رسول الإسلام محمد صلى الله عليه وسلم
Mu lina lya mlungu msyene chanasa chakwendelechela pa yagumbidwa yosope pa dunia pano,nambo soni chanasa chitakatendele wandu wakumkulupilila jwelejo lyuwa lya qiyama Mtume jwa dini ja chisilamu Muhammad -chanasa ni utendele wa mlungu ijaule kwa jwelejo. Mbiri ya chidule ya mtumiki wa chisilamu Muhammad mtendere ndi madalitso zipite kwa iye,ndipo nkatikati mwa mbiri yake ndikulongosola za dzina lake fuko lakemalo amene anabadwila komanso ndima banja ake chivumbulutso chake chomwe anabwela nacho kuyitanila kwake ku zinthu zomwe anabwela nazo zizindikilo za utumiki wake malomulo ake komanso…
These files are generated automatically from the book's text; their layout may differ from the printed edition.
Mu lina lya mlungu msyene chanasa chakwendelechela pa yagumbidwa yosope pa dunia pano,nambo soni chanasa chitakatendele wandu wakumkulupilila jwelejo lyuwa lya qiyama
Mtume jwa dini ja chisilamu Muhammad -chanasa ni utendele wa mlungu ijaule kwa jwelejo.
Mbiri ya chidule ya mtumiki wa chisilamu Muhammad mtendere ndi madalitso zipite kwa iye,ndipo nkatikati mwa mbiri yake ndikulongosola za dzina lake fuko lakemalo amene anabadwila komanso ndima banja ake chivumbulutso chake chomwe anabwela nacho kuyitanila kwake ku zinthu zomwe anabwela nazo zizindikilo za utumiki wake malomulo ake komanso ndikutambasula za anthu amene ankasutsana naye iye . [1]Ndayesetsa kuti ndizigundanitsa zina la utumiki ndi la Muhammad kuti pomasulirazisamakhale kuti zikusephana pofuna kuti ziziziwika kuti ndikunena mtumikiMuhammad.
1-Dzina lake fuko lake komanso ndi malo ameneanabadwira ndi kukulira
Mtumiki wachisilamundi Muhammad mwana wa Abdullah mwana wa Abdul Mutwalib,mwana wa Haashim mwana wa fuko la Ismaeliye ndi mwana wa Ibraheem mtendere ukhale kwa iye. Mtimiki wa Allah Ibraheem anachoka ku shami kupita ku Makka (yomwe pano ili syria)anali ndi nkazi wake Haajira ndi mwana wake Ismael panthawiyo Ismael ali mwana wa nchikuta ndiye anawasiya ku makah pachilamulo cha Allah pamene Ismael anasunduka mnyamata Ibraheem anabwela ku Makkah ndipo anamanga kaba nyumba yolemekezeka iye pamozi ndi mwana wake uja Ismael ndipo anthu anachuluka oyizungulira nyumbayi ndipo makka inasundula kopita anthu kukapanga mapephero kwa Allah mwini zolengedwa zonse.amene afuna kukapanga hajj ndipo anthu anapitilira kupanga mapephero amenewa mu omozi wa Allah mu njira imeneyi ya Ibraheem mpaka zaka zaka Kenako anthu anasintha makhalidwe ndipo anasiya kutsatila njira ya Ibrahim,ndiye anasanduka ma arabs kukhala ngati wina aliyense wa madela ena apa dziko lapasi,ndipo unawonekela nkhailidwe opembeza mafano kukwilira ana kwapondeleza azimayi,kunama poikila umboni, kumwa mowa,chiwelewere,kudya chuma chamasiye kutenga katapila.... Pa malo amenewa komanso ndikhalidwe lake limeneli ndiye ndi nthawi yomwe anabadwa mtumiki wa chisilamu Muhammad mwana wa Abdullah kuchokela ku fuko la Ismael mwana wa Ibraheem mtendele upite kwa iye,mu chaka cha 571, Bambo ake anamwalira iye asanabadwe,ndipo mayi ake anamwalira chaka cha 6 ,ndiye kenako anamulela amalume ake,ndipo anali wa masiye komanso wausiwa,ndipo amadya kuchokela mu ntchito za manja ake.
2-Banja lake lolemekezeka ndi mzimayi olemekezeka.
Pamene dzaka zake zidakwana 25,anakwatila mzimayi olemekezeka mwa azimayi apa makka amene ali Khadija mwana wa khuwailidi Allah asangalale naye, ndipo anapasidwa mwayi wa ana atsikana anayi ndi ana achimuna awiri,ndipo ana onse anamwalira ali achichepele, ndipo khalidwe lake kwa nkazi wake ndi banja lake linali labwino loleza mtima ndilachikondi,pachimenecho anamukonda nkazi wake kwambiri ndipo iye nayeso anabwezela kumukonda khadija ndipo sanamuyiwale ngakhale pambuyo poti wamwalira ankazinga mbuzi ndikuyigawa swadaqa m'malo mwa khadija pomulemekeza ndikusunga chikondi chake pomuchitila zabwino
3-Chiyambi cha chibvumbulutso (Quran)
Mtumiki anali ndimakhalidwe abwino kuyambila chimulengeleni Allah,ndipo anthu ake ankamutcha kuti oyankhula zoona komanso wachilungamo,akasungitsidwa zinthu,komanso ankagwilira limozi ntchito ndi zikulu zikulu ndi anthu,komanso amanyasidwa ndi khalidwe la anthu lopembeza ma fano,ndipo samapanga nawo zimenezo.
