipo anali ma swahaaba amene Mtumiki ﷺ anawaphunzitsa chikhalidwe cha Chisilamu maswahaab abwino, achilungamo, ozichepetsa ndi odekha, okwanilitsa malonjezo, ozipeleka pa Chipembezo chimenechi.
Mwa ophunzira ake amene anali achikhulupiliro chochuluka kwambiri, odziwa, ogwira ntchito potsatila malamulo, odziyeletsa mwa Allah, achilungamo, ozipeleka, amphamvu, komanso aulemelero ndi; Abubakar swidiq, Umar bin Al-khatwaab, Uthmaan bin Affan, Aliy bin Abi Twaalib - Allah asangalale nawo onsewo-. Amenewo ndiye anali oyambilira kulowa Chisilamu ndikuvomeleza ndi amenenso ali ma khulafaau pambuyo pake, amene anatenga utsogoleli wa Chipembezo pambuyo pake. Koma analibe kalikonse kokhuzana ndi utumiki ayi, koposa ma swahaab ena onse Allah asangalale nawo onsewo.
Allah anasunga buku lake lomwe anabweletsa kwa Mtumiki ﷺ pamodzi ndi sunnah zake, mbiri zake, zoyankhula zake, zochita zake, muchiyankhulo chomwe iye amayankhula, siyinasungike mbiri potengela nthawi ayi ngati mmene inasungidwila mbiri ya Mtumiki ﷺ, koma zinasungidwa ngakhale mmene ankagonela, kudya, kumwa ndi kuseka.
Komanso kodi Mtumiki ankakhala bwanji ndi akunyumba ake nkati mwa nyumba yake?
Khalidwe lake lonse Mtumiki ﷺ linasungidwa ndikulembedwa mu mbiri zake. Ndipo iye anali munthu, Mthenga, analibe kalikonse kokhuzana ndi umulungu ayi, komanso analibe kuthekela kozipatsa zabwino kapena zoipa.
4-UTHENGA WAKE
Allah anatumiza mtumiki Muhammad ﷺ pambuyo poti shirk inali itafalikila komanso ukafiri ndi umbuli pa dziko lapasi, ndipo palibe amene ankapembeza Allah mwachoonadi kupatula anthu ochepa kwambiri mwa eni mabuku. Kenako Allah anatumiza mthenga wake Muhammad ﷺ kukhala mtumiki womaliza. Anamutumiza ndi chiongoko komanso chipembezo choona kwa anthu onse kuti chikhale choonekela kwa zipembezo zonse, kuwatulutsa anthu ku mdima wa mafano, ukafiri ndi umbuli kupita ku umodzi wa Allah ndi chikhulupiliro. Komanso uthenga wake unali okwanilitsa mauthenga onse amene anabwela ndi azitumiki am'mbuyomu mtendere ukhale kwa iwo.
Anaitanila kwa zonse zomwe ankaitanila atumiki ndi aneneri onse mtendere ukhale pa iwo monga Nuhu Ibrahim, Mussah, Sulaiman, Daudi, ndi Issah mu chikhulupiliro chakuti Allah ndiye Mbuye amene ali Mulengi opeleka moyo ndi infa, mfumu ya mafumu, amene amayendetsa kalikonse. Iye ndi wantendere komanso wachisoni. Iye ndi amene analenga kalikonse komwe kali pa dziko pano, kamene timakawona ngakhalenso kamene sitimakaona. Ndipo kupatula Allah kalikonse ndi kolengedwa mu zolengedwa zake.
Ngati m'mene anaitanilira zopembeza Allah Mmodzi yekha ndikusiya kupembeza zina posakhala Iye. Ndipo analongosola mapeto akulongosola kuti Allah ndi M'mozi yekha pakupembezedwa, paumulungu wake, pakulenga pake, komanso pakayendetsedwe kake ka zinthu. Ndipo analongosola kuti Allah sanabeleke komanso sanabelekedwe, ndipo alibe ofanana naye komanso olingana naye. Ndipo samalowa mwa wina aliyense mu zolengedwa zake komanso samakhala ndi mawonekedwe a thupi la wina aliyense.
