وهذهِ رِسالَةٌ مُوجَزَةٌ لَكَ يا مَن فَقَدتَ قَرِيبًا أو عَزِيزًا، أو حَبِيبًا، نَسألُ اللَّهَ عزَّ وجلَّ أن ينفعنا وإياكَ بِها، وهي بِعنوان: (أحكامُ الجَنائِز).
Cholengedwa Chili chonse chimasonyeza kupezeka kwa Mlengi. Ndani adalenga kumwamba ndi dziko la pansi ndi zolengedwa zikuluzikulu zomwe zili mkati mwa ziwirizi zomwe sizimadziwika? Kodi ndi ndani adaika ndondomeko yokuya ndi yolongosoka bwino yakayendedwe ka zinthu kumwamba ndi dziko lapansi? Kodi ndani amene adalenga munthu ndikumupatsa makutu, maso, ndi nzeru? ndikumpatsa kuthekera kophunzira ndikudziwa zoona? Kodi mungafotokoze bwanji ndondomeko yodzama ndi yokuya ya momwe Mulungu adaikira ziwalo zapa thupi lako komanso ziwalo za zinthu za moyo? ndani adalenga zimenezo? Kodi dziko…
CHIKAKAMIZO CHOGWIRITSA NTCHITO SUNNA ZA MTUMIKI(SAW)NDIKUKANIRA KWA MUNTHU YEMWE ANGAZIKANE SUNNAZO.
23 languages
CHIKAKAMIZO CHOGWIRITSA NTCHITO SUNNA ZA MTUMIKI(SAW)NDIKUKANIRA KWA MUNTHU YEMWE ANGAZIKANE SUNNAZO.
WOLEMBA BUKU: ABDUL AZIZ BIN ABDUL ALLAH BIN BAZ(ALLAH AWACHITIRE CHISONI). M'dzina la Mulungu ,Wachifundo Chambiri ,Wachisoni Chosatha. MAU OYAMBA Kuyamikidwa konse ndikwa Mulungu, mbuye wa zolengedwa zonse, ndipo mathero abwino pa chinthu chilichonse amakhala kwa anthu oopa Mulungu, mtendere ndi madalitso a Mulungu zikhale pa kapolo komanso mtumiki wake,mneneri wathu Muhammad; amene anatumizidwa kuti akhale ozichitira chisoni zolengedwa zonse,komanso mtendere ukhale kwa anthu aku banja kwake,ophunzira ake anthu amene anatenga uthenga ochokera mu buku la mbuye wawo pamodzi ndi…
M'dzina la Mulungu ,Wachifundo Chambiri ,Wachisoni Chosatha. Kodi unayamba wazifunsa wekha? Kodi ndi ndani amene adalenga mitambo ndi nthaka,komanso zolengedwa zazikulu zikupezeka ku mitambo ndi pansi pa nthaka? Kodi ndani adapanga ndondomeko yokuya ndi yokonzedwa mwa ukadaulo?
Chitsanzo chachidule cha m'mene tingapangire Swalah, kuti tipembedze Allah momvetsa bwino, ndi kuti Swalah yathu ikhale yokwanira nsichi ndi malamulo ake. Kapempheredwe ka Swalah Tikafuna kuswali tiyenera kudziyeretsa kuchokera ku umve wa ung'ono ndi waukulu. Ndipo tipemphere ndi zovala zoyera komanso zophimba maliseche athu. Ndipo matupi athu ndi malo opempherera zikhale zoyeretsedwa ku nyasi. Tiyang'ane ku Qiblah Ndipo ndi bwino kupemphera pamalo pomwe pali chotchinga.