Pa nthawi yomwe anakwanitsa dzaka 40 ali ku makkah Allah anamusankha kukhala mtumiki anamubwelela ngelo Jibriel mtendere upite kwa iye anamubwelela ndi surat yoyamba mu Quraan amene ali mawu Allah oti : 1-(Welenga dzina la mbuye wako amene adakulenga) 2-(Anawumba mynthu kuchokela ku magazi oundana). 3-(Welengani ndipo ziwani kuti mbuye wanu alibe ofanana naye.). 4-(Mulungu wake amene waphunzitsa munthu ndi cholembera). 5(Amuphunzitsa munthu zomwe sanali kuziziwa). [Suratu Al A'laq:1-5] kenako mtumiki anabwelera kwa nkazi wake amene ali khadija Allah asangalale naye ali ndi mantha mtumiki mu mtima mwake,ndiye anamulongosolera nkhani ija zokhuzana kutsika kwa chivumbulutso,ndiye Khadija anamukhazikitsa mtima pansi, kenako khadija anamutenga mtumiki kwa mwana wa amalume ake amene anali Wraqa mwana wa Nufair ndipo anali nchristu woti amatha kuwelenga baibulo ndi chipangano cha kale (tora)ndiye khadija adanena kwa Nufair kuti ee iwe mwana wa amalume tanva zomwe akuyankhula mwana wa m'bale wako uyu,ndiye Waraqa ananena kuti Kodi iwe mwana wa m'bale wanga ukuwona chani? kenako mtumiki anafotokoza nkhani yonse zomwe adawona ndiye Waraqa ananena kuti: Ameneyu ndi mngelo amene anatumizidwansokwa Mussah koma ndikudandaulachifukwa cha ukalamba ndikudandaula zikanakhala kuti ndizakhalapo pamene anthu ako azizakuthamangitsa,ndiye mtumiki anati Kodi anthu azandithamangitsa anati inde ,palibe amene anabwela ndi zangati zomwe wabwela nazo iwe anthu ake ndikusamuda ayi, .[2] (2)Hadeeth imeneyi anagwirizana Imam Bukhari ndi Imam Muslim, mu hadeeth ya Aisha Allah asangalale naye mu Bukhari ili number 7/1/(2)pamene mu muslim ili pa 139/1/(152)
Ali ku MakkaQuraan inkatsika mondondozana ndipo imatsika podusila kwa Jibriel mtendere wa Allah mwini zolengedwa zonse upite kwa iye,ndipo monga mmene ankabweletsela malamulo otambasula bwino awuthenga wa chivumbulutso .
Ndiye anali akwaitanila anthu ake(ma Quraish) ku chipembezo cha chisilamu koma iwo anamuda ndi kukangana nayendipo kenako anamuwuza kuti asiye kuyitanila mwa Allah ampatsa ufumu ndi chuma koma mtumiki anakana zonsezondipo ndiye anamuwuza zinthu ngati mmene anthu akale ankawawuzila atumiki awo kuti mfiti wabodza wopeka zinthu ndiye anaupanga umoyo wake kukhala othina komanso anampatsa zopweteka pathupi pake ndikwavutitsa omutsatila akenso. Panthawi yomwe mtumiki analiku makkah ankaitanila anthu kwaAllah maka maka nthawi ya Hajj komanso ndi nthawi ya misika ya arabsamakumana ndi anthu mmenemo ndikumawalongosolela za chisilam ndipo sanafune zinthu zapazikokapena udindo ayi ndipo sanaope mpaliro,analibe udindi ngakhale ufumu,ndipo kumayambiliro kwa kuitanila kwakwe anawauza anthu kuti abweletse quraan yofanana ndi yomwe iye wabweletsa ndipo anapitiliza kulimbana ndi anthu amene ankamusutsa,ndiye anakhulupilira kwa amene anakhulupilira mwa maswahaba ake Allah asangalalenawo onse .
Panthawi imene anali ku makka mtumiki Allah anamulemekeza ndi chizindikilo chachikulu kwambiri umene uli ulendo omwe anayenda kupita kubaiti maqdasi kenako ananyamuka waku mwamba ndipo zomwe zili zoziwika ndi zoti Allah anamunyamula kupita ku mwamba ngati m'mene anamunyalila Iliyas ndi Issah mtendere ukhale kwaiwo ngati mmene zinafotokozeledwa kwa asilamu ndi achrisitu. Pamene mtumiki anali kumwambako analandila lamulo la swallah imeneyi ndiye swallah yomwe lero lino asilamu amapephera kasanu pa tsiku komanso ali ku makkah kunachitika chinthu chachikulu kumene kuli kugawikana kwa mwezi mpkana anthu opembeza mafano anawona nawo zimenezi.
