Kodi adalenga dziko ndi ndani? Kodi ndi ndani adandilenga ine?Nanga chifukwa chiyani adandilenga?
Kodi ine ndili panjira yolondola? Kodi ndi ndani amene adalenga mitambo ndi nthaka,ndi zolengedwa zikuluzikulu zosatheka kuzizungulira? Kodi ndi ndani adaika ndondomeko yokuya ndi yolongosoka bwino yakayendedwe ka zinthu kumwamba ndi dziko lapansi? Kodi ndani amene adalenga munthu ndikumpatsa makutu, maso, ndi nzeru? ndikumpatsa kuthekera kophunzira ndikudziwa zoona?
These files are generated automatically from the book's text; their layout may differ from the printed edition.
Kodi adalenga dziko ndi ndani? Kodi ndi ndani adandilenga ine?Nanga chifukwa chiyani adandilenga?
Kodi ine ndili panjira yolondola?
Kodi ndi ndani amene adalenga mitambo ndi nthaka,ndi zolengedwa zikuluzikulu zosatheka kuzizungulira?
Kodi ndi ndani adaika ndondomeko yokuya ndi yolongosoka bwino yakayendedwe ka zinthu kumwamba ndi dziko lapansi?
Kodi ndani amene adalenga munthu ndikumpatsa makutu, maso, ndi nzeru? ndikumpatsa kuthekera kophunzira ndikudziwa zoona?
Kodi ndi ndani amene adaika ziwalo zapa thupi pako mwa dongosolo ndi molondoloza,ndikukupatsa maonekedwe ndikuwakongoletsa maonekedwe ako?
Talingalira za kulengedwa kwa zolengedwa zomwe zili zamoyo za mitundu yosiyanasiyana, ndi ndani adadzilenga ndi maonekedwe opanda malire?
Kodi dziko lalikululi zimatheka bwanji zinthu kuchitika mwa ndondomeko komanso mokhazikika potengera malamulo okuya omwe akhala akulitetedza dzikoli kwa dzaka zochuluka?
Ndi ndani amene adakhazikitsa ndondomeko zomwe zimayendesa dzikoli(moyo ndi imfa, kuberekana kwa zamoyo, usiku ndi usana, kusintha kwa nyengo, ndi zina zotero)?
Kodi dzikoli lidazilenga lokha? Kapena lidangobwera popanda kochokera? Kapena zinangopezeka mwazizizi? Mulungu wapamwamba akuyankhula kuti: (Kapena adalengedwa popanda Mlengi, kapena iwo ndi amene adalenga zolengedwa(35). Kapena iwo ndi amene adalenga mitambo ndi nthaka? Koma kuti iwo samakhulupilira za chilango cha Mulungu chifukwa iwo ndi omuphatikiza Mulungu ndi zinthu zina). [Al-Tur:35-36].
Ngati sitidadzilenge tokha, ndipo ndi zosatheka kuti tinachokera ku zinthu zopanda chiyambi kapena mwazizizi, ndiye kuti chowona chomwe chilibe chokaikitsa ndi choti: dzikoli lili ndi Mlengi wamkulu amene ali nkuthekera kolenga,chifukwa ndi zosatheka kuti dzikoli lidadzilenga lokha,kapena lidangobwera popanda poyambira,kapena kungobwera mwazizizi.
Kodi chifukwa chiyani munthu amakhulupilira zopezeka kwa zinthu zoti sanazione?monga: (chidziwitso, nzeru, mzimu, malingaliro,ndi chikondi) kodi sichifukwa choti amaona zizindikiro zake?ndiye zitheka bwanji munthu kukanira zoti dzikoli lili ndi mlengi wake amene ali wamkulu,kumachita kuti zizindikiro za zolenga zake ,zochita zake komanso chisoni chake amaziona?!
Palibe munthu wanzeru amene angavomereze kuuzidwa kuti: Nyumbayi inabwera popanda wina kumanga! Kapena kuuzidwa kuti:chinthu choti panalibe ndi chomwe chinapezekesa nyumbayi!Ndiye zitheka bwanji kuti anthu ena azimuvomereza munthu amene akunena kuti: dziko lalikulu ngati ili linabwera popanda mlengi?zitheka bwanji munthu wa nzeru zabwino kuvomera kuti zinenedwe kwa iye kuti:ndithu dziko lomwe limayenda mwa ndondomeko bwino linangobwera mwazizizi?
Zonsezi zikutifikitsa pa mfundo imodzi yoti;dzikoli lili ndi mbuye wamkulu, wamphamvu, amene akuliyendetsa, ndi kuti iye yekha ndi amene ali oyenera kupembedzedwa mwa choonadi, ndikuti zina zonse zomwe zimapembedzedwa posakhala iye Mulungu,ndi zosokonekera,zomwe siziyenera kupembedzedwa.
Ambuye Mulungu ndi Mlengi Wamkulu
Pali mbuye mlengi m'modzi, amene ndi mwini zolengedwa zonse,oyendesa zonse,opereka zosowa za zolengedwa zonse,amene amapereka moyo ndi imfa,ndi Mulungu amene adalenga dziko lapansi ndikulipanga lokhazikika,ndikulipanga kukhala loyenera kukhala zolengedwa zake.Mulungu ndi amene adalenga mitambo ndi zolengedwa zikuluzikulu zikupezeka kumitamboko,ndipo adaika ndondomeko ya kayendedwe ka dzuwa,mwezi,usiku,usana, zomwe zikuonesa ukulu wake Mulungu.
Mulungu ndi amene adatifewesera potipatsa mpweya omwe popanda mpweyayo ife sitingakhale ndi moyo,komanso ndi iye(Mulungu)amene amatigwesera mvula,ndipo adatifewesera nyanja ndi mitsinje,Mulungu ndi amene amatipasa chakudya,ndipo amatiteteza kuyambira pamene tinali makanda m’mimba mwa azimai athu popanda mphamvu zathu.Mulungu ndi amene amayendetsa magazi m’mitsempha yathu kuyambira pamene tinabadwa mpaka kufa.
Ambuye Mulungu omwe ndi mlengi ,opereka zosowa za zolengedwa zake,ameneyo ndi Mulungu weni weni.
Mulungu wapamwamba akuyankhula kuti: (Ndithudi Mbuye wanu-ee! inu anthu!-ndi Mulungu,amene adalenga mitambo ndi nthaka kwa masiku asanu ndi limodzi, kenako adakhazikika pampando wake wachifumu,amaulowesa usiku mu usana ndikuchosa kuwala kwa dzuwa, ndikulowesa usana mu usiku ndikuchosa mdima wake,usiku ndi usana umakhala ukusatana mofulumira,Mulungu ndi amene adalenga dzuwa,mwezi,nyenyezi ndikuzipanga zogonjera malamulo a Mulungu pomwe zikutumikira zolengedwa zina,dziwani kuti zolengedwa zonse ndi zake,malamulo onse ndi ake,wayeretsedwa Mulungu mbuye wa zolengedwa zonse). [Al-A'araf: 54].
Ambuye Mulungu ndi mlengi wa china chilichonse chomwe timachiona komanso sitimachiona pa dziko pano,ndipo china chilichonse chome sichili iye Mulungu ndi cholengedwa mu zolengedwa zake, iye yekha Mulungu ndi amene akuyenera kupembedzedwa mwa choonandi, ndipo pasapezeke wina opembedzedwa limodzi ndi iye Mulungu,Mulungu alibe ophatikizana naye mu ufumu wake,pa zolenga zake,kayendesedwe kake ka zinthu kapena kupembedzedwa.
Titati tikukambirana nde tavomereza zoti pali milungu ina yopembedzedwa limodzi ndi Mulungu m'modzi opembedzedwa mwa choonadi,ndiye kuti dziko likanaonongeka;chifukwa choti sizingatheke kuti Milungu iwiri iyendetse zokhuza dziko pa nthawi imodzi,Mulungu akuyankhula kuti: {Zikadakhala kuti kumwamba ndi pansi pa dziko kuli milungu ina posakhala Mulungu m'modzi yoyendetsa zochitika kumwamba ndi dziko lapansi,ndondomeko yakayendedwe ka zinthu kakanakosokonekera}. [Al-Anbiya: 22].
