M'dzina la Mulungu ,Wachifundo Chambiri ,Wachisoni Chosatha. Kodi unayamba wazifunsa wekha? Kodi ndi ndani amene adalenga mitambo ndi nthaka,komanso zolengedwa zazikulu zikupezeka ku mitambo ndi pansi pa nthaka? Kodi ndani adapanga ndondomeko yokuya ndi yokonzedwa mwa ukadaulo?
Chipembedzo chogwirizana ndi chilengedwe, nzeru ndi chobweresa chisangalalo.
M'dzina la Mulungu ,Wachifundo Chambiri ,Wachisoni Chosatha.
Kodi unayamba wazifunsa wekha?
Kodi ndi ndani amene adalenga mitambo ndi nthaka,komanso zolengedwa zazikulu zikupezeka ku mitambo ndi pansi pa nthaka? Kodi ndani adapanga ndondomeko yokuya ndi yokonzedwa mwa ukadaulo?
Ndithu, kuli Mulungu wamkulu, Mlengi ndi Wolamulira wa chilengedwe chonse ndi zonse zili m’menemo, ndipo Iye ndi Mulungu Wamphamvu zonse.
Ndipo Ambuye, Ulemelero ukhale kwa Iye, adatitumizira ife atumiki, ndipo adawatsitsira atumikiwo mabuku (chivumbulutso),ndipo lotsiriza mwa mabukuwo ndi buku la Qur’an lolemekezeka, limene Mulungu adalivumbulutsa kwa Muhammad, womaliza mwa atumiki a Mulungu, ndipo kudzera mwa mabuku ake ndi atumiki ake:
⦁Anatizindikiritsa ife za iye mwini, mbiri zake, ndi zoyenera kuti tizimuchitira, ndipo wafotokoza zoyenera iye kutichitira ife ngati tachita zoyenera kumuchitira iyeyo.
⦁Watisonyeza potidziwitsa kuti iye ndi Mbuye amene adalenga zolengedwa zonse, ndikuti iye ndi wa moyo mpaka kale sadzamwalira, ndipo zolengedwa zonse zili m’manja mwake,pansi pa mphamvu ndi ulamuliro wake.
Ndipo adatiuza kuti zina mwa mbiri zake ndi kudziwa, ndithu iye ngodziwa chilichonse, ndi kuti ngwakumva,kupeya ,ndipo palibe chobisika kwa iye padziko lapansi kapena kumwamba.
⦁Ndipo adatiuza kuti Iye ndi Ambuye, amene amadziwika ndi mbiri zangwiro, ndipo adatipatsa maganizo ndi mphamvu zomwe zimazindikira zodabwitsa za chilengedwe Chake ndi mphamvu zake, zomwe zimatisonyeza ukulu wake, mphamvu zake, ndi ungwiro wa mbiri zake. ndipo anaika mwa ife chibadwa chimene chimasonyeza ungwiro Wake ndi kuti Iye sangadziŵike ndi kupunguka.
⦁Ndipo anatiphunzitsa kuti Ambuye ali pamwamba pa mitambo yake, ndipo salowa m’dziko lapansi, ndipo dziko lapansi silikhala mwa Iye.
⦁Ndipo anatiuza kuti tiyenera kugonjera kwa Iye, Ulemerero ukhale kwa Iye, pakuti Iye ndiye Mlengi wathu ndi Mlengi wa dziko komanso muyendetsi wake
Mlengi ali ndi mbili za ukulu ndipo sangadziŵike konse ndi kusoŵa kapena kupereŵera, Mbuye saiwala, samagona, sadya chakudya, ndipo sangakhale ndi mkazi kapena mwana. Zolemba zonse zomwe zili ndi chilichonse chotsutsana ndi ukulu wa Mlengi, sizili mbali ya chivumbulutso cholondola chomwe chidadza ndi Atumiki a Mulungu, mtendere ukhale pa iwo.