Anthu okanila ochokela mwa ma Quraish anayesetsa njira zosiyana siyana kuti alimbane ndi mtumiki kwaletsa anthu kuti asatsatile komanso kuwathamangitsa kuti asayandikile kunvela zokamba za mtumiki,ndikumampnga kuti abweletse ma umboni kuti iye ndi mtumikidi wa Allah ndikumapepha ayuda kuti awanthandize ndi maumboni omusutsila mtumiki komanso kwaletsa anthu kuti asafike kwa iye.
Panthawi imene anthu okanila mwa Allah ochokela mwama quraish anapitiliza kumuvutitsa mtumiki ndi anthu okhulupilira mtendere ndi madalitsozipite kwa iye, anawalamula kuti asamukile ku habasha,ndipo anawawuza kuti kumeneko kuli mfumu yachilungamo simapondeleza wina aliyense mwa inu,ndipo anasamuka magulu okwanila awiri kupita ku habasha pamene ma swahaba anafika ku habasha anamuziwitsa mfumu ija za chisilamu chomwe chinabwela ndi mtumiki ndipo analowa chisilamu ndiye anati,ndithu ndikulumbila zomwe zabwela ndi Muhammad ndiza Mussah zachokela malo amozi kenakokenako mavuto anayamba kubwela mondondozana kwa anthu ake ndi ophunzira ake
Mwa anthu amene analowa chisilamu nthawi ya Hajj ndikagulu kamene kanabwela kuchokela ku madina ndiye anapanga malonjezo ndi mtumiki kuti azamuteteza ngati atasamukila ku madina kumene panthawiyo kunkatchedwa kuti Yathribu,ndiye mtumiki anawalamula amene anatsala ku makka kuti asamukile ku madina ndipo anasamukila,ndiye chisilamu chinafalikila ku madina mpakana sikunatsale nyumba yomwe chisilamu sichinalowemo
Pambuyo poti wakhala mu makkah dzaka makumi awiri ndi zitatu akuyitanila mwa Allah kenako Allah anamulamula zosamuka kupita ku Madina ndipo anasamuka ndipo anakapitiliza kuyitanila nawo malamulo anali akupitiliza kutsika lamulo pambuyo palamulo,ndiye kenaako anayamba kutumiza ma uthenga kwa azitsogoleli ndi mafumu kwaitanila ku chisilamu ndipo mwa ena amene anawatumizilandi mfumu ya ku Romu mfumu yaku persia pano ndi Iran komanso mfumu yaku iguputo(Eygpt
Ali ku Madina kunachitika kadansana ndipo anthu anawopakwambiri,ndipo zimenezi zinachitika tsiku lomwe anamwalira mwana wa mtumiki Ibraheemmtendere ndi madalitsozipite kwa iye mtumiki ndiye anthu ankanena kuti izi zachitika chifukwa cha infa ya mwana wa mtumiki ndiye mtumiki ananena kuti: (Ndithumwezi ndi dzuwa sizimakumana chifukwa cha infa ya wina aliyense ayi kapena chifukwa cha moyo wake koma zimenezi ndi zizindikilo za Allah zimene Allah amawopyezela akapoplo ake)[3]. Zikanakhalakuti mtumiki anali wabodza poyitanila pake ndiye kuti akanatengela mwayi wa kadansana ameneyi ndi kuwawuza anthu kuti zachitika chifukwa cha infa ya mwana wake ndipo akananena kuti zachitika izi chifukwa cha infa ya mwana wanga nanga kuli bwanji inu amene mukundisutsa ine.
Mulungu anamukongoletsa mtumiki ndi makhalidwe abwino okwanila,ndipo anamulongosola ndi mawu ake oti: (Ndithu iwe Muhammad uli ndi makhalidwe abwino). [Suratu Al Qalam:4] Mtumiki ankaziwika ndi mbiri zabwino monga ngati kuyankhula zoona kuziyeletsa mwa Allahmphavu chilungamo kukwanilitsa malonjezo angakhake ndi anthu oti sakugwilizana nawo kuwolowa manja,ankakondanso kupeleka kwa ovitika ndi ovutikitsitsa azimayi amene asiyidwa ndi amuna awo ndi anthu onse amene ali ofunika nthandizo amayesetsa kuwawongolela ndikwapangila chisoni kuzichepetsa kwa anthu mpakana zimapezekakuti munthu wachilendokubwela akumufuna mtumiki koma osamuziwa chikhalilenicho ali pompo mpka amafunsa kuti kodi Muhammad ndi ndani apa?
Mbiri ya mtumiki chinali chisonyezo chakukwanila kwa makhalidwe ake pakakhalidwe kake ndi anthu onse popanda kusiyanitsa mdani wake mzake,oyandikana nawo apatali,wankulu mwana mamuna mzimayi,zinyama mbalame.