Ndipo amaitanila ku chikhulupiliro cha mabuku onse omwe anatumizidwa kuchokela kwa Allah monga ngati suhf Ibrahim ndi Mussah mtendere upite kwa iwo, Taurati, zaburi komanso Injiri, ngatinso mmene anaitanila za kukhulupilira za atumiki onse mtendere ukhale kwa iwo, ndipo munthu amene angakanile mwa mtumiki mmodzi mwa iwo ndiye kuti amatengedwa kuti wakanila atumiki onse.
Ndipo Mtumiki ﷺ amawasangalatsa anthu powawuza za chisoni cha Allah, kuti Allah ndi amene amayang'anila iwo pa dziko lapansi, komanso Iye Allah ndiye Mbuye wa chisoni, Iye yekha ndi amene angazawelengetse zolengedwa zake pa tsiku la chiweluzo pa nthawi yomwe zonse zizawukitsidwe mmanda. Ndipo Iye ndi amene azalipile anthu okhulupilira zabwino zawo kuyambila 10, ndipo choipa kuyambila chimozi. Ndipo ali ndi mtendere okhazikika ku mwamba. Ndipo yemwe angakanile ndikugwira ntchito yoipa amapeza malipilo ake oipawo pa dziko pano komanso ku mwamba.
Mthenga wa Allah Muhammad ﷺ mu uthenga wake sankazitamanda iye mwini kapena mtundu wake kapena mzinda wake ayi. Ndipo mu Qur'an mwatchulidwa maina atumiki ena monga Nuhu Ibrahim Mussah Issah -mtendere upite kwa iwo - amenewa atchulidwa kwambiri mu Qur'an kuposa dzina lake iye Muhammad ﷺ ndipo dzina la mayi ake silinatchulidwe ayi, angakhale maina azikazi ake, koma zina la mayi ake a Mussah latchulidwa koposa kamodzi ndipo ndzina la Marium latchulidwa kokwana ka 35.
Mthenga wa Allah Muhammad ﷺ anali otetezedwa ku zinthu zomwe zili zosephana ndi malamulo, nzeru, komanso chilengedwe, kapena zimene makhalidwe abwino amakana, chifukwa atumuki ali otetezedwa ku zimene amalalikila zochokela kwa Allah poti amalamulidwa kufalitsa uthenga wa Allah kwa akapolo ake. Ndipo atumiki alibe kena kalikonse kokhuzana ndi umulungu kapena kupembezedwa ayi, koma kuti iwo ndi anthu ngati mmene alili munthu wina aliyense, koma Allah Wapamwamba amatumiza chivumbulutso kwa iwowo cha uthenga wake.
Mu zunthu zina zikulu zikulu zosonyeza kuti chivumbulutso cha Muhammad ﷺ ndi chenicheni chochokela kwa Allah ndiye kuti mpaka lero chidakalipo ngati mmene chinalili kale mu nthawi ya umoyo wake. Ndipo anthu ambri oposa billion ndi amene akutsatila pogwilitsa ntchito malamulo amenewa monga swala, zaka, swaum, Hajj ndi zina monga izo popanda kusintha kapena kutembenuza
5-Zizindikilo za utumiki wake komanso zisonyezo ndi maumboni ake.
Allah ankamulimbikitsa mtumiki wina aliyense ndi zithu zozizwitsa zosonyeza utumiki wake zomwe zimasonyeza ndikuyikila umboni za uthenga wake. Ndipo Allah anapeleka kwa mtumiki wina aliyense zisonyezo zokwanila kwa anthu kuti amukhulupilire. Chisonyezo chachikulu chomwe anampatsa mtumiki Muhammad ﷺ ndiye Qur'an chimenecho ndichizindikilo chomwe chilipo mpaka tsiku la Kiyama, ngatinso mmene anampatsila zizindikilo zina zozizwitsa zikuluzikulu monga izi :
Ulendo umene anayenda Mtumiki ﷺ kupita ku Yelusalemu mu usiku umodzi komanso kumwamba, kugawikana kwa mwezi kukhala magawo awiri, kugwa kwa mvula pambuyo poti Mtumiki ﷺ wapepha nthawi yoti kunalibe ng'amba.