Mbiri Za Mlengi
Ambuye Mulungu ali ndi maina okongola osawerengeka,komanso ali ndi mbiri zikuluzikulu zapamwamba komanso zochuluka zomwe zimasonyeza kukwanira kwake Mulungu.Ena mwa maina ake ndi: Mlengi,ndi "Allah"lomwe limatanthauza kuti:opembedzedwa amene ndi oyenera kupembedzedwa mwa choonadi popanda omuphatikiza naye. Maina ena ndi : wamoyo(amene sadzamwalira),amene zonse zolengedwa zimadalira iye,wachisoni,opereka zosowa za zolengedwa zonse,owolowa popereka zabwino. Mulungu akuyankhula mu buku la Quran kuti: (Palibe Mulungu opembedzedwa mwa choonadi koma iye, wamoyo wamuyaya,odaliridwa ndi zolengedwa zonse,samasinza kapena kumupeza tulo,zolengedwa zonse zili ku mwamba ndi dziko lapansi zili m'manja mwake,palibe amene angakhale ndi mphamvu zomuthandiza wina pamaso pa Mulungu kupatula Mulungu ataloleza kuti zitero,amadziwa za zolengedwa zonse zomwe zinalipo kalekale,zomwe zili pano ndi zomwe zidzalengedwe msogolo,amadziwa za msogolo zomwe zidzachitikire zolengedwa zake komanso zomwe zinachitika kale,palibe cholengedwa chimadziwa zobisika zake kupatula zomwe iye Mulungu wachidziwitsa cholengedwacho,mpando wa ufumu wake malo ake ndi akulu monga m'mene kulili kumwamba ndi dziko lapansi,ndipo sizimamulemera kuzisunga ndikuteteza kumwamba ndi dziko lapansi,iye Mulungu ndi wapamwamba komanso wamkulu). [Suratu Al-Baqara: 255] .
Mulungu wapamwamba akuyankhula kuti: (Nena-iwe mtumiki kwa amene akukufunsa mwachipongwe mbiri za Mulungu wako-iye ndi Mulungu m'modzi(1) Mulungu ndi wokhala ndi zonse wodaliridwa ndi zolengedwa zake(2) Sadabereke mwana komanso sadaberekedwe(3) Ndiponso palibe aliyense wofanana ndi iye(4). [Al-Ikhlas:1-4].
Mulungu wopembedzedwa mwa choonadi amadziwika ndi mbiri zachikwanekwane.
Zina mwa mbiri zake ndi kuti iye ndi: Mulungu wopembedzedwa, ndipo china chilichonse chosakhala iye Mulungu ndi cholengedwa chomwe chapatsidwa malamulo, cholamulidwa ndi kugonjetsedwa.
Zina mwa mbiri zake ndi zakuti iye ndi: wamoyo wamuyaya, chilichonse chimadalira iye, ndikuti chilichonse cha moyo chili pa dziko lapansi , Mulungu ndi amene adachipatsa moyo ndi kuchipezekesa pambuyo poti panalibe, ndipo Iye ndi amene amachiyang'anira kuti chikhale chilipo,kuchipasa zosowa zake ndikuchisamalira. Mulungu ndi wa moyo wamuyaya ndipo sadzamwalira, ndipo ndi zosatheka kuti adzamwalire,amayang'anira kalikose samagona,ngakhale kusinza kapena tulo sizimampeza.
Zina mwa mbiri zake ndi kuti iye:ndi wodziwa kalikonse, palibe pa dziko lapansi kapena kumwamba chimene chimabisika kwa iye.
Zina mwa mbiri zake ndi kuti iye ndi :wakumva zonse ndi openya, amene amamva chilichonse choyankhulidwa,ndikuona chilichonse chomwe cholengedwa chimachita, amadziwa nkhani zobisika ndi za m'mitima,palibe chomwe chimachitika pa dziko lapansi ndikumwamba ndikubisika kwa iye Mulungu.
Zina mwa mbiri zake ndi zoti: iye ndi othekera kuchita kalikonse wamphamvu,palibe chomwe chimamukanika osachita,ndipo palibe angaletse chifuniro chake kuti chisachitike,amachita zomwe wafuna,komanso amaleletsa zomwe wafuna,amatha kuchita chinthu mofulumizitsa kapena kuchichedwetsa, ndipo ali ndi nzeru zakuya pochita kalikonse.
Zina mwa mbiri zake ndi zoti: iye ndi Mlengi, opereka zosowa za zolengedwa,amayendesa kena kalikonse,amene adalenga zolengedwa ndikumayendesa zonse zokhuza zolengedwazo,zolengedwa zonse zili m'manja mwake ndi pansi pa ulamuliro wake.
Mu zina mwa mbiri zake ndi zoti: iye ndi amene amayankha pemphero la munthu otsimidwa,ndikumuthandiza munthu amene ali ndi vuto,komanso iye ndi amene amamuchosera mavuto munthu amene ali pamavuto,ndikuti zolengedwa zonse zikakhala pa mavuto kapena kuvuta kwa zinthu,zimabwelera kwa iye motsimidwa.
Mapemphero ena aliwonse asachitike kupatula pofuna kusangalatsa Mulungu wapamwamba, chifukwa iye Mulungu ndamene ali okwanira ndikuyenera kupembedzedwa mwa choonadi kusiya chilichonse chosakhala iye Mulungu, ndipo chilichonse chimene chimapembedzedwa posakhala iye,ndithudi ndi chopembedzedwa molakwika,komanso ndi chosakwanira mu mbiri zake ,chidzamwalira ndikutha.
Mulungu olemekezeka adatidalitsa ndi nzeru zomwe timazindikira nazo china chake cha ukulu wake, ndipo adaika mwa ife chibadwa chokonda zabwino, ndikudana ndi zoipa,ndipo mtima umakhazikika ngati munthu wabwelera kwa Mulungu mbuye wa zolengedwa zonse pofuna thandizo,ndipo chilengedwe chimenechi chimasonyeza za kukwanira kwake Mulungu, ndikutinso iye Mulungu sizingatheke kukhala ndi mbiri zopunguka ayeretsedwe iye.
Sizoyenera kwa munthu wanzeru kuti alambire wina aliyense kupatula amene ali okwanira mu mbiri zake.Ndiye, zitheka bwanji munthu kupembedza cholengedwa chopunguka ngati iye mwini kapena chomwe chili chapansi kuposa iye!
Mulungu oyenera kupembedzedwa sangakhale munthu ,kapena fano kapena mtengo kapena chinyama!
Ambuye Mulungu ali pamwamba pa mitambo yake, anakhazikika pampando wake wachifumu, osiyana ndi zolengedwa zake,ndipo mwa iye mulibe chilichonse chofanana ndi zomwe zili mu zolengedwa zake, ndipo mu zolengedwa zake mulibe chilichonse chofanana ndi zomwe zili mwa Mulungu.Mulungu samalowa kapena kuzifanizira mu kena kalikonse mu zolengedwa zake.
Ambuye Mulungu palibe chilichonse chofanana ndi iye, ndipo iye ndi wakumva ndikupenya chilichonse, alibe ofanana naye.Iye ndi ozidalira yekha sasowa kanthu kwa zolengedwa zake;samagona kapena kudya.Iye ndi wamkulu kwambiri koti safuna kukhala ndi mkazi kapena mwana.Mulungu amakhala ndi mbiri zazikulu ndipo sizingatheke kuti adziwike ndi mbiri zosowa kanthu kapena zopunguka.
Mulungu akuyankhula kuti: (E, inu anthu! Fanizo laperekedwa; Choncho limvereni. Ndithu, amene mukuwapembedza m'malo mwa Mulungu, sangathe kulenga ntchentche ngakhale atasonkhana (kuti athandizane) pachimenechi. Ndipo ngati ntchentche itawalanda chinthu, sangathe kuchilanda kuntchentcheyo. wofooka kwenikweni wopempha ndiwopemphedwa(73). Sadamlemekeze Mulungu kumlemekeza komuyenera. Ndithu, Mulungu Ngwamphamvu Ngogonjetsa chilichonse). [Al-hajj:73-74].
Kodi chifukwa chiyani Mulungu adatilenga ? Ndi chiyani chimene Mulungu akufuna kwa ife?