Pa nthawi yomwe Allah anakwanilitsa chipembezo chake kwa mtumiki,ndipo mtumiki naye nafalitsa uthenga wake mmene umafunikila,kenako anamwalira mtumiki ali ndi dzaka makumi asanu ndi limozi kuza zitatu 63,ndipo dzaka makumi anayi ndizomwe anakhala asanalandile utumiki,ndipo dzaka makumi awiri ndi ziwiri atalandila utumiki komanso uthenga. Anaikidwa ku Madina mtendere ndi madalitso apite kwa ndipo sanasiye chuma kapena katundu oti anthu agawane,kupatula ngamila yake yoyela yomwe ankakwela,ndi nthaka yomwe anasiya kwa anthu apa ulendo ngati chopeleka.[4] [4]Sahih Bukhar (4461), 6/15. [3] Sahih Muslim-Buku la Imaam Muslim -nambala ya hadith mu bukumo (901).
Anali anthu ambiria amene analowa chisilam ndikutsatila ndipo anapanga nawo Hajj yomaliza ena mwa iwo okwana100 sauzand ndipozinali patangokhala miyezi 13 kuti amwalire mwinanso zimenezi ndi zina mwa zinsisi zimene zinapangitsa kutideen ifalikile ndipo anali ma swahaaba amene mtumiki anawaphunzitsa chikhalidwe cha chisilamu maswahaab abwinoachilungamo ozichepetsa ndi odekha okwanilitsa malonjezo ozipeleka pa deen imeneyi.
Mwa ophunzira ake amene anali achikhulupiliro oziwa ogwira ntchito potsatila malamulo oziyeletsa mwa Allah achilungamo ozipeleka amphabvu komanso aulemelero ndi Abubakar,swidiq Umar khatwaab,,Uthmaan Affan,Aliy bin Abi Twaalib Allah asangalale nawo onsewo,amenewo ndiye anali oyambilira kulowa chisilamu ndikuvomeleza ndi amenenso ali ma khulafaau pambuyo pake,amene anatenga utsogoleli wa deen pambuyo pake,koma analibe kalikonse kokhuzana utumiki ayikoposa ma swahaab ena onse Allah asangalale nawo onsewo.
Mulungu anasunga buku lake lomwe anabweletsa iye mtumiki pamozi ndi sunnah zake,mbiri zake zoyankhula zake zochita zake muchiyankhulo chomwe iye anayankhula,siyinasungike mbiri potengela nthawi ayi ngati mmene inasungigwila mbiri yake mtumiki koma zinasungidwa ngakhale mmene ankagonela kudya kumwa ndi kuseka Kodi mtumiki ankakhala bwanji ndi akunyumba ake nkati mwa nyumba yake? Khalidwe lake lonse mtumiki linasungidwa ndikulembedwa mu mbiri zake ,ndipo iye anali munthu mthenga analibe kalikonse kokhuzana umulungua ayi,komanso analibe kuthekela kozipatsa zabwino kapena zoipa.
4-UTHENGA WAKE
Mulungu anatumiza mtumiki Muhammad mtendere ndi madalitso zipite kwa iye pambuyo poti shirk kumphatikiza mulungu kunali kutafalikila ukafiri ndi umbuli pa dziko lapasi, ndipo palibe amene ankapembeza Allah mwachoonadi kupatula anthu ochepa kwambiri mwa achrisitu,kenako Allah anatumiza mthenga wake Muhammad mtendere ndi madalitso apite kwa iye kukhala mtumiki womaliza anamutumiza ndichiongoko komanso chipembezo choona kwa anthu onse kuti chikhale choonekela kwa zipembezo zonse kwatulutsa anthu ku mdima wa mafano ukafiri ndi umbuli kupita ku umozi wa Allah ndi chikhulupiliro,komanso uthenga wake unali okwanilitsa mma uthenga onse amene anabwela azitumiki ambuyomu mtendere ukhale kwa iwo .
Anaitanila kwa zonse zomwe ankaitanila atumiki ndi azithenga wonse mtendere ukhale kwa iwo monga Nuhu Ibrahim, Musssah, Sulaiman Daudi, ndi Issah mu chikhulupiliro kuti Allah ndiye mbuye amene ali mulengi opeleka moyo ndi infamfumu yama fumu,amene amayendetsa kalikonse iye ndi wantendere komanso wachisoni,iye ndi amene analenga kalikonse komwe kalipa dziko pano kamene timakawona ngakhalenso kamene sitimakaona ndipo kupatula Allah kalikonse ndi kolengedwa mu zolengedwa zake .
Ngati m'mene anaitanilira zopembeza mlungu mmozi yekha ndikusiya kupembeza zina posakhala iye ndipo analongosola mapeto akulongosola,kuti Allah ndi m'mozi yekha pakupembezedwa paumulungu wake pakulenga pake komanso pakayendetsedwe,ndipo analongosola kuti Allah sanabeleke komanso sanabelekedwe,ndipo alibe ofanana naye komanso olingana naye,ndipo samalowa mwa wina aliyense mu zolengedwa zake komanso samakhala ndi mawonekedwe anthupila wina aliyense
Ndipo amaitanila kuchikhulupiliro cha mabuku onse omwe anatumizidwa kuchokela kwa Allah monga ngati suhf Ibrahim ndi Mussah mtendere upite kwa iwo,tora zaburi komanso ndi Injiri,ngatinso mmene anaitanila za kukhulupilira za atumiki onse mtendere ukhale kwa iwo,ndipo munthu amene angakanile mwa mtumiki mmozi mwa iwo ndiye kuti amatenga kuti wakanila atumiki onse.