Kuchulukitsa kwa chakudya ndi madzi mpaka anthu ambiri kudya ndi kumwa ndikutsalanso.
Kulongosola zinthu zakalekale zimene sizinkadziwika kwa wina aliyense, amadziwa iye pouzidwa ndi Allah, ngati nkhani za atumiki mtendere ukhale kwa iwo ndi anthu awo komanso ndi nkhani ya anthu amene anabisala ku phanga (Aswihaabul kahafi).
Kufotokoza Mtumiki ﷺ zinthu za mstogolo zomwe zidachitika pambuyo poti iye wawuzidwa ndi Allah, monga kuuzidwa kuti moto uzatuluka ku nthaka ya Hijazi, ndipo anauwona amene anali ku Shami ndi kupikisana anthu pomanga manyumba.
Chisamaliro cha Allah kwa Mtumiki ﷺ ndi kumuteteza kwake ku ziwembu za wanthu.
Komanso kukwanilitsidwa kwa malonjezo ake omwe adawalonjeza maswahaba ake monga mmene adayakhulira mmawu ake akuti:
(Nthawi ikubwela imene muzagonjetse dziko la Roma ndi Persia ndipo chuma chake mudzachigwiritsa ntchito pa njira ya Allah)
Kuthandizidwa kwake ndi angelo kuchokela kwa Allah
Kuyankhula kumene anayankhula atumiki kwa anthu awo zokhuzana ndi kubwela kwa mtumiki Muhammad ﷺ, ndipo mwa omwe anayankhula izi ndi Mussah, Daudi, Sulaiman komanso Issah mtendere wa Allah upite kwa iwo, ndi enanso mwa atumiki ochokela ku ana a Israel.
Komanso ndi ma umboni ena ochokela ku nzeru komanso ndi zitsanzo zomwe anapeleka Allah zomwe zimagwirizana ndi nzeru zabwino.
(5)Monga mawu a Allah wapamwamba wonena kuti: (E inu anthu! Chapelekedwa chitsanzo ndipo chinvetseleni, ndithu anthu amene amampembeza wina posakhala Allah sangathe kulenga ntchenje, ngakhale atati asonkhane pa iyo. Komanso ngakhale ntchenjeyo itawalanda china chake sangakwanitse kuti ayilande. Ndithu ali ofooka onse opempha ndi opemphedwa.
Ndipo zizindikilo ndi zitsanzo izi zogwilitsa ntchito nzeru zilipo zambiri mu Qur'an yolemekezeka komanso mu Sunnah za Mtumiki ﷺ ndipo ma umboni ake ndi ambiri osawerengeka. Ndipo amene akufuna kudziwa za izi akuyenera kubwelela ku Qur'an ndi sunnah komanso mu mbiri za Mtumiki ﷺ chifukwa mma buku amenewa muli nkhani za nzeru zotsimikizika za zizindikilo zimenezi.
Zizindikilo zimenezi zikanati zisachitike ndiye kuti anthu amene amatsutsa za utumiki wake kuyambila ma kafiri achiquraish komanso Ayuda ndi Achrisitu aku chilumba cha ma arabs akanapezelapo mwayi omukanila Mtumiki ndikuwauza anthu kuti asamutsatire. .
Qur'an yolemekezeka ndilo buku lomwe Allah anavumbulutsa kwa mtumiki Muhammad ﷺ. Ndimawu a Mbuye wa zolengedwa zonse. Ndipo Allah anawatchalenja anthu ndi ziwanda kuti abweletse yofanana nayo kapena sura imodzi. Komanso amatchalenjabe mpaka lero. Qur'an yolemekezeka imayankha mafunso ambiri amene amazunguzika nawo mamiliyoni a anthu. Qur'an inasungika mu chiyankhulo chake cha Arabic chomwe inatsikila, ndipo simunapungulidwe ngakhale liwu limodzi. Inatsindikizidwa ndikugawiga. Ili ndibuku lolemekezeka lozidzwitsa. Ndibuku lalikulu lomwe linatumizidwa kwa anthu. Choncho nkofunika kuliwelenga komanso kuwelenga matanthauzo ake. Ndipo munthu amene kwamudutsa kuwelenga buku limeneli ndi kulikhulupilira ndiye kuti waluza zinthu zabwino kwambiri
Monga mmene zilili sunnah za mtumiki Muhammad ﷺ, chiongoko chake ndi mbiri yake zonse zinalembedwa ndikusungidwa, ndipo zimatengedwa kuzela kwa anthu okhulupilika, ndipo zinalembedwa muchiyankhulo cha charabu chomwe ankayankhula mtumiki Muhammad ﷺ kukhala ngati ali nafe pakati pathu. Ndipo zatanthauziridwa mu ziyankhulo zosiyanasiyana. Qur'an ndi sunnah ndiye ma buku awiri amene mumachokela malamulo achisilamu.