Kodi pali nzeru kuti Mulungu adangolenga zolengedwa zonsezi popanda cholinga?Kodi adazilenga zolengedwa mwa chibwana kumachita kuti iye ndi Mulungu wa nzeru zakuya wodziwa?
Kodi pali nzeru kuti amene adatilenga mu kalengedwe ka luso ndi mwadongosolo, ndi kutifewesera ife zonse zomwe zili ku mwamba ndi dziko la pansi, kuti angotilenga popanda cholinga kapena angotisiya popanda kuyankha mafunso ofunikira kwambiri , monga: chifukwa chiyani tili pa dziko la pansi lino? nanga pambuyo pa imfa pali zotani? Kodi cholinga cholengedwa kwathu ndi chiyani?
Kodi pali nzeru kuti kusakakhale zilango kwa munthu ochimwa,ndikumpasa malipiro munthu ogwira ntchito zabwino?
Mulungu akuyankhula kuti: (Kodi mukuganiza kuti tidakulengani chabe, ndikuti simudzabwezedwa kwa ife). [Al-Muminuna:115].
Mulungu adatumiza atumiki kuti tidziwe cholinga cha kupezeka kwathu pa dziko,ndipo adatilangiza momwe tingamupembedzere ndi kuziyandikitsa kwa Iye, ndikutiuza zimene Mulungu akufuna kwa ife! ndikutilangiza njira yopezera chisangalalo chake Mulungu,komanso adatiuza za komwe ndingakafikire pambuyo pomwalira.
Ndipo Mulungu adatumiza atumiki kuti adzatiuze kuti Iye yekha ndi amene ali oyenera kupembedzedwa mwa choonadi, ndi kuti tidziwe momwe tingamupembedzere, ndikutifikitsira zololedzedwa ndi zoletsedwa zake, ndikutiphunzitsa makhalidwe abwino omwe ngati titawatsatira, ndiye kuti moyo udzakhala wabwino, odzadza ndi zabwino komanso madalitso.
Mulungu adatumiza atumiki ambiri monga: (Nuhu, Ibrahim, Musa ndi Yesu) ndipo adawalimbikitsa ndi zisonyezo, zozizitswa zosonyeza kunena kwawo zoona ,ndi kuti iwo adatumidwa ndi Mulungu, otsiriza mwa iwo adali Muhammad-mtendere ndi madalitso a Mulungu zikhale pa iye.
Atumiki adatiuza momveka bwino kuti moyo omwe tikukhalau ndi ongofuna kutiyesa mayeso,ndikuti moyo weni weni udzakhala pambuyo pomwalira ndikuka m'manda.
Ndikuti kuli malo amtendere omwe akakhale anthu okhulupirira amene adali akupembedza Mulungu m'modzi yekha popanda kumuphatikiza naye ndi chilichonse,komanso adali akukhulupilira atumiki onse.Ndipo kuli moto umene Mulungu wakonzera anthu osakhulupirira omwe adali kupembedza milungu ina momuphatikiza Mulungu,kapena adali akukanira aliyense mwa atumiki a Mulungu.
Mulungu adanena kuti: (E inu ana a Adam! Akakudzerani Atumiki ochokera mwainu namakuuzani zivumbulutso zanga, (avomereni) choncho omwe adzitchinjiriza kuzoletsedwa ndi kuchita zabwino, sadzakhala ndi mantha komanso sadzadandaula(35). Ndipo amene atsutsa zivumbulutso zathu nazitukumula nazo, awo ndi anthu akumoto adzakhala m'menemo muyaya) [Al-A'araf: 35-36].
Mulungu akuyankhula kuti: (Ee! inu anthu! Pembedzani mbuye wanu yemwe adakulengani inu ndi anthu omwe adalipo kale inu musanabwere,kuti mukhale omvera malamulo a Mulungu (21) Mulungu amene adakupangirani nthaka kukhala choyala,ndikukupangirani mtambo kukhala ngati denga, ndipo amatsitsa madzi a mvula kuchokera kumitambo ndikumatulutsa ndi madziwo zipatso zosiyanasiyana kuti chikhale chakudya chanu.Choncho musamuikire Mulungu omufanizira naye ndikumazipembeza chonsecho inu mukudziwa kuti milungu inayo sinalenge kena kalikonse kuti zizipembedzedwa(22) Ngati inu mukukaira pa zomwe tazibvumbulutsa(Quran) kwa kapolo wathu(Muhammad)kuti sizinachokere kwa ife koma kuti wangopeka yekha,bweretsani chaputala chimodzi chofanana ndi cha mu buku la Quran ndipo muitane mboni zanu posakhala Mulungu,ngati inu mukunena zoona kuti buku la Quran silinachokere kwa ife ndikuti mtumiki Muhammad wangopeka(23) Ngati sangakwanitse panopa kubweretsa chaputala chofanana ndi cha mu buku la Quran,ndipo sadzakwanitsa ngakhale mtsogolo,choncho uopeni moto omwe nkhuni zake zikakhale anthu ndi miyala,moto umene wakonzedwa kuwakonzera anthu okanira(24). Ndipo auze nkhani yabwino amene akhulupirira nachita ntchito zabwino (molungama) kuti ndithu adzalandira minda ya mtendere momwe mitsinje ikuyenda pansi pake.Nthawi iliyonse kumeneko akapatsidwa zipatso ngati chakudya, adzakhala akunena: "izi ndi zomwe tidapatsidwa kale," (chifukwa chakuti) adzapatsidwa zipatso zofanana (m'maonekedwe ake ndi zimene adapatsidwapo kale. koma makomedwe ake ngosiyana).Ndiponso akalandira m'menemo akazi oyeretsedwa (ku umve wamtundu ulionse), ndipo iwo adzakhala m'menemo mpaka muyaya). [Al-Baqara:21-25].
Ndi chifukwa chiyani adatumizidwa atumiki ochuluka?
Mulungu adatumiza atumiki ake ku mibado yonse,ndipo palibe m'bado wa anthu omwe adabwera kupatula kuti Mulungu adatumizira mtumiki,kuti awalamulire zopembedza mbuye wawo Mulungu,ndikuwadziwitsa zololedwa ndi zoletsedwa zake,cholinga cha atumiki onse chinali choti:awalamulire anthu zopembedza Mulungu m'modzi yekha,ndipo m'bado wina ukayamba kusiya kapena kusintha zomwe mtumiki wawo adabwera nazo,zokhuza malamulo opembedza Mulungu m'modzi,Mulungu amatumiza mtumiki wina kuti akakonze njira yomwe anthu asiya kuisatira,ndikwabwezeresa anthu ku chibadwa chawo chabwino chopembedza Mulungu m'modzi ndikumamumvera malamulo ake. Kufikira pamene Mulungu adatsiriza kutumiza atumiki ndi kutumizidwa kwa Muhammad-mtendere ndi madalitso zikhale pa iye-, amene adabweretsa chipembedzo chokwana malamulo ake, ndi malamulo achipembedzo opita kwa anthu onse omwe adzakhale akugwira ntchito kufikira tsiku la chiweruzo,malamulo okwaniritsa malamulo omwe adabwera ndi atumiki ena,komanso malamulo omwe adachotsa ena mwa malamulo omwe adabwera ndi atumiki ena,ndipo Mulungu adalonjeza zoteteza malamulo achipembedzo chimenechi kufikira tsiku la chiweruzo.
Munthu sangakhale wokhulupirira kufikira atakhulupirira mwa atumiki onse.
Mulungu ndi amene adatumiza atumiki onse, ndipo adalamulira zolengedwa(anthu) zake zonse kuti ziwamvere iwo(atumikiwo), kotero kwa amene angakanire uthenga wa m'modzi wa iwo, ndiye kuti wakanira atumiki onse, ndipo palibe tchimo lalikulu kuposa kukanira komwe munthu angakanire chivumbulutso cha Mulungu,choncho kwa munthu amene akufuna kukalowa ku mtendere,akuyenera kukhulupilira mwa atumiki onse.