Ndipo mtumiki amawasangalatsa anthu powawuza za chisoni cha Allah,kuti Allah ndi amene amayang'anila iwo pa dziko lapansi,komanso iye Allah ndiye mbuye wa chisoni,iye yekha ndi amene angazawelengetse zolengedwa zake pa tsiku la chiweluzo pa nthawi yomwe zonse zizawukitsidwe mmanda ndipo iye ndi amene azalipile anthu okhulupilira zabwino zawo kuyambila 10 ,ndipo choipa kuyambila chimozi ndipo ali ndi mtendere okhazikika ku mwamba ndipo yemwe angakanile ndikugwira ntchito yoipa amapeza malipilo ake oipawo pa dziko pano komanso ku mwamba.
Mthenga wa Allah Muhammad mtendere ndi madalitso zipite kwa iye mu uthenga wake sankazitamanda iye mwini kapena mtundu wake kapena mzinda wake ayi ,ndipo mu Quraan mwatchulidwa maina azitumiki ena monga Nuhu Ibrahim Mussah Issah,mtendere upite kwa iwo amenewa atchilidwa kwambiri mu Quraan kuposa dzina lake iye Muhammad,ndipo dzina la mayi ake silinatchulidwe ayi,angakhale maina azikazi ake koma zina la mayi ake a Mussah latchulidwa koposa kamozi ndipo ndzina la Marium latchulidwa kokwana ka 35.
Mthenga wa Allah Muhammad mtendere ndi madalitso xipite kwa iye anali otetezedwa ku zinthu zomwe zili zosephana ndi malamulo mzeru,komanso chilengedwe,kapena zimene makhalidwe abwino amakana chikukwa atumuki ali otetezedwa ku zimene amalalikila zochokela kwa Allah poti amalamulidwa kufalitsa uthenga wa Allah kwa akapolo akendipo atumiki alibe kena kalikonse kokhuzana umulungu ayi kapena kupembezedwa ayi,koma kuti iwo ndi anthu ngati mmene alili munthu wina aliyense koma Allah amatumiza chivumbulutso kwa iwowo .
Mu zunthu zina zikulu zikulu zosonyeza kuti chivumbulutso cha Muhammad ndi cheni cheni chochokela kwa Allah ndiye kuti mpaka lero chidakalipo ngati mmene chinalili kale mu nthawi ya umoyo wake ndipo anthu ambri oposa million ndi amene akutsatilapogwilitsa ntchito malamulo amenewa monga swallah zakaat,swaumu,Hajj. ndi zina mwa izo popanda kusintha kapena kutembenuza
5-Zizindikilo za utumiki wake komanso zisonyendi maumboni ake.
Mulungu ankamulimbikitsa mtumiki wina aliyense ndi zithu zozwizwitsa zosonyeza utumiki wake zomwe zimasonyeza ndikuyikila umboni za uthenga wake,ndipo Allah anapeleka kwa mtumiki wina aliyense zisonyezo zokwanila kwa anthu kuti amukhulupilire, mwa chisonyezo chachikulu chomwe anampatsa mtumiki Muhammad mtendere ndi madalitso zipite kwa iye ndiye Quraan chimenecho chizindikilo chomwechilipo mpaka tsiku la qiyama ngatinsommene anampatsila zizindikilo zina zozwizwitsa zikulu zikulu monga izi :
Ulendo umene anayenda mtumiki kupita ku Jelusalemu mu usiku umozi komanso kumwamba,kugawikana kwa mwezi kukhala magawo awiri kugwa kwa nvula pambuyo poti mtumiki wapepha nthawi yoti kunalibe nvula
Chukulukitsa kwa chakudya ndi madzi mpakaanthu ambiri kudya ndi kumwa ndikutsalanso
Kulongosola zinthu zakalekale zimene sizinkaziwika kwa wina aliyense,amaziwa iyepouzidwa ndi mulungu,ngati nkhani za azitumiki mtendere ukhale kwa iwo ndi anthu awokomanso ndi nkhani ya anthu ameneanaliku mphanga (aswihaabul kahafi)
Kufotokoza mtumiki zinthu za msogolo zizachitike pambuyopoti iye wawuzidwa ndi Allah ngati kuuzidwa kuti moto uzatuluka ku nthaka ya Hijazi ndipo anauwona amene anali ku shami ndikupikisana anthu kumanga manyumba
Chisamaliro cha Allah kwa mtumiki ndikumuteteza kwakwe ku ziwembu za wanthu
Zimenezi zinachitika ngati mmene adayakhulira mtumiki mmawu ake: (Nthawi ikubwela imene muzagonjetse mzinda wa romu ndi persia ndipo zagwilitseni ntchito zimene muzapeze mmenemo mu njira ya Allah)
Kunthandizika kwakwe ndi angelo kuchokela kwa Allah
Kuyankhula kumene anayankhula azitumiki kwa anthu awo zokhuzana kubwela kwa mtumiki Muhammad mtendere ndi madalitso apite kwa iye, ndipo mwa omwe anaynkhula izi ndi Mussah Daudi Sulaiman komanso ndi Issahmtendere wa Allah upite kwa iwo,ndi enanso mwa atumiki ochokela ku ma ban Islael
Mwa ma umboni ena ochokela ku mzeru komanso ndi zitsanzo zomwe anapeleka Allah zomwe zimagwirizana ndi nzeru zabwino bwino (5)Ngati mawu Allah wapamwamba (Ee inu anthu chapelekedwa chitsanzo ndipo chinveleni,ndithu anthu amene amamphembeza wina posakhala Allah sangathe kulenga ntchenje,ngakhale atati asonkhane pa icho komanso ngakhale ntchenjeyo itawalanda china chake sangakwanitse kuti ayilande ndithu ali ofooka onse opepha komanso opephedwa.