6-Malamulo amene anabwera ndi mtumiki Muhammad ﷺ.
Malamulo amene anabwela ndi mtumiki Muhammad ﷺ ndi malamulo achisilam komanso ndi omaliza mwa malamulo ochokela kwa Allah ndi uthenga ochokole kwa Allah. Ndipo ndi ofanana chiyambi chake ndi ma uthenga onse amene anabwela ndi atumiki akale ngakhale zitasiyana kapangidwe kake.
Amenewa ndi malamulo okwanila amene amagwilizana ndi nthawi zonse komanso malo alionse, amene ali ndi chikonzelo cha chipembezo cha anthu ndi umoyo wawo wa dziko lapansi. Komanso muli ma pemphelo onse amene ali okakamiza kwa munthu kuti awachite kwa Mbuye wake Mwini zolengedwa zonse, monga ngati swala, zakat, komanso amalongosola za kachitidwe ka malonda a za chuma, komanso za chikhalidwe cha pa gulu, ndale ndi nthawi ya nkhondo, komanso zikhalidwe zomwe zili zoletsedwa ndi zovomelezeka ndi zina mwa izo zofunika pa moyo wa munthu.
Malamulo amenewa amasunga zipembezo za anthu, magazi awo, ulemelelo wawo, chuma chawo, mzeru zawo, komanso ana awo. Malamulo a Chisilamu amalamulira kalikonse kabwino ndi ubwino, komanso amachenjeza ku kalikonse koipa ndi konyansa. Malamulo amenewa amaitanila ku chithu chopeleka ulemelelo ndikukhala munthu wabwino, wachilungamo, oyeletsa Chipembezo cha Allah, waukhondo, wokhulupilila, wa chikondi, wokonda zabwino kwa anthu, kuteteza magazi, komanso kubweletsa mtendere, ndi kuletsa kuwaopyeza anthu popanda chifukwa. Ndipo Mtumiki ﷺ anali akulimbana ndi anthu amene anali odumpha malire owononga kwa mtundu uliowonsewo. Komanso ankatsutsana ndi zinthu zopeka komanso umoyo wokhala pa wekha komanso kusakwatila.
Komanso Mthenga Muhammad ﷺ analongosola kuti Allah analemekeza munthu wina aliyense mamuna ndi mkazi ndipo anamusungira maufulu ake onse. Komanso adzafunsidwa pazomwe adasankha kuchita mu zichitochito zake zonse, komanso amakhala ndi udindo wodzichitira zabwino iye mwini kapena kuwachitira ena, ndipo anampanga wina aliyense mwamuna ndi mkazi kukhala ofanana pa chikhulupiliro malipilo azabwino ndi zoipa. Malamulo amenewa amateteza mwapadela azimayi, monga mayi, mkazi wa munthu, mwana wachitsikana komanso mchemwali.
Malamulo amene anabwela nawo mtumiki Muhammad ﷺ anabwela kuzateteza nzeru ndikuletsa kalikonse koononga nzeruzo monga kumwa mowa. Chisilamu chinatenga chipembezo kukhala kuwala kounikila nzeru njira yake kuti munthu azitha kupembeza Mbuye wake mwa uzindikili ndi luntha, ndipo malamulo achisilamu anapanga nzeru kukhala chinthu chapamwamba, ndipo anazipanga nzeru kukhala njira yolamulidwila, ndipo nzeru anazimasula kuzinthu zopeka komanso zopembeza ma fano.