Choncho, ndi chofunika kwa munthu wina aliyense mu nyengo ino kuti akhulupilire mwa Mulungu ndi atumiki a Mulungu onse,ndikumakhulupilira tsiku lotsiriza,ndipo zimenezo sizingachitike pokha pokha atakhulupilira ndikumatsatira otsiriza mwa atumikiwo amene ndi Muhammad-mtendere ndi madalitso a Mulungu zikhale pa iye-,amene adalimbikisidwa pa utumiki wake ndi choziziswa chomwe chidzakhale mpaka kale kale chomwe ndi buku la Quran lolemekezeka,lomwe Mulungu adalonjeza zoiteteza kufikira pomwe iye Mulungu adzachose dziko lapansi ndi aliyense ali m'menemo.
Mulungu wanena mu buku la Quran kuti munthu amene angakane kukhulupirira mwa mtumiki wina aliyense mwa atumiki ake,ameneyo ndi munthu okanira mwa Mulungu ndi mau ake,Mulungu akuyankhula kuti: (Anthu amene amakanira mwa Mulungu ndi atumiki ake,mwa ayuda ndi akhirisitu,ndipo akumafuna azisiyanisa pakati pa Mulungu ndi atumiki ake pomakhulupilira mwa Mulungu ndikumakanira atumiki ake omwe Mulungu adatumiza kwa zolengedwa zake,kapena powavomereza atumiki ena ndikumawakanira ena,ndikumaganiza kuti ena mwa atumiki amamunamizira mbuye wawo,ndikumafuna kuti apeze njira yowasokelesela anthu ndikumapeka mu malamulo achipembedzo(150). Anthu otelowa ndi anthu okanira eni eni,ndipo anthu osakhulupirira ndipo tawakonzera chilango choyalutsa). [An-nisaa: 150-151].
ndi chifukwa chake ife Asilamu timakhulupirira mwa Mulungu ndi tsiku lomariza-monga momwe Mulungu adalamulira-,komanso timakhulupirira mwa atumiki ndi mabuku onse omwe adalipo kale,Mulungu akuyankhula kuti: Mtumiki wakhulupirira zimene zavumbulutsidwa kwa iye kuchokera kwa Mbuye wake. Naonso Asilamu (okhulupirira). Onse akhulupirira Mulungu, Angelo ake, mabuku ake ndi atumiki ake,iwo pamodzi ndi Mtumiki wawoyo akunena kuti): sitimalekanitsa pakati pa Atumiki ake,onse tikuwakhulupirira). '' Ndipo adanena : " tamva ndiponso tamvera. (choncho tikukupemphani) chikhululuko chanu, E! Mbuye wathu! Ndipo kwa inu nkobwelera.). [Al-Baqarah:285].
Kodi Qur'an yolemekezeka ndi chiyani?
Qur'an yolemekezeka ndi mau a Mulungu wapamwamba mwamba ndi chivumbulutso chake chimene adachivumbulutsa kwa mtumiki otsiriza Muhammad-mtendere ndi madalitso a Mulungu zikhale pa iye-ndipo ndi chozizwitsa chachikulu kwambiri chomwe ndi umboni osonyeza utumiki wake- mtendere ndi madalitso a Mulungu zikhale pa iye-, ndipo malamulo a buku la Quran ndi osimikiza kuti ochokera kwa Mulungu komanso nkhani zake zonse ndi zoona zokha zokha. Mulungu adawatsutsa otsutsa(aluya a nthawi yomwe Quran imatsika)kuti abweretse ngakhale lemba limodzi lofanana ndi la mu Quran koma adakanika kutero,chifukwa cha kukula kwa zomwe zili m'menemo ndi kukwanira kwa zomwe zili m'menemo pa chilichonse chokhudzana ndi munthu pa moyo uno ndi tsiku lomaliza, mulinso zoona zonse zachikhulupiliro zomwe ziyenera kuzikhulupirira. Mu Quran mukupezekanso malamulo ndi zoletsedwa zomwe munthu ayenera kuzitsatira pakati pa iye ndi Mbuye wake, kapena pakati pa iye ndi mzimu wake, kapena pakati pa iye ndi zolengedwa zina zonse, ndipo zonsezi zili mu kalembedwe kapamwamba kakulankhula ndi kulongosola momveka bwino. Buku la Quran muli maumboni ochuluka omveka bwino ndi mfundo maphunziro owona zomwe zikusonyeza kuti bukuli sizingatheke kukhala lochokera kwa munthu, koma ndi mau a Mbuye wa anthu, mwini ulemelero wa pamwamba.
Kodi Chisilamu ndi chiyani?
Chisilamu ndikugonjera mwa Mulungu wapamwamba mwamba pokhulupilira za umodzi wake, ndikugonjera mwa iye potsatira malamulo ake, ndikumachita malamulo ake mosangalala ndikuwalandira mwansangala, ndikukanira chilichonse chomwe chimapembedzedwa chosakhala Mulungu m'modzi.
Mulungu adatumiza atumiki onse ndi uthenga umodzi omwe ndi: kuwaitanira anthu kuti aadzipembedza Mulungu m'modzi yekha popanda omuphatikiza naye, ndi kukanira chilichonse chopembedzedwa kusiya Mulungu.
Chisilamu ndi chipembedzo cha Aneneri onse. Uthenga wawo ndi umodzi ndipo malamulo awo ndi osiyana, ndipo asilamu ndi okhawo amene amatsatira chipembedzo cholondola chimene chinabweretsedwa ndi aneneri onse. Mu nthawi ino, uthenga wa chisilamu ndi umene uli oona komanso ndi uthenga otsiriza ochokera kwa Mulungu kupita kwa anthu. Mulungu amene adatumiza Abraham, Mose, ndi Yesu- mtendere ukhale pa iwo-, ndi amenenso adatumiza Mtumiki omariza Muhammad-mtendere ndi madalitso zikhale pa iye-,malamulo a Chisilamu adabwera kuzafafaniza malamulo amene adadza patsogolo pake.
Zipembedzo zonse zomwe anthu amapembedza masiku ano - kupatula Chisilamu - ndi zipembedzo zopangidwa ndi anthu, kapena zipembedzo zomwe zidatumizidwa ndi Mulungu kenako anthu adasintha ena mwa mau a Mulungu ndikuikamo maganizo awo,ndipo mau a Mulungu adasakanikirana ndi zongopeka za anthu komanso nkhani zakale zokumva kwa azigogo awo komanso maganizo a wanthu.
Pomwe chipembedzo cha Asilamu, ndi chipembedzo chimodzi choonekera bwino chomwe sichisintha, monga momwe mapembedzero awo omwe amapembedza nawo Mulungu ndi amodzi, onse amapemphera kasanu pa tsiku,amapereka chaulere mu chuma chawo, amasala kudya mwezi wa Ramadhan. Talingalira buku la malamulo awo lomwe ndi Qur'an yolemekezeka. Limeneli ndi buku la malamulo maiko onse, Mulungu akuyankhula kuti: (Tsiku la lero ndakukwaniritsirani chipembedzo chanu, ndipo ndakwaniritsa pa inu chisomo changa, ndipo ndasangalasidwa pokusankhirani Chisilamu kukhala chipembedzo chanu.Koma amene wasimidwa chifukwa chanjala, popanda kupendekera kumachimo, (n'kudya zoletsedwazi, samapeza sambi)ndithu, Mulungu ndi okhululuka kwambiri wachisoni). [Surat Al-Maidah: 3].
Mulungu adanena mu Qur'an: (Nena uwauze-iwe Mtumiki-: Takhulupilira mwa Mulungu ndipo tikumutsatira malamulo ake, tilibe mbuye wina koma iye, tilibenso omupembedza mwa choonadi koma iye,ndipo takhulupilira mau ake amene wabvumbulutsa kwa ife,komanso uthenga umene adaumbvumbulutsa kwa bwenzi la Mulungu Abraham,ndi ana ake Ishmail andi Isac,komanso kwa mwana wa Isac amene ndi Yakobo,komanso mau omwe adawabvumbulutsa kwa atumiki omwe ndi ana obadwa mwa ana a Yakobo, ndi zomwe zidabvumbulutsidwa kwa Mose ,Yesu mu mabuku a Tora ndi Baibulo, ndipo takhulupilira zonse zomwe Mulungu adabvumbulutsa kwa atumiki onse,palibe amene tikumusiyanitsa pakati pawo ndipo ife tagonjera malamulo a Mulungu(84) Kwa munthu amene angafunefune chipembedzo china chosakhala Chisilamu, komwe ndi kugonjera mwa Mulungu pokhulupilira za umodzi wake ndikumatsatira malamulo ake,ndikugwira ntchito zonse zabwino pofuna kusangalatsa iye,komanso kumutsatira mtumiki wake otsiriza Muhammad-mtendere ukhale pa iye-pomukhulupilira mtumikiyo,kumutsatira, ndikumukonda pogwiritsa ntchito zoonesera ndi zobisika, chipembedzo chinacho sichidzalandiridwa tsiku la chiweruzo ndipo adzakhala m'modzi mwa anthu oludza(85). [Al-Imran: 84-85].