Izizi ndiye zizindikilo ndi zitsanzo zogwilitsa ntchito nzeru zilipo zambiri mu quraan yolemekezeka komanso mu sunnah za mtumiki ndipo ma umboni ake ndi ambiri osawengeka ndipo amene akufuna kuziwa za izi akuyenela kubwelela ku quraan ndi sunnah komanso mu mbiri za mtumiki chifukwa mma buku amenewa muli nkhani za nzeru zotsimikizika za ma ayah amenewa.
Zizindikilo zimenezi zikanatizisachitike ndiye kuti anthu amene amasutsa za utumiki wake ochokela kwa ma kafiri achi quraish komanso ayuda ndi achrisitu aku chilumba cha ma arabs akanapezelapo mwayi omukanila mtumiki ndikwauza anthu kuti asamutsatile. .
Quraan yolemekezeka limeneli ndiye buku lomwe Allah anavumbulutsa kwa mtumiki Muhammad mtendere ndimadalitso zipite kwa iye,ndimawu ambuye wazolengedwa zonse,ndipo Allah anawatchalenga anthu ndi ziwanda kuti abweletse yofanana nayo kapena sura imozo komanso amatchalenjabe mpaka tsiku lalero,Quraan yolemekezeka imayankha mafunso ambiri amene amazunguzika nawo anthu,Quraan inasungika mu chiyankhulo chake cha arabic yomwe inatsikila ndipo simunapungulidweangakhale liwu limozi inatsindikisidwa ndikugawiga ili ndi buku lolemekezeka lozwizitswa,ndi buku lalikulu lomwe linatumizidwa kwa anthu ndiye kofunika kuyiwelenga komanso kuwelenga matanthauzo ake ndiye munthu amene kumudutse kuwelenga buku limeneli ndi kukhulupilira ndiye kuti waluza zinthu zabwino kwambiri Ngati masunnah amtumiki Muhammad ntendele ndi madalisto zipite kwa iye chiongoko chake mbiri yake zinalembedwa ndikusungidwa ndipo zimatengedwa kuzela kwa anthu okhulupilika ndipo zinalembedwa muchiyankhulo cha charabu chomwe ankayankhula mtumiki Muhammad mtendere ndi madalitso zipite kwa iye kukhala ngati ali nafe pakati pathu ndipo zamasulidwa mu ziyankhulo zosiyana siyana Quraan ndi sunnah ndiye ma buku awiri amene mumachokela malamulo achisilamu .
6-Malamulo amene anabwera ndi mtumiki Muhammad mtendere ndi madalitso zipite kwa iye
Malamulo amene anabwela ndi mtumiki Muhammad mtendere ndi madalitso zipite kwa iye ndi malamulo achisilam ,ndiye ndi omaliza mwa malamulo ochokela kwa Allah komanso uthenga ochokole kwa Allah ndipo ndi ofanana chiyambi chake ndi ma uthenga onse amene anabwela ndi atumiki akale ngakhale zitasiyana kapangidwe kake.