Zoona zake n’zakuti, Mbuye, Mlengi Wamkulu, “Mulungu,” anatiuza za cholinga chake pakulengedwa kwa ife, chomwe ndi kupembedza Mulungu yekha, ndi zimene amafuna kwa ife! ndipo Adatiuza kuti Iye yekha ndiye woyenera kupembedzedwa, ndipo adatifotokozera kudzera mwa atumiki ake, mtendere ukhale pa iwo, momwe tingamupembedzere? Kodi tingaziyandikitse bwanji kwa Iye potsatira malamulo Ake ndi kusiya zoletsa zake? Kodi tingapeze bwanji chiyanjano Chake? Timachenjeza za chilango chake, ndikutiuza za tsogolo lathu pambuyo pa imfa?
Ndipo Adatiuza kuti moyo wapadziko lapansi ndi mayeso chabe, ndi kuti moyo weniweni ndi wokwanira udzakhala m’moyo wapambuyo pa imfa.
Adatiuzanso kuti yemwe adzapembedza Mulungu monga momwe adamulamulira, nasiya zomwe adamuletsa. Adzakhala ndi moyo wabwino padziko lapansi ndi chisangalalo chamuyaya tsiku lomaliza, ndipo amene samumvera ndi kukanira iye adzapeza masautso padziko lapansi ndi chilango chamuyaya tsiku lomaliza.
Chifukwa tikudziwa kuti sitingadutse moyo uno popanda aliyense mwaife kulandira mphotho ya zomwe adachita, zabwino kapena zoyipa; ndiye sipadzakhala chilango kwa ochita zoipa, komanso malipiro abwino kwa ochita zabwino?
Amene ayang’ana zimene anthu ambiri akupembedza lero; ampeza wina akupembedza munthu, wina akupembedza fano, wina akupembedza Nyenyezi, ndi zina zotero.Ndipo sizoyenera kwa munthu wanzeru kupembedza zina koma Mbuye wa zolengedwa zonse, wokwanira mu mbiri zake, nanga apembedza bwanji cholengedwa ngati iye mwini kapena chapansi kuposa iye! Mulungu wopembedzedwa sangakhale munthu, fano, mtengo, kapena nyama!
Zipembedzo zonse zomwe anthu akuzipembedza lero - kupatula Chisilamu - nzosavomerezeka kwa Mulungu, chifukwa ndi zipembedzo zopangidwa ndi anthu, kapena zipembedzo zomwe zidali zamulungu kenako nkusokonezedwa ndi manja a anthu, pomwe chisilamu ndi chipembedzo cha Mbuye wa Zolengedwa zonse, sichingasinthe kapena kusinthika, ndipo buku la chipembedzochi ndi Qur’an yopatulika, ndi buku losungidwa monga momwe Mulungu adalivumbulutsira ndipo likadali m’manja mwa Asilamu mpaka lero m’chinenero chomwe lidavumbulutsidwa nacho kwa Mtumiki womaliza.
Chimodzi mwa maziko a Chisilamu ndi kukhulupilira atumiki onse amene Mulungu anawatuma, onsewo adali anthu, Mulungu adawapatsa zisonyezo ndi zozizwitsa, ndipo adawatumiza kuti aitanire anthu kuti apembedze Iye yekha, popanda ophatikizana nawo.Womaliza mwa azithenga ake ndi M'thenga Muhammad (SAW) Mulungu adamutumiza ndi lamulo lomaliza lomwe limafafaniza malamulo a atumiki amene adalipo patsogolo pake, ndipo adamuthandiza ndi zizndikiro zazikulu ndipo chachikulu kwambiri ndi Qur'an yopatulika, liwu la Mbuye wa zolengedwa zonse, Buku lalikulu kwambiri lodziwika kwa anthu, lozizwitsa m'menemo, m'mawu ake, dongosolo lake, malamulo ake, ndipo m'menemo muli chiongoko cha kuchoonadi chobweretsa chisangalalo Padziko lino lapansi ndi tsiku lomaliza ndipo ndithu idavumbulutsidwa m’Chiarabu.
Pali maumboni ambiri omveka kuchokera mu nzeru ngakhale maphunziro omwe akutsimikizira popanda chikaiko kuti Qur’an iyi ndi mawu a Mlengi, Ulemerero ukhale kwa Iye, ndikuti sizingatheke kukhala zonena za anthu.