Chipembedzo cha Chisilamu ndi njira yokwanira ya moyo wa munthu,chogwirizana ndi chilengedwe ndi nzeru zabwino za munthu, malamulo ake amavomerezedwa ndi anthu a mitima yolungama. Mulungu amene adalenga zolengedwa zonse adalamulira kuti anthu adzisatira malamulo achipembedzochi, ndipo ndi chipembedzo chomwe chili ndi zabwino komanso chobweretsa chisangalalo kwa anthu onse pa dziko la pansi komanso moyo umene ukubwera. Chisilamu sichimasiyanitsa pakati pa mitundu ya anthu,kapena kusiyanitsa malamulo ake potengera khungu la munthu, anthu onse ndi ofanana pofunsidwa zotsatira malamulo ake. Ngati pali chosiyanitsa pakati pa anthu , ndi ntchito yabwino yokha basi.
Mulungu adanena kuti: (Munthu amene angamagwire ntchito zabwino,wa mmuna kapena wa mkazi, ndikukhala okhulupilira mwa Mulungu ndi Mtumiki -Muhammad,timukhazika umoyo wabwino, odekha pa dziko la pansi pano ngakhale atakhala ndi chuma chochepa, ndipo umoyo umene ukubwera, tidzamupatsa malipiro abwino kwambiri potengera ntchito zabwino zomwe amagwira pa dziko la pansi). [Al-Nahl: 97].
Chisilamu ndi njira yachisangalaro:
Chipembedzo cha Chisilamu ndi chipembedzo cha atumiki onse, komanso anthu onse, sikuti ndi chipembedzo cha anthu a mtundu wa chiluya okha.
Chisilamu ndi njira yobweretsa chisangalalo cheni cheni pano pa dziko la pansi,komanso njira yobweretsa mtendere osatha umoyo omwe ukubwera.
Chisilamu ndi chipembedzo chokhacho chomwe chimakwaniritsa zosowa za mzimu ndi thupi, ndipo chimathetsa mavuto onse a anthu. Mulungu wapamwamba adanena kuti: (Mulungu adayankhula kumuuza Adam ndi Hawa kuti: nonse tsikani kuchoka ku minda ya mtendere kupita dziko la pansi limodzi ndi Satana,inu awiri inu ndi Satanayo ndinu adani. Muli pa dziko la pansi, ngati uthenga wa chiongoko ochokera kwa ine ukakupezeni, kwa amene akatsatire uthenga wanga ndikumaugwiritsa ntchito, adzakhale olungama pa dziko la pansi ndipo sadzakhala wa tsoka tsiku lotsiriza pokalangidwa ndi zilango za Mulungu(123). (Kwa munthu amene angasiye kundikumbukira ine posagwiritsa malangizo omwe ndikumukumbutsa nawo zaine, umoyo wa pa dziko pano akhala umoyo opweteka ndi wa masautso-ngakhale atamaoneka kwa anthu kuti akusangalala komanso zonse ndi zopepuka kwa iye-, umoyo wa m'manda adzakhala ophinjidwa ndikuzunzidwa,ndipo tsiku lotsiriza adzasonkhanisidwa pa maso pa zolengedwa zonse ali osapenya komanso alibe mboni yomuikira kumbuyo). [Twaha:123-124].
Kodi ndipindula chani ngati nditalowa Chisilamu?
Kulowa Chisilamu kuli ndi maphindu akulu akulu, ena mwa maphinduwo ndi :
-Chipambano ndi ulemu umene munthu amapeza pa dziko lino lapansi pokhala kapolo wa Mulungu, apo ayi amakhala kapolo wa zinthu zopanda pake, Satana, ndi zilakolako.
-Kupambana pa tsiku lomariza pokakhululukidwa machimo ndi Mulungu,kupeza chisangalalo cha Mulungu, ndipo Mulungu akamulowesa ku mtendere, ndikukakhala munthu opambana popeza chisangalalo cha Mulungu ndi mtendere osatha, ndipo akakhala munthu opulumuka ku zilango zaku moto.
-Pa tsiku lomariza; munthu okhulupilira adzakhala pamodzi ndi aneneri, anthu oyankhula zoona,anthu omwe anafera ku nkhondo za Chisilamu ndi anthu olungama, kaye kutsekemera kukakhala limodzi ndi anthu atchulidwawa. Tsono, munthu amene sanakhulupilire; akakhala limodzi ndi a Satana, anthu oipa, anthu ochita zoipa ndi anthu owononga.
-Anthu amene Mulungu akawalowese ku mtendere, akakhala pa mtendere osatha mpaka kale , ndipo kukakhala kulibe imfa, matenda,ululu ulionse,ukalamba kapena kudandaula. Ndipo adzikapasidwa chilichonse mu zokhumba zawo. Tsono, anthu amene akalowe ku moto, akakhala pa zilango zosatha komanso zosalekeza mpaka kale.
-Ku mtendere; kuli zosangalatsa zomwe maso sadayambe aona,komanso makutu sanayambe atamva ndipo munthu sanayambe waziganizirapo. Ena mwa maumboni a zimenezi; ndi mau a Mulungu oti: (Munthu amene angamagwire ntchito zabwino,wa mmuna kapena wa mkazi, ndikukhala okhulupilira mwa Mulungu ndi Mtumiki -Muhammad,timukhazika umoyo wabwino, odekha pa dziko la pansi pano ngakhale atakhala ndi chuma chochepa, ndipo umoyo umene ukubwera, tidzamupatsa malipiro abwino kwambiri potengera ntchito zabwino zomwe amagwira pa dziko la pansi). [Al-Nahl:97]. Mulungu adanena kuti: (Palibe munthu amene akudziwa zomwe Mulungu wasungira ndi kuwabisira anthu okhulupilira , mtendere ndi zokoma zomwe zidzadekhese maso awo,malipiro awo pa ntchito zabwino zomwe amagwira pa dziko). [Surat As-sajidah: 17].
Kodi ndidzaluza chiyani ndikakana kulowa Chisilamu?
Munthu adzaluza maphunziro akulu omwe ndikudziwa zokhuza Mulungu. Adzaluzanso mwai okhulupilira mwa Mulungu ,chikhulupiliro chomwe chimamupatsa munthu mtendere ndikudekha pa dziko la pansi pano, komanso chikamupatsa munthu mtendere osatha moyo omwe ukubwera.
Munthu adzaluzanso mwayi owerenga buku lolemekezeka kwambiri lomwe Mulungu adalibvumbulutsa kwa anthu, komanso adzaluza mwayi olikukhulupilira bukuli.
Munthu adzaluzanso mwayi okhulupilira mwa atumiki akulu akulu, monganso adzaluzirenso mwayi okakhala limodzi ndi atumikiwa ku minda yaku mtendere tsiku lotsiriza. Ndipo adzakakhala limodzi ndi a Satana, anthu ochimwa ku moto waku Gahena, kaye kuipa malo amenewa kukhala okafikira komanso kaye kuipa abwenzi okakhala nawo kumeneko.