Amenewa ndi malamulo okwanila ,amene amagwilizana ndinthawi zonse komanso malo alionse amene ali ndi chikhonzelo cha chipembezo cha anthu ndi umoyo wawo wa dziko lapansi,Komanso muli ma pepheleo onse amene aliokakamiza kwa munthu kuti awachite kwa mbuye wake mwini zolengedwa zonse, monga ngati swallah zakat komanso amalongosoloza kachitidwe ka malonda aza chuma komanso za chikhalidwe cha pa gulu ndale ndi nthawi ya nkhondo komanso zikhalidwe zomwe zili zoletsedwa ndi zovomelezeka ndi zina mwa izo zofunika pa moyo wamunthu
Malamulo amenewa masunga zipembezo za anthu magazi awo ulemelelo wawo chuma chawomzeru zawo komanso ana awo malamulo achisilamu amalamulira kalikonse kabwino ndi ubwino,komanso amachenjeza ku kalikonse koipa ndi konyansa,malamulo amenewa amaitanila ku chithu chopeleka ulemelelo ndikukhala munthu wabwino wachilungamo oziyeletsa mwa Allah waukhondo wokhulupilila wa chikondi wokonda za bwino kwaanthu kuteteza magazi komanso kubweletsa mtendere, ndikuletsa kwawopyeza anthu popanda chifukwa ndipo anali mtumiki mtendere ndimadalitso apite kwa iye,anali akulimbana ndi anthu amene anali odupha malire owononga,kwa mtundu uliowonsewo komanso ankasutsana ndi zinthu zongoganiza komanso umoyo wokhala pa wekha ngati ansembe amene samakwatila
Mthenga Muhammad mtendere ndi madalitso zikhale kwa iye analongosola kuti Allah analemekeza munthu wina aliyense mamuna ndi nkazi ndipo anapasa ufulu zina zonse zomwe afuna kusankha pa ntchito komanso amakhala ndi udindo wantchito yabwino kwa iye kapena kwa wina ndipo anapanga wina aliyense mamuna ndi nkazi kukhala chimozi mozi pa chikhulupiliro malipilo azabwino ndi zoipa aliyense alinazo ufulu yekha,malamulo amenewa amateteza mwapadela azimayi,kholo la munthu kaya ndi nkazi kaya mwana wachitsikana mchemwali onsewo.
Malamulo amene anabwela nawo mtumiki Muhammad mtendere ndi madalitso zipite kwa iye anabwela kuzasunga mzeru ndikuletsa kalikonse koononga nzeruzo ngati kumwa mowa chisilamu chinatenga chipembezo kukhala kuwala kounikila nzeru njira yake,kuti munthu azitha kupembeza mbuye wake mwa uzindikili ndi luntha ndipo malamulo achisilamu anapanga nzeru kukhalachinthu chapamwamba,ndipo anazipanga nzeru kukhala njira yolamulidwila,ndipo nzeru anazimasula kuzinthu zongoganiza komanso zopembeza ma fano
Malamulo achisilamu amalemekeza maphuziro amene ali owona ndipo amalimbikitsa kufufuza maphuziro ndi mtima onse popanda zilako lako,komanso malamulo amaitanila kuyang'ana ndikuganizila iwe mwini komanso dziko mmene Allah analengela,ndipo zotsatila za kufufuza kwa kweni kweni siungapeze zosemphana ndi zimene zinabwela ndi mtumiki Muhammad mtendere ndi madalitso zipite kwa iye.
Mu malamulo achisilamu mulibe kupatula kwa mtundu wa anthu mwapadela dela ayi kusiya mtundu wina,komanso palibe ubwino la anthu ena kuposa ena,koma kuti pamalamulo ake amulungu anthu onse ndi ofanana,chifukwa anthu onse chiyambi chawo ndi chimozi,ndipo palibe kupatulika kwa ena ndi ena,kapena gulu lina ku gulu lina ayi,kupatula amene ali owopa mulungu,analongosola nthenga wa Allah mtendere ndi madalitso zipite kwa iye kuti munthu wina aliyense anabadwa pa chilengedwe chimozi palibe amene anabadwa ali olakwa kapena anatenga zolakwa za wina ayi.
Mu malamulo achisilamu Allah analamula kulapa;kumeneko ndiye kubwelela komwe munthu amabwelela kwa mbuye wake kusiya za sambi ndipo chisilamu chimachotsa sambi za kale zomwe unachita ndipo kulapa kumachotsa sambi zomwe zinali z m'mbuyo ndipo ndizosayenela kuti ulongosole pamaso pa munthu winanso mu chisilamu ubale wa munthu ndi mulungu wake umakhala oyandikana kwamberi umene siumafunikilanso kutiwina akhale m'khalapa pakati pakati pa iwe ndi Allah chisilamu chimaletsa munthu kuti atengedwe ngati mulungu kapena apangidwe othandizana ndi mulungu pa umulungu wake kapena pakupembezedwa pake.