Malamulo a Chisilamu amalemekeza maphuziro amene ali owona, ndipo amalimbikitsa kufufuza maphunziro popanda kulowetsa zibwana. Komanso malamulo amaitanila ku kuyang'ana ndikuganizila za mzimu komanso dziko lapansi mmene Allah analengela. Ndipo zotsatila za kufufuza kolondola sizimasemphana ndi zimene anabweretsa mtumiki Muhammad ﷺ.
Mu malamulo a Chisilamu mulibe kupatula mtundu wa anthu mwapadela kusiya mtundu wina ayi, komanso palibe ubwino wa anthu ena kupotsa ena, koma kuti pa malamulo ake a Allah anthu onse ndiofanana, chifukwa anthu onse chiyambi chawo ndi chimodzi, ndipo palibe kupatulika kwa ntundu wina kupotsa wina, kapena gulu lina kupotsa gulu lina ayi, kupatula amene ali owopa Allah. Mthenga wa Allah ﷺ analongosola kuti munthu wina aliyense anabadwa pa chipembezo cha chilengeswe (Chisilamu), palibe amene anabadwa ali olakwa kapena atatengera zolakwa za wina ayi.
Mu malamulo a Chisilamu Allah analamula kulapa; kumeneko ndiye kubwelela komwe munthu amabwelela kwa Mbuye wake, kusiya za machimo, ndipo Chisilamu chimachotsa machimo akale omwe unachita, komanso kulapa kumachotsa machimo omwe adachitika m'mbuyo. Ndipo ndizosayenela kuti ulongosole pamaso pa munthu winanso za machimo ako. Mu Chisilamu ubale wa munthu ndi Mbuye wake umakhala oyandikana kwambiri umene siumafunikilanso kuti wina akhale m'khalapakati pa iwe ndi Allah. Chisilamu chimaletsa munthu kuti atengedwe ngati mulungu kapena apangidwe othandizana ndi Mulungu pa umulungu wake kapena pakupembezedwa kwake.
Malamulo amene anabwela nawo mtumiki Muhammad ﷺ ndimalamulo amene anachotsa malamulo amene analipo chifukwa malamulo amene anabwela nawo Muhammad ﷺ amenewa ndiye malamulo omaliza mpaka tsiku la Kiyama. Ndipo ndimalamulo awonse, ndichifukwa chake anachotsa malamulo akale onse monga mmene ankachotserana malamulo enawo m'mbuyomu. Ndipo Allah salandila chipembezo china posakhala cha Chisilamu chimene chinabwela ndi mtumiki Muhammad ﷺ. Munthu amene afune chipembezo china posakhala cha Chisilam mdiye kuti sichizalandilidwa. Ndipo amene akufuna kuti adziwe motambasula za malamulo a Chisilamu ndiye kuti afunefune m'mabuku amene ali odalilika amene amafotokoza za Chisilamu.
Cholinga cha malamulo a Chisilamu monganso momwe chiliri cholinga cha mauthenga onse a Allah, ndichakuti chipembezo choona chikale chofunikira kwambiri kwa munthu kuti akhale kapolo opembeza momuyeletsera chipembezo Allah Mbuye wa zolengedwa zonse. Ndi kumumasula mu ukapolo opembeza munthu mzake, kapena zinthu zadziko lapansi, kapenanso zopeka.
Ndithu malamulo a Chisilamu ndi abwino nthawi zonse ndi malo ena alionse, ndipo samasephana ndi ubwino ulionse wa munthu, chifukwa anatsika kuchokela kwa Allah amene amadziwa zofunika za munthu, ndipo anthu akufunikira kukhala ndi malamulo omwe ali owona, amene samatsutsana ena ndi ena, abwino kwa munthu, komanso amakhala ochokelakwa kwa Allah osati kwa munthu. Amamuongolela munthu ku njila yolungama ndi yowongoka. Ngati anthu akugwirtsa ntchito malamulo amenwa zinthu zawo zimalongosoka, zimaongoka ndipo amapulumutsidwa ku kupondelezana wina ndi nzake.
7-Maganizo a anthu otsutsana ndi Mtumiki ﷺ poyikila pawo umboni za Mtumikiyo.