Mulungu adanena kuti: (Nena-iwe mtumiki-: ndithudi anthu oludza-kuluza kweni kweni-ndi anthu amene akakhale oludza iwowo pamodzi ndi aku banja kwawo tsiku la chiweruzo,chifukwa choti anali akuwasocheretsa pa dziko pano posapanga kukhala okhulupilira. Dziwani kuti kuludza komwe akaludze anthu omuphatikiza Mulungu ndi zinthu zina pamodzi ndi aku banja kwawo pa tsiku lotsiriza, ndikuluza kowonekera(15). Anthu oluzawa pa tsiku lotsiriza akakhala ku moto wa Gahena ndipo pa mwamba pawo pakakhala gawo la zilango za moto zomaoneka ngati mthunzi ochita kumangidwa,pansi pawonso chimodzi modzi. Chilango chafotokozedwachi,Mulungu akuwaopseza nacho akapolo ake kuti akapewe zilangozo. E! inu akapolo anga, ndiopeni ine pochita malamulo anga ndikusiya machimo ondinyoza nawo ine). [Al-Zumar:15-16].
Kwa munthu amene akufuna kukapuluka umoyo umene ukubwera,akuyenera kulowa Chisilamu ndikumamutsatira mneneri Muhammad-mtendere ndi madalitso a Mulungu zikhale pa iye.
Zina mwa zinthu zoona zomwe aneneri ndi atumiki-mtendere ukhale pa onse- adagwirizana ndi zoti: palibe amene akapulumuke ku moyo omwe ukubwera kupatula Asilamu omwe adakhulupilira mwa Mulungu ndipo samamuphatikiza ndi zinthu zina pomwe amamupembedza Mulunguyo, komanso adakhulupilira aneneri ndi atumiki onse. Anthu onse omwe amawatsatira atumiki ndikumakhulupilira zomwe adabwera nazo atumikiwo; adzakalowa ku mtendere, ndikupumuka ku moto waku Gahena.
Anthu amene adali mu nthawi ya mneneri Mose ndipo anamukhulupilira Moseyo ndikumatsatira chiphunzitso chake, anthu amenewo ndithudi adali Asilamu,Okhulupilira ndi Olungama. Koma pambuyo poti Mulungu wamutumiza Yesu kukhala mtumiki , zinali zokakamizidwa kwa omutsatira Mose kumukhulupilira Yesu ndikumutsatira. Anthu amene adamukhulupilira Yesu, ndithudi amenewo adali Asilamu Olungama,ndipo amene adakana zomukhulupilira Yesu ndikumayankhula kuti: ine ndikhalabe otsatira malamulo a Mose, munthu ameneyo si okhulupilira; chifukwa choti wakana kumukhulupilira mneneri amene adatumizidwa ndi Mulungu. Kenako pambuyo poti Mulungu watumiza mtumiki otsiriza Muhammad-mtendere ndi madalitso a Mulungu zikhale pa iye-,ndi zokakamizidwa kwa anthu onse kumukhulupilira mtumiki omarizayu. Mulungu amene adamutumiza Mose, Yesu; ndi yemweyonso amene adamutumiza mtumiki otsiriza Muhammad. Choncho, kwa munthu amene angakanire uthenga umene adabwera nawo Muhammad-mtendere ndi madalitso a Mulungu zikhale pa iye,-ndikumayankhula kuti ine ndizitsatirabe Mose ndi Yesu,munthu ameneyo sali okhulupilira pamaso pa Mulungu.
Sizikukwanira kwa munthu kungoyankhula kokha mau oti iye amawalemekeza Asilamu,komanso sizikukwanira kuti akapulumuke moyo omwe ukubwera pongopereka chaulere ndikuthandiza osauka, koma akuyenera kukhala munthu okhulupilira mwa Mulungu , mabuku ake, atumiki ake ndi tsiku lotsiriza; ndi cholinga choti Mulungu akalandire ntchito zake zabwinozo! Palibe mchimo lomwe lili lalikulu kuposa kumphatikiza Mulungu ndi zinthu zina,kumukanira Mulungu, ndikukana mau a Mulungu omwe Mulunguyo adabvumbulutsa kapena kukana utumiki wa mneneri otsiriza mwa aneneri ake Muhammad-mtendere ndi madalitso zikhale pa iye.
Kotero Ayuda, Akhrisitu ndi ena amene adamva za utumiki wa Muhammad, Mtumiki wa Mulungu (SAW), nakana kumukhulupilira ndi kukana kulowa m’chipembedzo cha Chisilamu;adzakhala ku moto wa Gahena mpaka kale, limeneli ndi lamulo la Mulungu sikuti ndi lamulo la munthu wina aliyense,Mulungu akuyankhula kuti: (Ndithudi anthu amene akanira Mulungu ndi mtumiki wake mu gulu la Ayuda, Akhirisitu ndi anthu omuphatikiza Mulungu ndi zinthu zina,zilango zawo zikakhala moto wa Gahena komwe akakhaleko mpaka kalekale, magulu a anthu amenewa ndi omwe zili zolengedwa zoipitsitsa). [Al-Bayyina: 6].
Pambuyo potsika uthenga otsiriza ochokera kwa Mulungu kupita kwa anthu; zili zokakamizidwa kwa munthu wina aliyense amene angamve zokhuza Chisilamu, ndikumva za uthenga wa mneneri otsiriza Muhammad- mtendere ndi madalitso zikhale pa iye-,amukhulupilire ndikutsatira malamulo ake, ndikutsatira zomwe adalamulira ndikumasiya zomwe adaletsa. Choncho, kwa munthu amene angamve zokhuza uthenga otsirizawu ndikukana osausatira, Mulungu sakalandira ntchito ina iliyonse kuchokera kwa iye ndipo umoyo omwe ukubwera akamupatsa zilango.
Umboni wa izi ndi kuyankhula kwa Mulungu koti: (Kwa munthu amene angafunefune chipembedzo china chosakhala Chisilamu, komwe ndi kugonjera mwa Mulungu pokhulupilira za umodzi wake ndikumatsatira malamulo ake,ndikugwira ntchito zonse zabwino pofuna kusangalatsa iye,komanso kumutsatira mtumiki wake otsiriza Muhammad-mtendere ukhale pa iye-pomukhulupilira mtumikiyo,kumutsatira, ndikumukonda pogwiritsa ntchito zoonesera ndi zobisika, chipembedzo chinacho sichidzalandiridwa tsiku la chiweruzo ndipo adzakhala m'modzi mwa anthu oludza). [Al-Imran: 85].
Mulungu adanena kuti: (Nena-iwe mtumiki-uwauze anthu omwe adapasidwa mabuku omwe ndi Ayuda ndi Akhirisitu kuti: tabwerani ku liwu la chilungamo ndi loona lomwe tonse tikuyenera kuligwiritsitsa: loti tidzipembedza Mulungu m'modzi yekha popanda omuphatikiza naye, ndikuti pasapezeke ena mwa ife owatenga anthu ena kukhala milungu kumamvera kusiya Mulungu m'modzi. Ngati atakana pambuyo powaitanira ku zabwinozi,nenani kwa iwowo-inu okhulupilira kuti-: ikirani umboni oti ndife Asilamu ogonjera mu malamulo a Mulungu ndi omupembedza iye yekha). [Al-Imran: 64].
Kodi ndi chiyani ndikuyenera kuchita kuti ndikhale msilamu?
Kuti munthu alowe Chisilamu; akuyenera kukhulupilira nsichi zisanu ndi imodzizi:
Kukhulupilira mwa Mulungu wapamwamba,ndi kuti Iye ndi Mlengi, Opereka zosowa za zolengedwa, Oyendetsa chilichonse, ndi mwini zonse zolengedwa zonse. Palibe cholengedwa chofanana ndi Iye, alibe mkazi kapena mwana, ndi kuti Iye yekha ndi amene ali oyenera kupembedzedwa mwa choonadi. Ndikuti pasapezeke chopembedzedwa limodzi ndi Iye, ndikuti munthu akhulupilire zoti kupembedza china chilichose chosakhala Mulungu m'modzi, ndi mapembedzo osokonekera.
Kukhulupilira mwa angelo kuti iwo ndi akapolo a Mulungu, amene adalengedwa ndi Mulungu kuchokera mu kuwala, ndipo ina mwa ntchito yomwe adawapatsa ndi yotsika ndi mau a Mulungu kupita nawo kwa Aneneri ake.
Kukhulupilira mabuku onse amene Mulungu adawavumbulutsa kwa Aneneri ake (monga Chipangano chakale ndi cha tsopano - mabukuwa asadasinthidwe ndi anthu oipa)-, ndipo buku lomariza ndi la Qur’an lolemekezeka.