Zina mwa maziko a Chisilamu ndi kukhulupirira angelo ndi kukhulupirira tsiku lomaliza, pamene Mulungu adzaukitsa anthu m’manda awo pa tsiku lachimaliziro kuti awawerengere pazochita zawo, choncho amene anachita zabwino ali wokhulupirira adzapeza chisangalalo chosatha ku m’Paradaiso, ndipo amene Akanira ndi kuchita zoipa, adzakhala ndi chilango chachikulu ku moto. ndipo mwa maziko a Chisilamu ndiko kukhulupilira zimene Mulungu adakonza nzabwino kapena zoipa.
Ndipo Chipembedzo cha Chisilamu ndi njira yokwanira ya umoyo, yogwirizana ndi Chilengedwe ndi nzeru, ndipo chimalandiridwa ndi mitima yangwiro, idakhazikitsidwa ndi Mlengi Wamkulu pa zolengedwa Zake, ndipo ndi chipembedzo cha ubwino ndi chisangalalo kwa anthu onse padziko lapansi ndi tsiku lomaliza, silisiyanitsa gulu la munthu wina ndi wina, ngakhalenso mtundu wina kuposa wina, ndipo anthu m’menemo ndiwofanana, palibe amene ali wopatulika mu Chisilamu kupatula ndi mulingo wa ntchito zake zolungama.
Zina mwa zimene Mulungu akutsimikiza m’Qur’an yopatulika ndi kuti kukhulupirira kuti Mulungu ndi Mbuye ndi wopembedzedwa, Chisilamu ndi chipembedzo, ndi kuti Muhammad ndi Mtumiki, ndi kulowa m’Chisilamu ndi chinthu chofunikira chomwe munthu alibe kuchitira mwina, Tsiku lachimaliziro padzakhala chiwerengero ndi malipiro. Amene ali Msilamu wokhulupirira woona, adzapambana ndi kupambana kwakukulu. Ndipo amene anali wokanira adzakhala ndi kuluza koonekera.
Cholengedwa Chili chonse chimasonyeza kupezeka kwa Mlengi. Ndani adalenga kumwamba ndi dziko la pansi ndi zolengedwa zikuluzikulu zomwe zili mkati mwa ziwirizi zomwe sizimadziwika? Kodi ndi ndani adaika ndondomeko yokuya ndi yolongosoka bwino yakayendedwe ka zinthu kumwamba ndi dziko lapansi? Kodi ndani amene adalenga munthu ndikumupatsa makutu, maso, ndi nzeru? ndikumpatsa kuthekera kophunzira ndikudziwa zoona? Kodi mungafotokoze bwanji ndondomeko yodzama ndi yokuya ya momwe Mulungu adaikira ziwalo zapa thupi lako komanso ziwalo za zinthu za moyo? ndani adalenga zimenezo? Kodi dziko…
Mu lina lya mlungu msyene chanasa chakwendelechela pa yagumbidwa yosope pa dunia pano,nambo soni chanasa chitakatendele wandu wakumkulupilila jwelejo lyuwa lya qiyama Mtume jwa dini ja chisilamu Muhammad -chanasa ni utendele wa mlungu ijaule kwa jwelejo. Mbiri ya chidule ya mtumiki wa chisilamu Muhammad mtendere ndi madalitso zipite kwa iye,ndipo nkatikati mwa mbiri yake ndikulongosola za dzina lake fuko lakemalo amene anabadwila komanso ndima banja ake chivumbulutso chake chomwe anabwela nacho kuyitanila kwake ku zinthu zomwe anabwela nazo zizindikilo za utumiki wake malomulo ake komanso…
Buku lofotokoza za njira zothandizira kukhala umoyo wa chimwemwe lolembedwa ndi Sheikh Abdul-Rahman bin Nasir as-Sa'die, limafotokoza mozama njira zobweresera chisangalalo chenicheni kuchokera pa mawonedwe a chikhulupiliro chozama; ndipo limatsogolera owerenga ku bata la mtima kudzera mu chikhulupiliro ndi ntchito zabwino, kukumbukira Mulungu, kukhutira, kusinkhasinkha za madalitso, kuchita ubwino, kuyezamira mwa Mulungu, kuleza mtima, ndi kuzindikira moyenera kufunika kwa zinthu. Mu kalembedwe kokongola, limayika pamaso panu kalozera wa moyo wamtendere, wolinganizika, komanso wosangalala…