Malamulo amene anabwela nawo mtumiki Muhammad mtendere ndi madalitso zipite kwa iye-ndi malamulo amene anachotsa malamulo amene analipo chifukwa malamulo amene anabwela nawo Muhammad mtendere ndi madalitso zipite kwa iye,amenewa ndiye malamulo omaliza mpaka tsiku la qiyamandipondi malamulo awonse, ndichifukwa anachotsa malamulo akale onsengati mmene malamulo enawo ankachotselana m'mbuyomu,ndipo mulungu salandila chipembezo china posakhala cha chisilamu chimene chanabwela ndi mtumiki Muhammad mtendere ndi madalitso zipite kwa iye,munthu amene afune chipembezo china posakhala chachisilam mdiye kuti sichizalandilidwa,ndipo amene akufuna kuti aziwe motambasula za chisilammalamulo ake ndiye kuti afune fune mma buku ameneali odalilika amene amafotokoza chisilm
Cholinga cha malamulo achisilamu monganso momwe chiliri cholinga cha mauthenga onse amulungu, ndiye kuchitchula chipembezo choona kwa munthu kuti akhale kapolo opembeza moziyeletsa kwa Allah mbuye wazolengedwa zonse,ndikumumasula mu ukapolo opembeza munthu mzake,kapena zinthu zaziko lapansi,kapenanso zokhumba za moyo zopanda umboni
Ndithu malamulo achisilamu ndi abwino nthawi zonse ndi malo ena alionse,ndipo samasephana ndi ubwino ulionse wa munthu,chifukwa anatsika kuchokela kwa Allah amene amaziwa zofunika za munthu, ndipo anthu akufunika malamulo owona kwa aliyense,amene samasutsana ena ndi ena abwino kwa munthu amane sataika ena ndi mzake, koma amakhala ochokelakwa kwa Allah osati kwa munthu amamuongolela munthu ku njila yolungama ndi lowongoka, ngati anthu akugwirtsa ntchito malamulo amenwa zinthu zawozimalongosoka zimaongoka ndipo amapulumutsidwa ku kupondelezana wina ndi nzake.
7-Maganizo a anthu osutsana ndi mtumiki poyikila pawo umboni kwa mtumikiyo.
Palibe kukaikila kuti mtumiki wina aliyense anali ndi anthu amene amasutsana nawo za kuitanila kwawo komanso amawaletsa anthu kuti asakhulupilire ndipo Mtumiki Muhammad mtendere ndi madalitso zipite kwa iye anali nawonso ambiri mu nthawi ya umoyo wake komanso angakhale atamwalira,koma Allah anathandiza atumiki onsewo,ndipo maumboni ambiri ayikidwa kuchokela kwa iwo akale komanso apompano, kuti iye ndi mtumiki ndipo anabwela ndizonga zomwe anabwela nazo atumiki ena akale mtndere upite kwa iwo, ndipo iwo amaziwa kuti iye ali pa chilungamo koma zambirizimawaletsa kuti akhulupilire monga ngati kukonda ma udindo,mantha kuopa anthu okhala nawo kapena kuluza chuma chomwe amachipeza chifukwa cha udindo wawo.
Kuyamikidwa konse ndi kwa Allah mbuye wazolengedwa zonse
Related books
All books
CHIKAKAMIZO CHOGWIRITSA NTCHITO SUNNA ZA MTUMIKI(SAW)NDIKUKANIRA KWA MUNTHU YEMWE ANGAZIKANE SUNNAZO.23 languagesCHIKAKAMIZO CHOGWIRITSA NTCHITO SUNNA ZA MTUMIKI(SAW)NDIKUKANIRA KWA MUNTHU YEMWE ANGAZIKANE SUNNAZO.
WOLEMBA BUKU: ABDUL AZIZ BIN ABDUL ALLAH BIN BAZ(ALLAH AWACHITIRE CHISONI). M'dzina la Mulungu ,Wachifundo Chambiri ,Wachisoni Chosatha. MAU OYAMBA Kuyamikidwa konse ndikwa Mulungu, mbuye wa zolengedwa zonse, ndipo mathero abwino pa chinthu chilichonse amakhala kwa anthu oopa Mulungu, mtendere ndi madalitso a Mulungu zikhale pa kapolo komanso mtumiki wake,mneneri wathu Muhammad; amene anatumizidwa kuti akhale ozichitira chisoni zolengedwa zonse,komanso mtendere ukhale kwa anthu aku banja kwake,ophunzira ake anthu amene anatenga uthenga ochokera mu buku la mbuye wawo pamodzi ndi…
CHISILAMU89 languagesCHISILAMU
M'dzina la Mulungu ,Wachifundo Chambiri ,Wachisoni Chosatha. Kodi unayamba wazifunsa wekha? Kodi ndi ndani amene adalenga mitambo ndi nthaka,komanso zolengedwa zazikulu zikupezeka ku mitambo ndi pansi pa nthaka? Kodi ndani adapanga ndondomeko yokuya ndi yokonzedwa mwa ukadaulo?
الإسلام دين رب العالمين
Ndani adandilenga? Nanga chifukwa chiyani?75 languagesNdani adandilenga? Nanga chifukwa chiyani?
Cholengedwa Chili chonse chimasonyeza kupezeka kwa Mlengi. Ndani adalenga kumwamba ndi dziko la pansi ndi zolengedwa zikuluzikulu zomwe zili mkati mwa ziwirizi zomwe sizimadziwika? Kodi ndi ndani adaika ndondomeko yokuya ndi yolongosoka bwino yakayendedwe ka zinthu kumwamba ndi dziko lapansi? Kodi ndani amene adalenga munthu ndikumupatsa makutu, maso, ndi nzeru? ndikumpatsa kuthekera kophunzira ndikudziwa zoona? Kodi mungafotokoze bwanji ndondomeko yodzama ndi yokuya ya momwe Mulungu adaikira ziwalo zapa thupi lako komanso ziwalo za zinthu za moyo? ndani adalenga zimenezo? Kodi dziko…