Kukhulupilira mwa atumiki onse monga Nowa, Abraham, Mose ndi Yesu ndipo omarizira mwa iwo ndi Muhammad. Aneneri amenewa adali anthu,ndipo Mulungu adawalimbikitsa pa utumiki wawo ndi zizindikiro zozizwitsa zomwe zimasonyeza kukamba kwawo zoona.
Kukhulupilira za tsiku lomariza lomwe Mulungu adzaukitse anthu oyambilira ndi omarizira kulengedwa , ndikuwweruza pakati pa zolengedwa zake pa zomwe adali kusemphana pa dziko la pansi, ndikukawalowesa anthu okhulupilira ku mtendere ndipo anthu okanira kukalowesa ku moto.
Kukhulupilira za chikonzero cha Mulungu,ndi kuti Mulungu amadziwa zonse, zomwe zidalipo kale ndi zomwe zidzachitike mtsogolo,ndi kuti Mulungu adadziwa, adazilemba, adafuna kuti zikhale m'mene zililimo, ndi kulenga chilichonse.
Usachedwetse chiganizo!
Dziko la pansi si malo okhala mpaka muyaya...
Kukongola konse kudzachoka,ndipo chilakolako chili chonse chidzazimitsidwa...
Lidzafika tsiku limene munthu adzawerengesedwa pa chilichonse chimene adatsogoza, ndipo limenelo ndi tsiku lotsiriza ,Mulungu wapamwamba adanena kuti: Buku la ntchito za wina aliyense lidzaikidwa kumanja kapena kumanzere kwake, ndipo udzaona anthu oipa ali ndi mantha chifukwa cha machimo awo omwe adasogoza ndipo pambuyo poona mabukuwo adzizayankhula kuti: Kalanga ife taonongeka! ndi buku lanji ili lomwe silinasiye kalikonse mu zochita zathu kakang'ono kapena kakakulu koma kuti linasunga?! Adzapeza ntchito zonse zomwe adagwira pa dziko la pansi zili poonekera zitalembedwa, ndipo mbuye wako Mulungu samapondereza wina aliyense,popungula malipiro a munthu wangwiro,kapena kumonjezera olakwa chilango kuposa chilango chake). [Al-Kahf: 49].
Mulungu Wapamwamba wanena kuti munthu amene salowa Chisilamu; ndithu malo ake okafikira ndi ku moto wa Gahena komwe akakhale mpaka muyaya.
Kukhala munthu oluza sichinthu chophweka koma ndi chinthu chachikulu,komanso ndi chinthu chopweteka, Mulungu akuyankhula kuti: (Kwa munthu amene angafunefune chipembedzo china chosakhala Chisilamu, komwe ndi kugonjera mwa Mulungu pokhulupilira za umodzi wake ndikumatsatira malamulo ake,ndikugwira ntchito zonse zabwino pofuna kusangalatsa iye,komanso kumutsatira mtumiki wake otsiriza Muhammad-mtendere ukhale pa iye-pomukhulupilira mtumikiyo,kumutsatira, ndikumukonda pogwiritsa ntchito zoonesera ndi zobisika, chipembedzo chinacho sichidzalandiridwa tsiku la chiweruzo ndipo adzakhala m'modzi mwa anthu oludza). [Al-Imran: 85].
Chisilamu ndi chipembedzo chokhacho chomwe Mulungu akachilandire tsiku lotsiriza.
Mulungu ndi amene adatilenga, ndipo kwa Iye tidzabwerera, ndipo umoyo wa dziko lino ndi mayeso kwa ife.
Munthu akuyenera kukhulupilira kuti: umoyo uno nthawi yake ndi yochepa ngat m'mene imakhalira nthawi ya maloto....palibe amene akudziwa nthawi yomwe adzamwalire.
Kodi adzayankha chiyani kwa mbuye wake akadzamufunsa tsiku la chiweruzo: chifukwa chiyani sanatsatire chipembedzo choona? chifukwa chiyani sanatsatire m'neneri otsiriza?
Nanga mbuye wako adzayankha motani tsiku lotsiriza?. Kumachita kuti Mulungu wachenjeza zakuopsa kosiya kutsatira Chisilamu ndikumatsatira zinthu zomwe muli kukanira za Mulungu, ndipo wanena kuti anthu okanira mathero awo ndikukalowa ku moto komwe akakhale mpaka kalekale.
Mulungu adanena kuti: (Kwa anthu amene sanakhulupilire ndiponso amatsutsa mau athu, anthu amenewo ndi aku moto komwe akakhale mpaka muyaya). [Al-Baqarah: 39].
Palibe chifukwa chomveka chomwe angapereke munthu amene amasiya kutsatira choona ndi kumatsatira zochita za makolo ake.
Mulungu wapamwamba adatiuza kuti anthu ambiri amakana kulowa Chisilamu chifukwa choopa malo omwe amakhala.
Anthu ambiri amakana Chisilamu chifukwa chosafuna kusintha zikhulupiliro zawo, zomwe adatengera kwa makolo awo kapena adazitenga kuchokera kumalo ndi madera awo omwe amakhala ndiye anazizolowera. Anthu ambiri chomwe chimaletsa kulowa Chisilamu ndi sankho komanso kukhala ndi maganizo oteteza zinthu zolakwika zomwe adazipeza kuchokera kwa makolo awo.
Anthu onsewa alibe chifukwa chomveka pakusiya kutsatira choona, ndipo adzaima pamaso pa Mulungu popanda umboni.
Palibe chifukwa chomveka chomwe munthu osakhulupilira kuti kuli Mulungu angamanenere kuti: ine ndidzapitirizabe kukhala osakhulupilira kuti Mulungu kulibe chifukwa ndinabadwira m’banja losakhulupirira kuti kuli Mulungu!.M’malo mwake, iye akuyenera kugwiritsa ntchito nzeru zake zimene Mulungu adamupatsa,ndikumalingalira za m'mene Mulungu adalengera mitambo ndi nthaka, ndikumakhala ochulutsa kulingalira pogwiritsa ntchito nzeru zomwe Mlengi wake adamupatsa kuti adzindikire zoti dziko amalionali lili ndi Mlengi wake. Chimodzimodzinso munthu amene amapembedza miyala ndi mafano, alibe chifukwa chomveka bwino powatsatira makolo ake popembedza zimenezo. Zomwe zikufunika kwa iye; ndi kufufuza zoona zeni zeni ndikumadzifunsa yekha kuti: zitheka bwanji kuti ndizipembedza chinthu chosagwedezeka chomwe sichimandimva, sichimandiona komanso sichimandithandiza pa vuto lililonse?!
Chimodzimodzinso Mkhirisitu amene amakhulupilira zinthu zosemphana ndi chilengedwe chabwino,nzeru zabwino, akuyenera kumazifunsa yekha: zitheka bwanji kuti Mulungu aphe mwana wake amene sadachite mchimo lililonse, ndikumupha chifukwa cha machimo a anthu ena? uku ndikupondereza kwakukulu!. Zitheka bwanji kuti anthu amupachike pa mtanda ndikumupha mwana wa Mulungu?! Kodi Mulungu mesa ali ndikuthekera kokhululuka machimo a anthu popanda kuwalola anthuwo kuti aphe mwana wake? Kodi Mulungu mesa ali ndikuthekera komuteteza mwana wake?
Choncho, ndi zofunika kwa munthu wa nzreu zabwino kutsatira choona, ndikusiya kuwatsatira makolo ndi azigogo ake pa zinthu za bodza.
Mulungu adanena kuti: (Ndipo akauzidwa kuti: bwerani mutsatire zomwe Mulungu wavumbulutsa komanso zomwe mtumiki adalamulira, iwo amanena kuti: zikutikwanira zomwe tidawapeza nazo makolo athu akuchita. Kodi iwo atsatira za makolo ngakhale atakhala kuti adali osadzindikira kapena sanali pachiongoko). [Al-Maida: 104].
Kodi munthu amene akufuna kukhala Msilamu koma akuziopezera yekha ku mazunzo ochokera kwa abale ake atani?
Munthu amene akufuna kulowa Chisilamu koma akuwaopa anthu omwe amuzungulira, atha kulowa Chisilamu ndi kubisa za Chisilamu chake kufikira Mulungu nthawi yomwe Mulungu adzamupepusire njira yabwino yodziimira pa yekha ndikuonesera zoti iye ndi Msilamu.