Palibe kukaikila kuti mtumiki wina aliyense anali ndi anthu amene amatsutsana naye za kuitanila kwake, komanso amawaletsa anthu kuti asakhulupilire. Ndipo Mtumiki Muhammad ﷺ anali nawonso ambiri mu nthawi ya umoyo wake komanso angakhale atamwalira. Koma Allah anathandiza atumiki onsewo, ndipo maumboni ambiri apelekedwa kuchokela kwa iwo akale komanso apakalipano, kuti iye ndi Mtumiki ndipo anabwela ndizonga zomwe anabwela nazo atumiki ena akale mtendere upite kwa iwo, ndipo iwo amadziwa kuti iye ali pa chilungamo koma pali zambiri zomwe zimawaletsa kuti akhulupilire, monga kukonda ma udindo, mantha owaopa anthu okhala nawo, kapena kuluza chuma chomwe amachipeza chifukwa cha udindo wawo.
Kuyamikidwa konse ndi kwa Allah Mbuye wa zolengedwa zonse.
Related books
All books
CHIKAKAMIZO CHOGWIRITSA NTCHITO SUNNA ZA MTUMIKI(SAW)NDIKUKANIRA KWA MUNTHU YEMWE ANGAZIKANE SUNNAZO.23 languagesCHIKAKAMIZO CHOGWIRITSA NTCHITO SUNNA ZA MTUMIKI(SAW)NDIKUKANIRA KWA MUNTHU YEMWE ANGAZIKANE SUNNAZO.
WOLEMBA BUKU: ABDUL AZIZ BIN ABDUL ALLAH BIN BAZ(ALLAH AWACHITIRE CHISONI). M'dzina la Mulungu ,Wachifundo Chambiri ,Wachisoni Chosatha. MAU OYAMBA Kuyamikidwa konse ndikwa Mulungu, mbuye wa zolengedwa zonse, ndipo mathero abwino pa chinthu chilichonse amakhala kwa anthu oopa Mulungu, mtendere ndi madalitso a Mulungu zikhale pa kapolo komanso mtumiki wake,mneneri wathu Muhammad; amene anatumizidwa kuti akhale ozichitira chisoni zolengedwa zonse,komanso mtendere ukhale kwa anthu aku banja kwake,ophunzira ake anthu amene anatenga uthenga ochokera mu buku la mbuye wawo pamodzi ndi…
الإسلام دين رب العالمين
Ndani adandilenga? Nanga chifukwa chiyani?75 languagesNdani adandilenga? Nanga chifukwa chiyani?
Cholengedwa Chili chonse chimasonyeza kupezeka kwa Mlengi. Ndani adalenga kumwamba ndi dziko la pansi ndi zolengedwa zikuluzikulu zomwe zili mkati mwa ziwirizi zomwe sizimadziwika? Kodi ndi ndani adaika ndondomeko yokuya ndi yolongosoka bwino yakayendedwe ka zinthu kumwamba ndi dziko lapansi? Kodi ndani amene adalenga munthu ndikumupatsa makutu, maso, ndi nzeru? ndikumpatsa kuthekera kophunzira ndikudziwa zoona? Kodi mungafotokoze bwanji ndondomeko yodzama ndi yokuya ya momwe Mulungu adaikira ziwalo zapa thupi lako komanso ziwalo za zinthu za moyo? ndani adalenga zimenezo? Kodi dziko…
الشهادتين78 languagesالشهادتين
Ngati ukufuna kulowa mu chipembedzo cha Chisilamu, ukuyenera kuyankhula mau oikira umboni awa momveka bwino: Ngati ukufuna kulowa mu chipembedzo cha Chisilamu,ukuyenera kuyankhula mau oikira umboni awa momveka bwino,komanso umvetsetse matanthauzo ake ndikuwakhulupilira matanthauzowo: Ndikuikira umboni kuti palibe mulungu oyenera kupembedzedwa mwa choonadi koma , Ndikuikira umboni zoti palibe Mulungu oyenera kupembedzedwa mwa choonadi koma Mulungu m'modzi yekha(mau amenewa amatanthauza kuti palibe wina aliyense amene akuyenera kupembedzedwa koma Mulungu m'modzi yekha). Ash-hadu an laa ilaha…