Choncho, ndi zofunika kwa munthu osachedwa kulowa Chisilamu,koma sikuti ndi zokakamizidwa kuwauza anthu omwe amuzungulira zakulowa kwake Chisilamu kapena kufalitsa zakulowa kwa Chisilamu zikakhala kuti zimupezesa mavuto.
Ndipo dziwa kuti munthu akalowa Chisilamu, adzakhala m’bale wa Asilamu ochuluka kwaambiri, ndipo angathe kulumikizana ndi akulu akulu apa mzikiti,kapena malo ochitikira za Chisilamu m’dera lakelo, ndi kumawafunsa maganizo komanso thandizo ndipo Asilamu zimawasangalasa zimenezo.
Mulungu wapamwamba mwamba adanena kuti: (Ndipo amene akumuopa Mulungu, amukonzera njira yotulukira m'mavuto. Ndipo amupatsa zosowa za moyo wake kuzera mu njira yomwe sadayembekezere). [At-TAlaq:2-3].
Okondedwa owerenga olemekezeka
Kodi mesa kukondweretsa Mulungu Mlengi - amene watipatsa madalitso ake onse, amene amatipatsa chakudya pamene tinali m'mimba mwa amayi athu ndi kutipatsa mpweya umene tikupuma tsopano - ndi kofunika kwambiri kuposa kukondweretsa anthu kwa ife?
Kodi mesa kupambana kwa pa dziko la pansi ndi moyo umene uli mkudza ndikoyenera kudziperekera nsembe ndi zosangalatsa zonse za moyo wakutha? Inde, ndikulumbira Mulungu!
Choncho,sizoyenera kwa munthu kuti alole zoipa zake zakale zimulepheretse kukonza zolakwika zake ndi kumachita zabwino.
Munthu akuyenera kukhala okhulupirira weniweni lero!ndipo asalole kuti Satana amulese kutsatira choonadi!
Mulungu wapamwamba adanena kuti: (E inu anthu! Ndithudi, wakudzerani umboni wochokera kwa Mbuye wanu ndipo takuvumbulutsirani buku la Quran kukhala lokuwalisiran njira ya choonadi(174) Tsono,anthu amene akhulupirira Mulungu ndikumagwiritsa buku lomwe latumizidwa kwa iwowo, anthu amenewo Mulungu adzawalowesa ku minda ya mtendere kamba ka chisoni ndi ubwino wake, ndipo pa dziko lino la pansi adzawafewesera kuti adzisatira njira yomwe ingakafikitse ku minda ya mtendere tsiku lotsiriza(175). [Al-Nisa:174-175].
Kodi mwakonzeka kupanga chisankho chachikulu kwambiri pa moyo wanu?
Ngati zonse zakambidwazi zili zomveka bwino, ndiye kuti munthu wadziwano zoona mu mtima mwake, choncho, akuyenera kuchita zoyenera kuti akhale Msilamu.
Munthu amene akufuna kuthandizika popanga chiganizo chabwino pa moyo wake, komanso kumusonyeza momwe angakhalire Msilamu.
Asalole kuti machimo ake amulepheretse kulowa Chisilamu. Mulungu watiuza mu Qur’an kuti Iye amakhululuka machimo onse a munthu ngati alowa Chisilamu ndi kulapa kwa Mlengi wake. Ngakhale kuti pambuyo polowa Chisilamu, potengera chibadwa cha munthu,munthu adzidachitanso machimo ena ,ife ndi anthu sikuti ndife Angelo otetezedwa ku machimo. Koma chimene chikufunika kwa ife; ndi kumupempha Mulungu chikhululuko ndi kulapa kwa iye, ndipo ngati Mulungu atationa kuti tafulumira kuvomereza choona ndipo talowa Chisilamu, ndikuyankhula mau ochitira umboni zakuyenera kupembedzedwa kwa Mulungu ndi utumiki wa Muhammad,, ndiye kuti adzatithandiza kusiya machimo ena, ndipo amene walunjika kwa Mulungu,Mulungu adzatithandiza kuti tikwanitse kusiya machimo ena. Munthu amene amavomereza malamulo a Mulungu ndikumatsatira zoona,Mulungu amamupepusira njira zogwilira ntchito zabwino. Choncho, munthu sakuyenera kuchita chidodo polowa chisilamu.
Ena mwa maumboni a izi ndi mau a Mulungu wapamwamba: (Nena kwa osakhulupirira kuti: ngati asiya zochita zawo zoipa, adzakhululukidwa zoipa zimene zidatsogola). [Al-Anfal:38].
Ndichite chiyani kuti ndikhale Msilamu?
Kulowa m’Chisilamu ndi chinthu chophweka ndipo sichofunika kuchita miyambo, ndondomeko zapadera, kapena kupezeka kwa wina aliyense. Koma munthu angonena mau ochitira umboni (Shahada) uku akudziwa matanthauzo ake, ndikuwakhulupirira, ndipo anene kuti: (Ndikuikira umboni kuti palibe wina wopembedzedwa mwachoonadi koma Allah, ndipo ndikuikira umboni kuti Muhammad ndi Mtumiki wa Allah), ngati kuli kotheka kwa inu kuti munene mu Chiarabu, ndizabwino, ndipo ngati kuli kovuta kwa inu, kukukwanirani kulankhula muchilankhulo chanu, ndipo motero udzakhala Msilamu, Kenako uyenera kuphunzira chipembedzo chako, chomwe chidzakhala gwero lachisangalalo chako pa dziko lapansi ndi chipulumutso chako ku moyo wosatha.
Kuti mumve zambiri za Chisilamu, ndikulangizani kuti mupite patsamba lino:
Kuti mudziwe momwe mungachitire malamulo a Chisilamu, tikukulangizani kuti mulowe pa tsamba lino:
Related books
All books
Ndani adandilenga? Nanga chifukwa chiyani?75 languagesNdani adandilenga? Nanga chifukwa chiyani?
Cholengedwa Chili chonse chimasonyeza kupezeka kwa Mlengi. Ndani adalenga kumwamba ndi dziko la pansi ndi zolengedwa zikuluzikulu zomwe zili mkati mwa ziwirizi zomwe sizimadziwika? Kodi ndi ndani adaika ndondomeko yokuya ndi yolongosoka bwino yakayendedwe ka zinthu kumwamba ndi dziko lapansi? Kodi ndani amene adalenga munthu ndikumupatsa makutu, maso, ndi nzeru? ndikumpatsa kuthekera kophunzira ndikudziwa zoona? Kodi mungafotokoze bwanji ndondomeko yodzama ndi yokuya ya momwe Mulungu adaikira ziwalo zapa thupi lako komanso ziwalo za zinthu za moyo? ndani adalenga zimenezo? Kodi dziko…
CHISILAMU89 languagesCHISILAMU
M'dzina la Mulungu ,Wachifundo Chambiri ,Wachisoni Chosatha. Kodi unayamba wazifunsa wekha? Kodi ndi ndani amene adalenga mitambo ndi nthaka,komanso zolengedwa zazikulu zikupezeka ku mitambo ndi pansi pa nthaka? Kodi ndani adapanga ndondomeko yokuya ndi yokonzedwa mwa ukadaulo?
Njira zothandiza za moyo wachimwemwe85 languagesNjira zothandiza za moyo wachimwemwe
Buku lofotokoza za njira zothandizira kukhala umoyo wa chimwemwe lolembedwa ndi Sheikh Abdul-Rahman bin Nasir as-Sa'die, limafotokoza mozama njira zobweresera chisangalalo chenicheni kuchokera pa mawonedwe a chikhulupiliro chozama; ndipo limatsogolera owerenga ku bata la mtima kudzera mu chikhulupiliro ndi ntchito zabwino, kukumbukira Mulungu, kukhutira, kusinkhasinkha za madalitso, kuchita ubwino, kuyezamira mwa Mulungu, kuleza mtima, ndi kuzindikira moyenera kufunika kwa zinthu. Mu kalembedwe kokongola, limayika pamaso panu kalozera wa moyo wamtendere, wolinganizika, komanso wosangalala…
الإسلام دين رب العالمين